Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera...

20
Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi Luka’s Safety Adventure By/Wolemba Ruth B. Rimmer Illustrations by/Wojambula zithunzi Allyson Rimmer

Transcript of Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera...

Page 1: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi

Luka’s Safety Adventure

By/Wolemba Ruth B. RimmerIllustrations by/Wojambula zithunzi Allyson Rimmer

Page 2: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

- Ruth Rimmer, Ph.D.

Copyright ©2010 Books BeCause!Illustrations copyright ©2010 by Allyson Rimmer

All rights reserved.

This book may not be reproduced in whole or in part, by any means (with the exception of short quotes for the purpose of review),

without permission of the publisher.

For information, address: Books BeCAUSE! at www.booksbecause.com

Layout: Shawn Winchester Chichewa translators: Mr. Stancellous Kumwenda, Mr. Euthant Chirambo.

Printed in U.S.A.

Bukhu limeneli lalemberedwa kwa Benson Mutuvi-Kavu, chifukwa chakulimba mtima komanso kukhala ndi chikanga populumuka ndikukhalabe ndi moyo atapsa kodetsa nkhawa ali ndi zaka zitatu. Benson ndi mchimwene wake Jeofrey anali ndi zilonda zobwera kamba kakupsa ndi moto zoopseza moyo ndipo anachiritsidwa ku Arizona Burn Center. Mogwirizana ndi makolo awo, Benjamin ndi Dora iwo akubweretsa uthenga wakapewedwe kakupsa ndi moto kwa ana aku Malawi kudzanso makolo awo. Kuthokoza kwa padera kupite kwa banja la a Mutuvi-Kavu ndi a Cunningham Law Firm pothandiza kuti bukhuli litheke ndi kusindikizidwa.

DEDICATION / CHIKUMBUTSO

FORWARD / TSOGOLOThe Children’s Burn Foundation has been sponsoring teams of medical professionals traveling to Zambia to teach healthcare workers techniques to care for and treat severe burn injuries. These teams collaborate with medical staff at both St. Francis Hospital in Katete and University Teaching Hospital in Lusaka. A significant majority of the patients treated for burn injuries at these hospitals are unfortunately young children. Although teaching burn care is a major goal of our mission, preventing the number of burn injuries to children is essential. It is our hope that Luka’s story will help teach the children of Zambia how to stay safe around fire and other dangers to ultimately remain injury free.

The Children’s Burn Foundation is honored to support the production of this wonderful tool to help in our mission to prevent burn injuries to children through education. Many burn injuries to children are very preventable. The Children’s Burn Foundations’ Prevention and Education programs have successfully helped reduce the number of accidental burn injuries to children throughout the world. In addition to Education and Prevention programs, the Children’s Burn Foundation provides Full Recovery medical, psychological and psychosocial services to child burn survivors throughout the world. We are proud of our partnership with the American Burn Association, as we continue our worldwide mission.

The Children’s Burn Foundation defines its role as GIVING NEW HOPE.

Sincerely,

This book is dedicated to Benson Mutuvi-Kavu, for his courage and valor in surviving a serious burn injury when he was just three years old. Benson and his brother Jeofrey, originally from Africa, both experienced serious life threatening burns and were treated at the Arizona Burn Center. They have joined together with their parents, Benjamin and Dora, to bring the burn prevention message to Malawian children and their parents. A special thank you to the Mutuvi-Kavu family and the Cunningham Law Firm for making this book possible.

Carol Horvitz Executive Director Children’s Burn Foundation 5000 Van Nuys Boulevard, Suite 450 Los Angeles, California 91401

1-800-949-8898 Toll Free

Page 3: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

1

Precious ndi Manny amakhala ndi mai awo komanso agogo awo akazi mdziko la Zambia, ku Afrika. Tsiku lina, iwo adatumidwa ndi mai awo ku kukatola nkhuni zophikira. “Ine ndipita,” adatero Precious. “Nanenso,” ndipita adateronso Manny.

Precious and Manny live with their mother and grandmother in Zambia, Africa. One day, their mother asked them to get some wood for the cooking fire. “I’ll go,” said Precious. Manny said, “I’ll go too.”

Page 4: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

2

When they got to the forest, they began to pick up wood and put it in their basket. Suddenly a big rabbit with a beautiful hat hopped up. “Hello children,” said the rabbit. “Welcome to my home. Are you collecting wood for your mother?”

Atafika mnkhalango adayamba kutola nkhuni zija ndi ku maziponya mudengu. Mwadzidzidzi, Kalulu wamkulu adatulukira atavala kachipewa kokongola. Kalulu uja adawalonjera ana aja, ndakulandirani kwathu kuno, iye adatero. Mukutola nkhuni za mai anu?

Page 5: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

3

“Yes.” said Precious. She and Manny looked at the rabbit in surprise! “Well then, that must mean someone is going to make a cooking fire,” replied the rabbit.

“Inde,” adayankha Precious pamenepo ndikuti akumuyang’ana kalulu uja modabwa! “Chabwino izi zikutanthauza kuti munthu wina akukayatsa moto? Kalulu uja adafunsa.

Page 6: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

4

“Yes,” said Manny. “Did you just talk? Rabbits can’t talk!”

“Inde,”Manny adayankha. Munayankhula? Adamfunsa kalulu uja, akalulu sangayankhule.

Page 7: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

5

“I can, because I’m a magical rabbit. My name is Luka. I’d like to come back to your village and teach you some safety rules.”

Ine ndikhoza chifukwa ndine kalulu wamizimu. Dzina langa ndine Luka ndikufuna kupita nanu kumudzi kwanu kuti ndikakuphunzitseni njira zopewera ngozi?

Page 8: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

6

“Great,” said Manny. The children finished collecting wood and started towards the village. “When we see cars or trucks on the road we need to stay off the road. Always walk towards traffic so you can see the vehicles.”

Manny adati, “zofunika.” Atamaliza kutola nkhuni zija ana aja adayamba kubwerera kumudzi. Tikaona magalimoto ang’onoang’ono kapenanso akuluakulu tisamayandikire kufupi ndi mnseu. Nthawi zonse tsatirani mbali imene kukuyenda magalimoto kuti muziaona.

Page 9: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

7

They came to the children’s home. Precious walked towards the fire. “Wait,” said Luka. “Precious you’re too young to put wood on the fire safely. All small children should stay far away from fire. Let’s build a magic circle out of rocks and put it around the fire. The children should always stay outside the circle.”

Adafika kumudzi kuja ndipo Precious anayenda molunjika moto. “Dikira,”adatero Luka. Precious ndiwe mwana kwambiri kuti usonkhezere moto bwinobwino. Ana onse azikhala kutali ndi moto. Tiyeni timange mzere ndi miyala mozungulira moto. Kenako nthawi zonse ana onse azikhala kunja kwa mzerewo.

Page 10: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

8

“Mothers, fathers and grandmothers and grandfathers should light the fire; not children. Fire and flames can burn our skin. Fire can be very dangerous. We need to respect it and stay away.”

Azimai, Azibambo komanso azigogo akazi ndinso amuna aziyatsa moto osati ana. Moto komanso malawi ake akhoza kuotcha khungu lathu. Moto ukhoza kukhala oopsa zedi. Moto ndiofunika kuti tiziulemekeza ndipo tizikhala kutali nawo.

Page 11: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

9

“Hot water and food can also burn us like fire. Staying away from the cooking pot when mother is cooking is a good idea too!”

Madzi otentha komanso chakudya chotentha zikhoza kutiotchanso ngati moto. Kukhala kutali ndi poto ophikira amai akamaphika ndi ganizo labwinonso.

Page 12: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

10

“If you do get too close and your clothes catch on fire you need to STOP, DROP, COVER, and ROLL and ROLL and ROLL until the fire is out.”

Mukakhala pafupi kwambiri ndi moto ndipo malaya anu agwira moto mukuyenera KUIMA, KUGONA PANSI, KUZIFUNDISA, ndiponso KUZIGUBUDUZA mpakana moto utazima.

Page 13: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

11

“Then cool the burn with water and go to hospital as soon as possible.”

Kenako ziziritsani mabala a motowo ndi madzi ozizira kenako thamangirani kuchipatala mnsangamnsanga.

Page 14: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

12

“Let’s go inside. See the paraffin lamp and candle. They give us light but can also cause burns and fires. Lamps and candles must be on a flat surface so they don’t fall over and start a fire. They should always be up high and extinguished before we leave the room or go to sleep. And remember never leave the paraffin oil where small children can get it. It is very poisonous.”

“Tiyeni tilowe mnyumba. Mukuiona nyale ya parafini komanso kandulo, izi timaunikira koma zikhozanso kutiotcha ndinso kuyatsa moto. Nyale ndi makandulo zizikhala pamalo okhazikika bwino kuti zisagwe ndikuyatsa moto. Nthawi zonse zizikhala pamalo okwera komanso tikumbukirenso kuzimitsa tisanachoke mchipinda kapena tisanagone. Tikumbukirenso kuti tisasiye mafuta a parafini pamalo ofikira ana chifukwa mafutawa ngoopsa ndinso akhoza kupha.”

Page 15: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

13

They walked outside. “One more thing,” Luka said as he pointed to the lake. “We must always keep little children away from the lake or river; especially during the rainy season. We don’t want them to drown.” The children waved goodbye as Luka hopped away.

Adatuluka panja. “ chinthu chomaliza,” Adayankhula Luka akulodza nyanja. Nthawi zonse tiletse ana kukhala pafupi ndi Nyanja kapena mitsinje; makamaka nthawi ya dzinja. Sitikufuna kuti adzamire ayi. Ana aja anabaibitsa Luka uja iye akujowera kwao.

Page 16: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

14

Precious and Manny learned a lot from Luka. Now, every morning, Precious and Manny remember to stay away from the fire and stay outside of the magic circle. They also remind their friends not to sit or sleep close to the fire. They want to keep them safe. Make sure you build a magic circle around your fire too!

Precious ndi Manny adaphunzira zambiri kuchoka kwa Luka. Pano, m’mamawa uli onse Precious ndi Manny amakumbukira kukhala kutali ndi moto kunja kwa mzere ozungulira moto uja. Amakumbutsanso anzao kuti asamakhale kapena kugona pafupi ndi moto. Akufuna kuti azikhala opewa nthawi zonse. Yesetsani kwambiri kuti nanunso mmange mzere m’mbali mwamoto!

Page 17: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

15

Tsamba la kholo – Samalani ana.1. Moto ndi wabwino kwa anthu, koma ukhoza kukhala woopsa ukakhudza malaya athu kapena thupi.

Nsalu ya chitenje ndi yopyapyala ndipo yimagwira msanga moto ndiye onetsetsani kuti zovala za ana anu zili patali ndi moto. Ikani ana kutali ndi moto.

2. Thawi zonse yang’anilani ana ophunzira kuyenda ndi makanda akakhala pafupi ndi moto. Osalora ana kusewera pafupi ndi moto kapena poto amene ali pa moto. Jambulani nzele kuzungulira malo a moto ndipo ana asadumphe nzelewo. Iyi ndi njira yodalilika kwambiri yopewera zilonda za moto.

3. Chenjezo! Madzi a moto, chakudya cha moto ndi phala la moto ndi zinthu zoopsa kwambiri. Kukhudza zinthu tatchulazi kwa mphindi zochepa, chilonda cha moto chikhonza kupangika. Zilondazi zimakhala za ululu kwambiri, ndipo zimasiya zipsyela zosatha pa thupi. Sungani mapoto ophikira kutali ndi ana.

4. Amayi ndi ana okulirapo akhale tchelu pophika ndi pamene abeleka ana mu chitenje. Ana atha kugwera pa moto kuchokera mu chitenje. Choncho osaphika pamene mwanyamula makanda m’manja.

5. Ikani nyali yoyaka pamwamba posafikira ana makamaka oyamba kumene kuyenda. Aphunzitseni ana kuti asagwire nyali. Zimitsani nyali mukamatuluka mu chipinda.

6. 6. Nthawi zonse sungani mafuta anyali mu chiwiya cha bwino. Osasunga mafutawa mu chiwiya ngati botolo la fanta kapena katoni ya mkaka popeza zikhoza kupha munthu.

7. Ngati mwana wamwa parafini mwangozi, osamudyetsa kapena kum’mwetsa chilichonse.Osamukakamiza munthuyo kuti asanze chifukwa izi zitha kupangitsa parafini kuti alowe mu mapapo ndikuyambitsa vuto lalikulu. Pitani naye ku chipatala chimene mulinacho pafupi mofulumira kwambri.

8. Osayatsa moto mnyumba ndi cholinga chowotha kapena kuphikira. Malawi a moto ndiwopsa ndipo amapeleka vuto lalikulu mu njira yodutsa mpweya wopuma.

9. Yang’anirani ana pamalo ozungulira nyanja kapena mtsinje, makamaka nthawi ya mvula. Osasiya zidebe za madzi pafupi ndi ana. Vindikirani kapena muchotse madziwo popeza ana atha kugweramo ndikumira.

10. Munthu wamkulu ayang’anire mwana pamene akusamba mu chidebe. Mwana osayang’anilidwa atha kumira ndi kufera m’madzimo.

11. Ngati muli ndi munthu wongwa khunyu, musungeni kutali ndi moto nthawi zonse. Osawalora kuphika. Matendawa akayamba akuphika, atha kupsya kumaso ndi njira yodutsa mpweya wopuma. Pa chifukwa ichi aliyense akhale ndi udindo woyang’anira athu ngati amenewa. Onetsetsani kuti akumwa mankhwala tsiku lililonse kuti apewe khunyu.

12. Ngati munthu zovala zake zagwira moto, asayende, mukhadzikeni pansi ndipo agubududzike pansi. Zimitsani malawi a moto ndi zisanza zamabulangete ndiponso mchenga kapena zinyalala. Sungani chidebe cha zinyalala kapena mchenga pafupi ndi moto kuti muzimitsire moto ukavuta.

13. Zizilitsani zilonda za moto ndi madzi ozizira nthawi yomweyo. Ngati zayamba kupanga matuza kapena kuyamba kuda, kawonaneni ndi dokotala wamkulu ku chipatala. Phimbani mabala a moto ndi kansalu koyela bwino mpakana akaondedwe ndi dokotola. Mabala ang’onoang’ono atha kupakidwa mankhwala a kilimu, koma mabala akulu kapena akuya amafunika opareshoni kuchipatala.

14. Mutha kupeza chithandizo pachitala chaching’ono chomwe muli nacho pafupi mwana wanu akapsya. Chilonda chikakhala chachikuku, akhoza kumutumiza ku chipatala chachikulu cha Nkhoma kuti akalandire chithandizo choyenera.

Page 18: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

16

Zokhudzana ndi Nthenda yakhunyuMatenda a kugwa amabwera chifukwa chakusokonekera kwa kagwiridwe ka ntchito ka ubongo nthawi zina amatchedwa kukomoka.Iyi simisala ayi.Khunyu ndi matenda akanthawi kochepa basi, matendawa amasinthitsa mmene ubongo umagwirira ntchito.Matenda amenewa angathe kupangitsa munthu kukomoka, komanso kumgwetsa pansi mosayembekezera, kulimbitsa thupi lake komanso kumgwedeza kwambiri.Pamene khunyu ikuchitika mwana sakhala ndi ulamulilo pazochita zao. Samathanso kukumbukira china chilichonse akatsitsimuka.Zifukwa zomwe zimapangitsa kukomokaKhunyu, ndi chifukwa chimodzi chomwe chitha kupangitsa munthu kuyamba kukomoka.Kukomoka kukhoza kuyambanso chifukwa cha:• Kutentha thupi kwambiri• Kuvulazidwa kwa mutu kapena ubongo• Kapenanso matenda omwe amakafika m’madzi

amu ubongo(nthenda yotupitsa ubongo, matenda oumitsa khosi, ndinso malungo ogwira ubongo)

Machiritsidwe a khunyuDotolo akakhutitsidwa kuti mwana ali ndi khunyu, amasankha mankhwala othandiza kusiitsa kukomoka.Kuti mankhwalawa agwire bwino ntchito yake ndikofunika kuonetsetsa kuti akumwedwa tsiku lililonse komanso nthawi imodzimodzi.Mwana akapitiliza kukomoka pamene akumwa mankhwala, mulingo wamankhwalawo umafunika kusinthidwa ndi dotolo. Mankhwalawa asaimitsidwe.Nthawi zambiri kukomoka kumasiya kokha mu mphindi imodzi kapena ziwiri.Ngati mwana apitilira kukomoka ndipofunika kukumana ndi munthu wazaumoyo kuchipatala chaching’ono kapena chachikulu mwachangu.Zoona za khunyuAna amene amakomoka atha kukhala ndimoyo wamphamvu, komanso wabwino bwino potsatira.

Mankhwala komanso chisamaliro cholondola.Atha kusewera ndi ana anzao komanso kupita ku sukulu.Khunyu siyopatsirana. Khunyu simabwera chifukwa cha khalidwe loipa komanso mizimu yoipa. Komanso siiyamba chifukwa chatizilombo tam’mimba.Khunyu siimayambanso chifukwa cha kulakwa kwa mwana.Chifukwa chani ana akhunyu azichenjera akakhala pafupi ndi motoNgati mwana ali ndi mbiri ya kukomoka amakhala pachiopsezo chogwera pamalo otentha kapena pamoto kumene pamene iye akomoka. Izi ndi zoopsa kwambiri ndipo ngati kuli kotheka anthu owonerera ayesetse kumchotsa pamotopo bwininobwino.Ngati ana athandizira kuphika, ndipofunika kuti akhale ndi owayang’anira pafupi kuti asazipweteke komanso kugwera mmalawi amoto, ndipofunikanso kuonetsetsa kuti zovala zao zisagwire moto.Kakhalidwe kabwinoAna amene amakomoka amakhala okhudzidwa chifukwa chakusokonokera kwa moyo wao, komanso amakhudzidwa ndizakukomoka kwao pamaso pa mabanja awo koanso anzao.Anawa sayenera kuchita manyazi chifukwa cha umoyo waowu.Anzake komanso akubanja kwa mwana odwala matenda akhunyu amthandize kuti akhutitsidwe ndi moyo wao komanso zomwe angathe kuchita mmoyo wao.Mwana wina aliyense amene amakomoka kapena amene ali ndi khunyu asazunzidwe.Anzake kapena achibale a mwana amene amakomoka aphunzitsidwe zaumoyo wake komanso kuti zikhoza kuimitsidwa kapena kutetezedwa ndi mankhwala.Abale ndi alongo akhale ndi mwai ofunsa mafunso okhuzana ndi khunyu komanso akambirane pa zizindikiro zina za kukomoka zomwe zingaaopse.

Page 19: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

ALLYSON RIMMERUku ndi kusindikiza koyamba kwa zolemba za Allyson. Iyeyu ndi mtsikana wa zaka khumi ndi mphambu zisanu ndi chimodzi ndipo ndiwojijirika kwambiri ndi pologalamu ya za mankhwala okhudzana ndi zamasewero, pa sukulu ya pamwamba ya Mountain View ku Mesa Arizona. Kuonjezera pamenepo iyeyu ndiwojijirikanso ndi ntchito yozipereka pa Maricopa Medical Center, malo amene kuli Arizona Burn Center. Allyson adayamba maphunziro ake aluso mu gawo laling’ono la sukulu zapamwamba, ndipo akufuna kuthokoza aphunzitsi ake amene anagwira ntchito yabwino kwambiri pomuphunzitsa.

This is Allyson’s first publication. She is sixteen and actively involved in the sports medicine program at Mountain View High School in Mesa, Arizona. She is also an active volunteer at Maricopa Medical Center, home of the Arizona Burn Center. Allyson began her art lessons in junior high, and would like to thank her teacher Shawn Winchester for his excellent instruction.

ABOUT THE ILLUSTRATOR

RUTH BRUBAKER RIMMERDr. Ruth Rimmer, yemwe ndiodziwa za saikoloje(odziwa za mmene mzimu wamunthu umaganizira ndikugwirira ntchito) pa Arizona Burn Center, wakhala akugwira ntchito ndi ana opwetekedwa kamba kakupsa ndi moto kwa zaka zoposera khumi ndi mphambu zisanu ndi chimodzi. Iye ndi wotsogola pa akatswiri pazinthu zokhuza kaganiziridwe komanso kakhalidwe kokhudzana ndi za kupsa ndi moto komanso kapewedwe kake ndipo wakhala akuyankhula za zimenezi paliponse pa dziko lonse la pansi. Ili ndi bukhu lake la chisanu ndi mphambu ziwiri (seveni). Ruth ndi osangalala kwambiri popeza mwai wothandiza kufikitsa uthenga wa kapewedwe kakupsa ndi moto mdziko la Malawi ndiponso ndionyadira chifukwa chakukhala mbali imodzi ya pologalamu ya Africa Burn Relief.

Dr. Ruth Rimmer, a psychologist at the Arizona Burn Center, has worked with burn-injured children for over sixteen years. She is a leading expert on the psychosocial aspects of burn injury and burn prevetion and has spoken about these isues all over the world. This is her seventh book. Ruth is so happy to have the opportunity to help bring the prevention message to Malawia and is proud of her affiliation with Africa Burn Relief!

ABOUT THE AUTHOR

Page 20: Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozidownload.lww.com/wolterskluwer_vitalstream_com/... · Ulendo wa Luka wophunzira njira zabwino zopewera ngozi. Luka’s Safety

A special thank you to our sponsors:

www.booksbecause.com

www.childburn.orgwww.ameriburn.org