Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA...

208
Auntie Stella Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre, Zimbabwe

Transcript of Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA...

Page 1: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

AuntieStellaAuntieStella

Bwalo la achinyamata

DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA

Training and ResearchSupport Centre, Zimbabwe

Page 2: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Training and Research Support Centre (TARSC) Zimbabwe is a non-profit making companyregistered in Zimbabwe in 1994.

TARSC provides training, research and support services to state and civil societyorganisations.

TARSC is a learning and knowledge organisation, with a particular focus on skills buildingand methods to support community-based work, and with a commitment to long termcapacity building in the public sector and in civil society. TARSC researched, wrote andproduced the English version of Auntie Stella – Teenagers talk about sex, life andrelationships. The kit is now available in English, Shona, Ndebele, Portuguese, Swahili andChichewa.

Please visit our website at www.tarsc.org or contact us at [email protected] for further information on TARSC andon our other participatory training and research materials and programmes.

Auntie Stella: Bwalo la achinyamata is published byTraining and Research Support Centre (TARSC)PO Box CY 2720 Causeway Harare ZimbabweTel: 263-4-795124 Fax: 263-4-737220Email: [email protected] [email protected], www.tarsc.org, www.auntiestella.org

© Training and Research Support Centre/Barbara Kaim, February 2009

TARSC and B Kaim have full joint copyright over this material. While we encourage wide use of the material fornon-profit purposes, under the copyright we require that those seeking to use or adapt the materials first obtainpermission from TARSC and comply with copyright requirements to acknowledge TARSC and the authors in aform agreed with us and to send us a copy of the adapted version for our feedback before publication.

ISBN: 978-0-7974-3730-2

Printed by: Easi-Print, 199 Lower Main Road, Observatory, Cape Town, Tel: 021 448 4181

Youth Net and Counselling (YONECO) is a non-profit making non-governmentalorganisation that was formed in September 1997.It was established to address the socialinjustice and reproductive health issues affecting youth, women and children. YONECO isregistered with the National Youth Council of Malawi under the National Youth Council(1996) Act, under the Trustees Incorporation Act (1962) and with the NGO Board.

YONECO is committed to: Empowering the youth, women and children; Combating the spread of HIV infection;Mitigating the impact of AIDS; and, Promoting human rights and democracy for socio-economic development.

YONECO went into partnership with TARSC of Zimbabwe and Solon in implementing a project called:‘Preserving the Future Generation: Addressing Adolescent Sexual and Reproductive Health Needs in Malawi’through the pack, Auntie Stella –Teenagers talk about sex, life and relationships. The project seeks to empoweradolescents to actively take part in protecting themselves against unsafe sex, early pregnancy, STIs and HIV andAIDS by making proper informed decisions that affect their lives. The project adapted and translated AuntieStella into Chichewa for use in Malawi.

YONECO PO Box 471 Zomba Malawi

Tel: (265) 01 525 674 Email: [email protected] Website: www.yoneco.org

SOLON

We are grateful to the SIDA Regional HIV/AIDS Team in Africaand Solon for their generous financial support in the productionof this publication.

Page 3: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZAMKATIMU

Thumba la Auntie Stella ndi chiyani? . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .6

Mndandanda wa ma khadi a Auntie Stella . . . . . . . . . . . . . . . .8

Udindo wa munthu otsogolera maphunziro . . . . . . . . . . . . . . . . . . . 9

Zina mwazinthu zimene achinyamata ayenera kudziwa . . . . .10

Kukambirana m’magulu . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .11

Mmene mungagwiritsire ntchito thumba la Auntie Stella . . . . . . . . .12

Chitsanzo cha kalembedwe ka kaundula wa makhadi amenemagulu atsiriza kukambirana . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .14

Ndime yokambirana zinthu zoyambirira . . . . . . . . . . . . . . . . .15

Gawo la awiri lolemba kalata, ndi lokhala m’magulu akazikapena amuna okha okha . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .16

Ndime yokambirana mitu ikuluikulu . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .17

Kuwonanso ndi kuwunika zimene mwakhalamukukammbirana . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .21

Mmene mungakonzere masewera osiyanasiyana . . . . . . . . . . . . . . . .23

Mavuto amene otsogolera zokambirana angakumane nawo . . . . . .27

Maphunziro oyenera anthu otsogolera zokambirana ndichithandizo chimene angachifune . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .29

Mabuku ena amene mungagwiritse ntchito . . . . . . . . . . . . . . . . . . .32

Page 4: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

4

Otsogolera zokambirana!

Werengani bukhu lino musanayambe kugwiritsa ntchito thumba laAuntie Stella. Bukhuli limakuwuzani zonse zimene mungafunekudziwa za thumbali ndipo lidzakuthandizani kuti mudziwe mmenemungagwiritsire ntchito makhadi a mthumbali komanso mmenemungapangire ndondomeko ya ntchito yanu pa maphunziro amenewa.

Zigawo zofunikira kwambiri kwa inu ndi:

• Udindo wa mtsogoleri (tsamba 9)

• Mmene mungagwiritsire ntchito thumba la Auntie Stella(tsamba 12)

Zigawo ziwiri mu bukhu lino zalembedwa kuti zithandize mabungwe:

• Kuphunzitsa ndi kuthandiza anthu otsogolera maphunziroamenewa (tsamba 28)

• Kugwiritsa ntchito thumba la Auntie Stella kuti ligwirizanendi malo kapena dera kumene achinyamata ali komansopotengera chikhalidwe chathu (tsamba 32)

Tili ndi chikhulupiriro kuti bukhu ili likuthandizani inu ndiachinyamata anu kukhala osangala ndi olimbikitsidwa kugwira ntchitolimodzi pokonza tsogolo la bwino komanso Malawi wa bwino limeneachinyamata amatha kupanga zisankho zoyenera komanso kutengambali pomanga mfundo zimene zimakhudza miyoyo yawo.

Page 5: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Dongosolola otsogolerazokambirana

Page 6: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

THUMBA LA AUNTIE STELLA NDI CHIYANI?

6

Thumba la Aunti Stella ndi ndondomeko ya maphunziro imeneachinyamata amakhala pa modzi ndi kumakambirana nkhani zokhuzakugonana, moyo wawo komanso zokhuza ubwenzi osiyanasiyasiyanaumene amakhala nawo. Maphunziro amenewa ndi oyeneraachinyamata a dzaka zapakati pa 12 ndi 19 za kubadwa.Maphunzirowa anayamba kukonzedwa ku Zimbabwe koma akhozakugwiritsidwa ntchito mmaiko onse a muno mu Africa komansomaiko ena a padziko lino lapansi

Thumbali limagwiritsa ntchito mafunso ochokera kwa achinyamatandi mayankho amene Auntie Stella amapereka. Mafunso amenewaamakhala ngati amene achinyamata amalembera ku manyuzi pepalaosiyanasina kuti awathandize pa zinthu zina zokhudza moyo wawo.Mafunso a m’thumba limeneri amakhudza mavuto osiyanasiyanaamene achinyamata paokha (monga nkhani zogonana) amakumananawo komanso mavuto amene amawachitikira chifukwa cha anthu enakapena chifukwa cha chikhalidwe ndi zikhulupiro zathu. (Onanimndandanda onse wa mavuto amenewa pa tsamba 8).

Achinyamata akakumana kumakambirana nkhani za mthumbali,amakhala mmagulu. Nthawi zina magulu amenewa amakhalaophatikizana anyamata ndi atsikana ndipo nthawi zinanso amakhalamagulu anyamata okhaokha atsikananso okhaokha. Pa gulu pawopoamawerenga khadi limene liri ndi kalata. Akatero, amakambiranamafunso amene alembedwa kuseri kwa kalatayo. Akamaliza,amatenga ndi kuwerenga khadi limene liri ndi yankho limene AuntieStella apereka. Pomaliza penipeni amachita masewero osiyanasiyanamonga role plays, kuchita mtsutso, kujambula zithunzi, kulemba ndikuimba nyimbo ndi zina zotero malinga ndi mmene zaperekedwera pakhadi limeneri. Nthawi zina achinyamatawa akhoza kuchita izi onsepamodzi.

Cholinga cha Auntie Stella

• Kupereka mwai kwa achinyamata okhala omasukandikumakambirana posaopa chirichonse nkhani zimenezimakhudza moyo wawo monga zogonana, za matupi awondi ubwenzi osiyanasiyana umene amakhala nawo;

• Kuwapatsa achinyamata uthenga ndi mfundo zenizenizokhudza iwo eni komanso zokhudza matupi a wo;

• Kuwathandiza kukhala odzidalira popanga chisankho kapenazisankho zoyenera pa moyo wawo komanso kuti adzithakuthandizana popanga zisankho zoyenerazi;

• Kuwapatsa luso lowathandiza a chinyamata kukonzandondomeko yawo pawokha, kulankhula za ku khosi, kupitaokha kukafuna chithandizo chimene akufuna, kucheza ndikukambirana ndi makolo, abwenzi awo komanso kumapitakumakacheza ndi anthu kapena mabungwe ameneangawathandize pa moyo wawo;

Page 7: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

7

Auntie Stella pa website

Auntie Stella akupezekanso pa www.tarsc.org kapena pawww.auntiestella.org ndi pa ma CD-ROM. Amene akufunakuphunzira paokha ,awiri awiri kapena mmagulu a ng’onoang’ono akhoza kugwiritsa ntchito web imeneyi. Anthu amenewaamagwiritsa ntchito makina a computer akamaphunzira.

• Kulimbikitsa achinyamata kuti adzigwiritsa ntchitozithandizo zosiyanasiyana zimene zimapezeka m’dela lawokomanso kuti adzikhala pa tsogolo powonesetsa kutimabungwe amenewa akupereka chithandizo chokwanira ndichoyenera kwa achinyamata.

Nthawi zambiri achinyamata amadziwa kwambiri zimene akufuna pamoyo wawo, amangosoweka kuthandizidwa kuti akwaniritse zimeneakufuna. Chifukwa cha ichi,Auntie Stella samawauza achinyamatakuti pangani chakuti ayi. Mmalo mwake, amawathandiza kuti adzithakuganiza mozama pawokha za chisankho chimene angachitezokhudza iwo eni kapena a pa banja pawo ndi abwenzi awo.Amalimbikitsidwa kuti apeze njira zimene zingawathandize kutiadzikambirana ndi kugwiririra ntchito limodzi, kutengapo mbalipopanga mfundo zimene zimakhudza moyo wawo komanso ndikulankhula za kukhosi. Pakuchita izi, amalimbikitsidwa kukonzatsogolo lawo ndi udindo umene ali nawo pokonza tsogolo limeneri.

Thumba la Auntie Stella ndi njira zophunzitsira maphunziro amthumbali, linayamba ndi kafukufuku amene achinyamata a kuZimbabwe anachita pa zimene achinyamata amafuna kapena zimeneamasowa ndi mavuto amene amakumana nawo. Pologalamu yamaphunziro a mthumbali isanayambe, makhadi amthumbali anayambakaye awayesezera mmaiko a Malawi, South Africa, Tanzania ndiZambia kuti awone ngati amagwirizanadi ndi mavuto ameneachinyamata amakumana nawo mmaiko amenewa.

Thumbali liri ndi makhadi 40 ( amafunso 20 ndi amayankho 20),bukhu lino komanso makhadi ena awiri (lina la mndandanda wamaphunziro amene ali mthumbali komanso lina limene likufotokozeramau ovuta). Thumbali linatsindikizidwa koyamba mchaka cha 1997ndipo analiwunikanso ndi kulisindikiza kachiwiri mzaka za2004/2005. Panopa makhadi amapezeka mzilankhulo zosiyanasiyanamonga Chindebele, Chishona, Chipwitikizi ndipo panopa thumbalilathanthauziridwanso Mchichewa.

Page 8: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

MNDANDANDA WA MA KHADI A AUNTIE STELLA

8

1 Kodi ndingathe kugonana naye?

2 Kodi chokodzera changa ndichaching’ono kwambiri?

3 Kodi ndigonane naye mwamuna wamchemwali wanga?

4 Ndikusamalira munthu odwalamatenda a Edzi

5 Ndine mutu wa banja lathu tsopano

6 Ndikufuna ndidzichita zogonana ngatimmene amachitira anzanga

7 Ndinatengapo matenda opatsiranapogonana – Kodi sindidzabereka?

8 Aphunzitsi anga akufuna kutiadzigonana nane

9 Mnzanga ndi wamakhalidwe ogonanaamuna okhaokha

10 Chibwenzi changa chiri ndi mimba

11 Ndimakhala ndi chilakolako chofunakugonana ndi atsikana pafupipafupi

12 Kodi sindiyenera kugonana nayengakhale ndi mamuthandiza mu njirazosiyanasiyana?

13 Ndiri ndi tiziphuphu (totupa) pachokodzera changa

14 Mwina ndiri ndi kachilombo ka HIV

15 Ndikuwopa khansa ya m’chiberekero

16 Ndinagwiriridwapo

17 Kodi ndiyambe uhule kuti ndipezendalama?

18 Ndimatulutsa umuna ndikagona usiku

19 Kodi ma ARV ndi chiyani?

20 Akufuna kuti ndizigonana nawo.

21 Papita nthawi yaitali ndisanapangepiriyodi

22 Kodi ndimuuze kuti ndiri ndikachilombo ka HIV?

23 Kodi chamba chingandichotsemanyazi?

24 Makolo anga ndi ovuta

25 Kodi ndimuuze kuti ndiri ndi matendaopatsirana pogonana?

26 Ndiri ndi kachilombo ka HIV. Kodindimwalira?

27 Kodi ndiri ndi mimba?

28 Bwenzi langa akukwatiwa

29 Aphunzitsi anapereka mimba kwamnzanga

30 Mwamuna wanga ndiwachimasomaso

31 Ndimakhala ndi nkhawa popandachifukwa

32 Sindikumfuna mwana ameneyu

33 Chipembedzo changa chimaletsamakondomu

34 Ndimafuna kukhala mchikondi ndiakazi okha okha – kodi alipoangandikonde

35 Ndimamva ululu kwambiri ndikakhalakuti ndiri kumwezi (ndikusamba)

36 Achidya makanda anga amandizunza

37 Chikondi chimandilepheretsakuwerenga

38 Mai anga ali ndi kachilombo ka HIVndipo samabisa

39 Ndingathane nazo bwanji ziphuphuzanga?

40 Ndine oyembekezera komnso ndirindi kachilombo ka HIV

41 Mchimwene wanga anachitamdulidwe

42 Ndiri ndi zibwenzi zambiri zogonananazo

Page 9: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

UDINDO WA MUNTHU OTSOGOLERA MAPHUNZIRO

9

Anthu osiyanasiyana akhoza kutsogolera anthu pa zochitikazosiyanasiyana monga: achinyamata ophunzitsa anzawo, aphunzitsi,anthu ogwira ntchito za umoyo, anthu opereka uphungu kapena kutimakhansala, kapena achinyamata amene amagwira ntchitozosiyanasiyana za boma. Monga mtsogoleri, ndi bwino kuti:

• Muzidziwa mozama za umoyo wa ubereki wa achinyamata,kumene mungapezeko zida zophunzitsira komanso zimeneachinyamata ayenera kudziwa.

• Muzikhala munthu omasuka kucheza ndi achinyamatakomanso kumakamba nawo nkhani zokhudza kugonana ndiza zibwenzi.

• Muzipereka mpata kwa munthu wina aliyense otenga nawombali pazokambilana zanu ndiponso mukhoza kuthandizamagulu kuti athe kukambirana pofuna kupeza maganizoamene angathe kuthetsa mavuto osiyanasiyana.

• Mukhoza kuwasiya achinyamata mmagulu kutiazikambirana; ndiponso simuyenera nthawi zonsekumawauza chochita kapena kudziwa china chilichonsechimene akunena.

• Achinyamata amakupatsani ulemu chifukwamumawamvetsetsa ndiponso mumawathandiza maganizopankhani yolimbikitsa ubale wawo ndi anthu a mdera lawo.

Choncho udindo wanu mu zokambilana za Auntie Stella ndiofunikakwambiri. Ntchito yanu yofunika kwambiri ndiyoonetsetsa kutiachinyamata akukumana ndikumakambirana momasuka nkhanizokhudza moyo wawo, akutha kugawana nzeru, akufunsana mafunsondiponso akuphunzira mmene zisankho zosiyanasiyana zokhudzamoyo wawo angamapangire. Cholinga chanu ndikuonetsetsa kutiachinyamatawa akumakambirana, kupereka maganizo awo, kutsutsazimene sakugwirizana nazo, akusangalala ndi zimene zikuchitika.Akuchita mtsutso, kuimba nyimbo ndikuchita maseweroosiyanasiyana. Komanso mayankho a mavuto amene akukambiranaasamachokere kwa inu koma achinyamata okhaokha pokambirana.

Atsogoleri ena a magulu a Auntie Stella ndiodziwa kale ntchito yawondipo safunikiranso kuphunzitsidwa. Ngakhale izi zili chonchobukhulu ndilofunikilabe kwa anthu amenewa. Koma ngati mukuonakuti ndikoyenerabe kuphunzitsidwa, kambilanani ndi akuluakuluakumabungwe anu ndipo onani zina mwa zinthu zimenezingakuthandizeni pa tsamba 28-29.

Page 10: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

10

• Konzekerani mokwanira zimene achinyamata ayenera kukambilana akakumanammagulu awo. Simuyenera kudandaula mukaona kuti ndikoyenera kusintha zomwemunakonza kuti achinyamata akakambilane malinga ndi zofuna zachinyamatawopanthawiyo. Muyenera kukhala munthu omvetsetsa ndikuchita zimeneachinyamatawo akufuna kuchita.

• Onetsetsani kuti chikonzero cha zokambiranazi chikupereka mwayi kwa winaaliyense. Munthu aliyense akhoza kupereka maganizo ake nthawi ina iliyonseimene iye akufuna. Musadandaule nazo ngati azikangana kapena kuchita phokoso.

• Onetsetsani kuti mukupereka ndondomeko kapena malangizo omveka bwino pazinthu zina zilizonse zimene mukufuna kuti achinyamata achite ndiponsoonetsetsani kuti aliyense wamvetsa chomwe mukufuna kuti achite.

• Maganizo awina aliyense ndiofunika. Onetsetsani kuti zokambiranazachinyamatawa sizikuyendera maganizo anu okha.

• Chilichonse chimene mwamva pazokambiranazi ndi chachinsisi. Chonde musauzeanthu ena pankhani iliyonse imene mwamva muzokambiranazi chifukwa mukateroachinyamatawa sadzakukhulupiliraninso.

• Muwakumbutse achinyamata onse kuti ayenera kulemekeza maganizo a anzawondipo nkhani ina iliyonse imene yakambidwa pagulu ndi yachinsisi. Atsogoleriamene asankhidwa kuti adziimilira gululi akhoza kuthandiza pakufotokozeraanzawo zakufunika kosungilana chinsisi.

• Gulu lisankhe lokha chiyankhulo chimene akumafuna kugwiritsa ntchitopokambirana.

• Onetsetsani kuti mwauza akuluakulu kaya mabungwe mdela lanulo za ntchitoimene mukugwira ndi achinyamatawa ndipo muwapemphe kuti azikuthandizanim’njira zosiyanasiyana. Kuonjezera apo, werengani makadi onse kuti mudziwezinthu zofunika ndi kuzichita.

• Konzekelani mokwanira popeza zida zina zophunzitsila khadi ina iliyonse. Zidazimutha kuzipeza ku mabungwe osiyanasiyana monga a boma, omwe sali a boma,mabuku, makanema ndi zina. Ntchito yanu ina ndikuthandiza achinyamatamaganizo pamene akuchita kafukufuku.

ZINA MWAZINTHU ZIMENE ACHINYAMATA AYENERA KUDZIWA

Odziwa kusamalirandi kuthandiza ena

Odekha mtima

Osunga chinsinsi Wamtima wa bwino

Omvetsamavuto ameneachinyamata

amakumana nawo

Samapsyamtima msanga, samane-na kuti ndi otanganidwa

ukamafunsa kutiakuthandize

Ndidzikhalaomasuka ndi

otetezedwa ndikafunakuti ndilankhulanenaye

Amene amalimbik-itsa munthu kutiazichita za bwino

zokha zokha

Bonginkasi Bhayi

Page 11: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

KUKAMBIRANA M’MAGULU

11

Zokambirana zambiri za pulogalamu ya Auntie Stella, zimachitikiram’magulu ang’ono ang’ono. Nthawi zina gulu lonse limakhozansokukhala pamodzi pochita zokambirana zawo. Udindo wanu m’magawoawiriwa ndi osiyana.

Kukambirana m’magulu ang’ono ang’ono

Mu magawo amenewa, achinyamata amakhala m’magulu pameneakukambirana za ma khadi a Auntie Stella. Maguluwa amakhalaosakaniza anyamata ndi atsikana. Nthawi zina maguluwa amakhalaanyamata okha okha komanso atsikana okha okha. Muzokambirana zam’maguluzi inu muyenera:

• Kuyambitsa kuti achinyamatawo ayambe zokambirana zawo ndipomukatero muwasiye kuti apitirize okha;

• Gulu lirilonse lizikambirana modekha m’mene angathere;

• Akamaliza kukambirana za pa khadi imene ali nayo, apatseni ina;

• Muwalimbikitse kuti adzikufunsani ngati akufuna kudziwa chinthuchina chiri chonse chimene sakuchimvetsetsa, kapena pamenesakudziwa chochita komanso ngati apeza mau ena amenesakuwadziwa kutanthauza kwake (Tsamba 13 likofotokozatsatanetsatane wa zimene muyenera kuchita);

• Musamamvetsere zimene akukambirana kapena kuwafunsa mafunsopa zimene akufotokozerana;

• Musamapereke maganizo anu pa zokambirana zawo.

Kukambirana kwa onse pamodzi

Nthawi zina ndi bwino kuwasonkhanitsa onse pamodzi pochitazokambirana zawo. Zinthu zimene angakambirane onse pamodzi kapenakuchitira pamodzi ndi monga pamene akukambirana mitu ikulu ikulu yamthumba la Auntie Stella, ndime yowunikanso zimene akhalaakukambirana kwa ka nthawi, pamene akukambirana kufunika kwaAuntie Stella ndi pamene mwakonza kuti achite masewero, mtsutso,kuimba nyimbo ndi zina zotero (Ndondomeko ya mmene mungachitirezimenezi ikupezeka pa tsamba 16-22):

• Konzekerani ndime ndi zochitikachitika zonse mokwanira ndithu.Mukawona kuti sizikuyenda monga mmene munakonzera poyamba,muyenera kusintha kuti zigwirizane ndi nthawi imene achinyamataakutenga kuti amalize zimene akukambirana kapena zimeneakuchita.

• Mudziwawongolera ndi kuwatsogolera pa zokambirana ndizochitikachitika zawo.

• Muzionesetsa kuti akukambira zoona. Akonzeni mosawadzudzulangati akupereka maganizo olakwika kapena a bodza ndipo muwauzekumene angapite kuti akadziwe zambiri.

• Muwapatse nthawi yokwanira imene ayenera kutenga pazokambirana zawo ndipo auzeni kuti atsala ndi nthawi yaitali bwanjinthawiyo isanatheretu.

Page 12: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

MMENE MUNGAGWIRITSIRE NTCHITO THUMBA LA AUNTIE STELLA

Kugwiritsa bwino ntchito nthawi

Ngakhale kuti kusunga nthawi ndi kofunika kwambiri, ndi bwino kuonesetsa kuti zimene mwakonza kutimuchite, mwa chichita bwino bwino ndi kuchimaliza kusiyana ndi kuchita zinthu zambirimbiri nthawiimodzi.

Ngati muli ndi gulu lalikulu, zokambirana zanu zimatenga nthawi yaitali. Choncho ndi bwino kuwagawaanthu kuti akhale m’magulu okhala ndi anthu ochepa. Magulu onse akamaliza kukambirana abwerepamodzi kuti adzagawane ndi anzawo zimene amakambirana kumagulu awo. (Onani pa tsamba 17-22 kutimudziwe zambiri za mmene mungachitire izi)

Palibe vuto ngati mukuona kuti magulu ena akufulumira pa zokambirana zawo ndipo ena akutsalirammbuyo. Kumbukirani kuti Zoyenera Kuchita (Action Points) zina zimene ziri pa makhadi zikhozakudikira mpaka nthawi ina imene mudzakonzenso kuti gulu lonse lidzakhale pamodzi pa zokambiranakepena pa zochita zina

Pa nthawi imene mukuchita kwizi (quiz), mtsutso ndi ma roleplays, onesetsani kuti mwawauza kutizimenezi zitenga nthawi yaitali bwanji. Nthawi ikatsala pang’ono kutha muziwachenjeza ndi cholingachakuti amalize zimene akuchitazo pa nthawi yake.

Pokonza ndondomeko, onesetsani kuti mwakonzekera mokwanira kuti pamene chochita chafika kumapeto,nthawi yomweyo mukhoza kupitiriza pochita chinthu china kuopa kutaya nthawi. Pa nthawi imenezochitika kapena zokambirana zikuchitikira pa gulu lonse, onesetsani kuti mwasunga mphindi zisanukumapeto kwake kuti muthe kuwafotokozera mwachidule zimene akhala akuchita ndi kukambirana nawozimene aphunzirapo. Dziwiranitu zimene akufuna kuti adzachite mukadzakumananso ngati kuli kofunikakutero. Nthawi zonse tsekani zokambiranizi kapena zochitikazi bwino bwino osati mothamanga ayi.

Mukhoza kugwiritsa ntchito Auntie Stella mu njira zosiyanasiyana monga mkalasi, kumagulu a za achinyamata, magulu okambirana za Edzi, magulu ochita za maseweroosiyanasiyana, popereka uphungu kwa achinyamata komanso kwa makolo. Nthawi zinandime ya zokambiranazi imatenga mphindi pafupifupi 40 (nthawi zambiri kukakhala kusukulu) ndiponso nthawi zina ikhoza kutenga mmawa kapena masana onse.

Musanayambe

• Werengani makhadi onse ndi kumvetsetsa zimene akukamba kuti muthe kufotokozeraachinyamata amene angafune kuti muwathandize.

• Musanayambe ndime iri yonse kapena zokambirana ndi zochita ziri zonse onesetsanikuti mwawerenga mokwanira za mmene muyenera kuchitira dongosolo limenemwakonza. Dongosolo la zonsezi likupezeka pa tsamba 16-22

• Konzani ndondomeko ya mmene mukufunira kuti zokambirana zanu ziyendere.Ndondomeko imeneyi mukhoza kuisintha nthawi ina iri yonse malingana ndi mmenezokambirana zanu zikuyendera. (Onani chitsanzo cha bwino mu bokosi lirimmunsimu.)

• Pamene mukukonza ndondomeko yanu, dziwani kuti makhadi ena akhoza kukhalaosafunikira ku gulu la achinyamata limene muli nalo (kaya ndi ku mudzi kapena kutawoni) komanso chifukwa cha kusiyana miyambo ndi chikhalidwe. Ngati ndichoncho muyenera kuwasiya ma khadi amenewa kapena mukhoza kukambirana zamavuto ofanana ndi amene ali pa ma khadi a mtundu uwu amene achinyamata akudera lanu amakumana nawo.

• Werengani nkhani iri mu bokosi lomwe liri munsimu imene ikukamba za kugwiritsabwino ntchito nthawi. Zimenezi zidzakuthandizani kukonza ndondomeko ya bwino.

Page 13: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kuyamba zochitika

Onesetsani kuti muli ndi filipi tchati ndi zolembera.

• Chitani kalikonse kamene kangachititse kuti anthu akhale omasuka.Adziwane ngati akukumana koyamba.

• Aonetseni makhadi amafunso komanso amayankho ndipo muwauzemmene adziwagwiritsira ntchito.

• Pa makhadiwa pali Zoyenera Kuchita komanso ZoyeneraKukambirana. Auzeni kuti zonsezi ndi zofunikira kwambirichifukwa zimaonetsa m’gwirizano umene uli pa makhadi ndi zinthuzimene zimachitika mmiyoyo yawo.

• Muwawerengere ndi kuwaonetsa mndandanda wa maphunziroamene adzikambirana.

• Agwirizane ndi kukhadzikitsa malamulo amene azigwiritsa ntchitopa nthawi imene abwera ku zokambirana. Mwachitsanzo:

– Osasekana

– Kupereka mpata kwa wina aliyense kuti aperekepo maganizo ake

– Kusungirana chinsinsi

Akamaliza amate zimene agwirizanazo pa khoma.

• Muwatsimikizire kuti inu simumamvetsera zimene iwoazikambirana koma angathe kukufunsani china chiri chonse ngatiakufuna kutero. Muwaonetse khadi limene lalembedwa kuti “mauawa akuthandauza kuti chiyani” ndipo muliike pa malo akutialiyense akhoza kuliona ndi kuligwiritsa ntchito. Muwauze kutinanunso mukhoza kuwafotokozera.

• Aliyense asankhe gulu limene akufuna kukhala. Magulu amenewaakhale a anthu osachepera anthu 4 komanso osapitirira anthu 6.Gulu lirilonse lisankhe dzina la gulu lake.

• Gulu lirilonse lidzisunga mndandanda wa makhadi amene amalizakugwiritsa ntchito. Azichita izi motsatizira zimene zalembedwa patsamba 14. Inunso muyenera kukhala ndi mndandanda wa gululirilonse.

• Gulu lirilonse lidzisankhire mtsogoleri. Muwalongosolere kutintchito ya mtsogoleri ndi kuthandiza gulu lake kuti lidzisungamalamulo, kulemba mndandanda wa makhadi amene amalizakukambirana komanso kukumbutsa anzake kuti akafotokozereanzawo a magulu ena za zimene akhala akuchita.

• Maguluwa apeze malo akuti samamverana zimene anzawoakukambirana ndipo muwauze kuti akhoza kumalankhulachilankhulo chiri chonse chimene akufuna.

• Yambani ndi zinthu zosavuta. Mukaona kuti aliyense akutsatirabwino zochitika mu thumba la Auntie Stella mukhoza kuyambakugwiritsa ntchito makhadi enawo.

13

Page 14: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kaundula wa guluDzina la gulu Malo

Tsiku Khadi limene Zimene Ndemanga ndi mafunsoamaliza kukambira anachita

CHITSANZO CHA KALEMBEDWE KA KAUNDULA WAMAKHADI AMENE MAGULU ATSIRIZA KUKAMBIRANA

14

Kaundula wa otsogolera zokambirana

Gulu Nambala ya khadi Zimene Ndemangandi tsiku limene anachitaanamaliza

Ndemanga izi zikhale zokhuza zinthu zimenemwaona kuti zimayenda bwino, mavutoamene munakumana nawo, zinthu zimenemukuganiza kuti ndi zofunika kukonzanso ndizinthu zimene mukuona kuti mukhoza kuchitamwa mtundu wina mutakhala ndi mpata winaochitira zinthu zimenezi.

Ngati munakhazikitsa gulu la atsogoleri,kaundulayu adzakukumbutsani zinthu zimenemuyenera kukambirana.

Ma mamembala a gulu lirilonse akhozakulemba zimene amaona nthawi imeneamakambirana kapena amachita.Zimenezi zikhozanso kukupinduliraniinu ngati mtsogoleri.

Ndemangazi ndi mafunso amenewasayenera kulembedwa mwatsatanetsa-tane ayi koma mwachidule ngatichonchi- zokambirana zathu zinalizosangalatsa kwambiri kapena nthawiinali yochepa.

Page 15: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Mundime imeneyi achinyamata amakhala m’magulu ang’ono ang’onoophatikizana anyamata ndi atsikana. Gulu lirilonse limawerenga kalatayomwe iri pa khadi yomwe apatsidwa ndipo limagwiritsa ntchitomafunso amene ali pa Zoyenera Kukambirana kuti awathandizepokambirana vuto limene liri mkalatayo. Kenako amawerenga yankholimene Auntie Stella anapereka pa khadi la mayankho. Akateroamachita zimene khadiyo yanena kuti achite. Zochitazi akhoza kuchitapa nthawi imene akukambirana kapena nthawi ina atamalizazokambirana ndipo amadzafotokozera anzawo za zimene anachitaakamadzakumananso. Zochitikachitikazi zimawathandizakumvetsetsa nkhani imene akukambirana komanso mmene nkhaniyoimakhudzira miyoyo yawo ya tsiku ndi tsiku ndi kudziwa zimeneangachite pothana ndi zinthu ngati zimenezi.

Zimatenga pafupifupi mphindi 15 kuti gulu lirilonse limalizekukambirana khadi limodzi. Izi zimatengera ndi chidwi chimene mamembala a gululo ali nacho pa nkhani imene akukambiranayokomanso zimene akuchita.

Machitidwe ake amakhala chonchi:

• Gulu lirilonse lipatseni khadi. Mwachitsanzo ngati muli ndimagulu 5, yambani 1, 9, 17, 25 ndi 32 motsatizana ndi2,10,18,26 ndi 33. Gulu lirilonse likhozanso kusankha khadilimene akulifuna.

• Gulu lirilonse likambirane pa lokha ndipo azibwera kwa inuakafuna kudzatenga khadi la mayankho kapena khadi la mafunsokapenanso pamene akufuna kuti muwathandize kapenakukufunsani mafunso.

• Mphindi 10 ya ndime ya zokambirana isanathe, gulu lirilonsemuliuze kuti lisiye zokambiranazo ndipo ligwiritse ntchito nthawiyotsalayo polemba mu kaundula wa makhadi amene agwiritsantchito. Makhadi amene sanawakambirane akhozakudzawagwiritsa ntchito nthawi ina.

• Mutenge mndandanda wa kaundulayu ndikumusunga mu thumbala Auntie Stella.

• Muwafunse ngati ali ndi funso lina lirilonse la kagwiritsidwentchito ka makhadiwa.

• Mu gawo lina lirilonse, muzionesetsa kuti malamulo awo ajaamatidwa pa khoma kapena pa bolodi. Aliyense ayenera kukhalapa gulu lake (asasinthe gulu) pokhapokha ngati pali chifukwachokwanira chimene wina akufunira kusinthira gulu.Mudziwakumbutsa a tsogoleri a m’magulu kuti adzikumbutsa mamembala awo za kufunika kwa kusunga malamulo.

• Kenaka magulu atenge kaundula wawo wa makhadi ameneamaliza ndi makhadi amene sanawakambirane. Poyambazokambirana zina ayenera kugawana ndi anzawo zimene anachitachisiyanilareni pa gawo kapena ndime yatha.

NDIME YOKAMBIRANA ZINTHU ZOYAMBIRIRA

15

Page 16: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

16

GAWO LA AWIRI AWIRI, LOLEMBA KALATA, NDI LOKHALAM’MAGULU AKAZI KAPENA AMUNA OKHA OKHA

Kukhala awiriawirikapena atatuatatu

Kulembera kalatakwaAuntie Stella

Magulu a akazi kapenaa amuna okha okha

Pali njira zambiri zogwiritsira ntchito makhadi a Auntie Stella. Njirazimenezi zimachititsa kuti pulogalamu ya Auntie Stella kukhalayosangalatsa komanso zimakupatsani mwai owonesetsa kutiwachinyamata wina aliyense akudziwa zoona zenizeni. Zina mwanjirazi ndi izi:

Poyambirira onse akhale m’magulu awo ndipo kenaka akhale awiriawiri kapena atatuatatu. Ali awiriawiri choncho awerenge khadi lafunso ndi zoyenera kukambirana ndipo alembe mayankho awolimodzi. Akamaliza abwerere ku gulu lawo kumene onse awerengensofunso lija ndi mayankho ake. Akatero agwirizane chimodzi. Kenakoawone mmene Auntie. Stella anayankhira. Awonenso zoyenerakuchita. Kuchita zonsezi kumatenga nthawi yaitali kotero kuti mwinamukhoza kufuna kukumana kangapo kuti mukwaniritse kuchitazimenezi.

Aliyense payekha alembe kalata kwa Auntie Stella yokhuza vuto lake,kepana vuto la m’nzake kapenanso vuto la m’bale wake.Muwatsimikizire kuti palibe munthu amene adziwe yemwe walembakalata ina iri yonse. Iwo sayenera kulemba dzina pa kalata zimenealemba. Apatseni mphindi 20 kapena 25 zolembera kalata zimenezi.Amene wamaliza msanga akhoza kulemba kalata ina. Onse akamalizakulemba kalatazi, abwerere m’magulu awo ndipo apindepinde kalatazawo ndikuziika mu thumba kapena mu bokosi. Membala aliyense wagulu azitenga kalata imodzi mu thumbali ndi kuiwerenga mokwezakuti ma membala anzake amve. Akatero ma membala onseakambirane ndi kugwirizana zoti ayankhe. Muwakumbutse kuti panthawi imeneyi ndi kofunika kwambiri kusunga malamulo awo aja.Muonesetse kuti palibe munthu amene akuseka kapena kuipidwa ndizolembedwa mu kalata ina iri yonse. Kuti magulu onse amalize,mwina mungafune nthawi yochulukirapo kapena kudzapitiriza nthawiina.

Achinyamata ambiri amasangalala akhala m’magulu ophatikizanaamuna ndi akazi. Komabe mudzaona kuti mavuto ena amene ali pamakhadi ena ndi ofunika kuti anyamata akambirane paokhaatsikananso akambirane paokha. Gulu lirilonse (la anyamata ndi laatsikana) likhoza kusankha lokha makhadi amene likufuna kutilidzakambirane pa gawo limeneri ndipo inu mungowauza nthawiimene achitire zimenezi. Poyamba pa ndime yotsatira adzabwerera kumagulu awo akale aja ndipo akhoza kudzawauza ma membala anzawozimene amakambirana pa gulu la tsopanoli.

Makhadi amene akhoza kusankha pa gulu la tsopanoli ndi awa:

2 Kodi chokodzera changa ndi chaching’ono?

5 ndikuopa kukhala ndi matenda a khansa ya m’chiberekero

8 Ndimalota ndi kugonana ndi mtsikana

9 Ndimapanga piliyodi patali patali

Page 17: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

17

NDIME YOKAMBIRANA MITU IKULUIKULU

Mu ndime imeneyi gulu lililonse limakambilana mutu umenelasankha, pogwiritsa ntchito makhadi oyenera. Patsamba 18 pali mitukhumi ikuluikulu imene gulu lililonse lingathe kusankhapo kutilikambirane ndipo mitu ina yagawidwanso mmitu ina ing’onoing’ono.Akasankha mitu yoti akambirane afunseni kuti ndi mitu iti imeneakuona kuti ndiyowayenera iwo.

Makhadi ambiri ndiwogwirizana ndi mitu yambiri imeneyaperekedwayo. Choncho zokambirana zanu pamituyi zimagwirizanandi zinthu zomwe zili pamakhadiwa.

Musanayambe ndimeyi:

• Sankhani mutu/mitu. Posankha mutu kapena mitu ganiziranimozama zantchito imene mumagwira osati za Auntie Stellazokha ayi. Choncho ndikoyenera kupeza zida zoyenerazophunzitsira kupatulako makhadi. (onani pa tsamba 30 pamenepalembedwa za zipangizo zina zimene muyenera kukhala nazo).

Kumbukirani kuti pa makhadi ena, khadi lonse ndilogwirizanandi mutu umene mwasankha pamene pa makhadi ena ndi kagawokakang’ono chabe kazochitika kamene kakugwirizana ndi mutuwomwe mwasankha. Onetsetsani izi pamene mukukonzandondomeko yazokambilana zanu.

• Pali njira zambiri zimene mungachitire ndime yokambirana mituikuluikuluyi. Onani njira zina pa tsamba 19 ndi 20 ndipomusankhe njira yomwe mukufuna kugwiritsa ntchito. Komansomukhoza kupanga njira yanuyanu ngati mukudziwa bwinontchito yanu ndi gulu la achinyamata limene muli nalo.

• Konzani ndondomeko ya ndime ina iliyonse bwino lomwendiponso mudziwe kuti ndime ina iliyonse idzatenga nthawiyotalika bwanji. Mitu ina ikhoza kukutengerani masiku awirikapena kupitilira apo.

• Konzekeranitu kuti mudzafuna kuchita chiyani mmaguluang’onoang’ono ndipo ndiziti zimene mwachita pamodzi ndigulu lonse. Ganiziraninso kuti mudzakhala ndi maguluang’onoang’ono angati.

• Konzekeraninso zimene mwadzachite ngati zochita mmaguluzidzatenga nthawi yochepa kapena yaitali kuposa mmenemunakonzera poyamba.

Ndime yokambirana mituikuluikulu

(m’magulu aakulu ndiaang’ono)

Page 18: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

18

Mitu khumi ikuluikulu

9Mgwirizano

ndi anthu pabanjakomanso a mdera

lathuUbale ndi makolo komanso akuluakulu

3, 10, 24, 28, 38Kugwiritsa ntchito zithandizo zaumoyokomanso zoperekedwa mudzi mwathu:

4, 13, 14, 15, 19, 21Kuchita mgwirizano ndi athu ena pofu-

na kupeza chithandizo3, 5, 8, 26, 34

10Kusintha

kwa maderaKusintha kwa malingaliro:

9, 16, 17, 22, 38, 41Kuchitapo kanthu:4, 16, 28, 29, 35

Kuchita mgwirizanos:5, 19, 20, 29, 35

8Kulankhulazakukhosi

1, 5, 14, 16, 23, 30

1Kukula

Kusintha kwa matupi athu:2,11,18,21,35,39

Kusintha kwa kaganiziridwe kathu:23,31,37

Kusangalatsidwa ndi mmene tiliri:2,6,39

7Kukhala ndi

kachirombo kaHIV ndi matenda a

edzi14, 19, 22, 26, 40

Kukhala ndi zotsatira zakachirombo ka HIV ndi

matenda a edzi:4, 5, 38, 41, 42

6Matendaopatsiranapogonana

7, 13, 25

4Kugonanamoumilizidwa

Kugonana chifukwa cha umphawikapena khalidwe la mderalo

3,12,17,20Kugwiliridwa:8,16,20,29,36

3Kugonanamoziteteza1,11, 22, 25, 27,

33, 41, 42

2Zibwenzi ndi

kugonanaChikondi ndi kugonana:

1,6,12,22,30,34, 42Mgwirizano wa pakati pa

mwamuna ndi mkazi:3,12,16,23,30,36

AuntieStella

5Kutenga

mimbazosayem-bekezera

10,27,29,32

Page 19: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

19

Njira yoyamba

1 Onesetsani kuti muli ndi zida zokwanira zimene mungafunekugwiritsa ntchito monga zalembedwera pa tsamba 17.

2 Musanayambe gawo kapena ndime iri yonse, yambanimwawafotokozera matanthauzo a mau ena amene mukuganizakuti ndi ovuta kuwamvetsa, kapena mau achilendo monga“kupereka ndi kalandira uthenga” komanso “kuchitam’gwirizano”.

3 Poyamba pa phunziro achinyamata akhale awiri awiri ndipoalembe mafunso amene ali nawo okhuza mutu umenewasankhidwa. Inu mulembe mafunso amenewa pa chipepalachachikulu ndipo muwamate kapena kukhoma pa khoma kapenapa mtengo kuti wina aliyense adzionapo pa nthawi imeneakukambirana m’magulu awo.

4 Mugawe magulu malinga ndi kuchuluka kwa makhadi amenemuli nawo. Mwachitsanzo ngati muli ndi makhadi anayi, ndiyekuti magulu akhalenso anayi. Gulu lirilonse mulipatse khadilimodzi ndipo akamaliza asinthane makhadiwo kuti gulu lirilonselikhale ndi mwai wokambirana makhadi anayi onsewo. Ngatipanali choti achitire onse pamodzi, muwauze kuti achisiye kayempaka nthawi yake itakwana

5 Onse akamaliza kuwona makhadiwa, afunseni kuti akuuzenizimene makhadiwa akuphunzitsa ndipo inu muzilembe pachipepala chachikulu. Mukatero muwatsogolere kukambiranakapena kuchita zinthu zimene analephera kuchita ali m’maguluawo kapena zimene inu mwaona kuti ndi zofunika kuchitiralimodzi. Muonesetse kuti pali m’gwirizano pakati pa zimeneakuchitazi ndi maphunziro amene analemba poyamba paja.

6 Pomaliza onaninso mafunso amene analemba poyamba pa ndimeino. Kodi akhoza tsopano kuyankha mafunso amenewa? Ngatipali mafunso ena amene akuwavutabe awuzeni kumene angapitekuti akawathandize ngati inuyo simungathe kutero. (Nthawi zinamukhoza kuwona kuti zimene sakuzimvetsetsazo ndi zofunikakudzakambirana pa mutu wina ndipo izi zizakupatsani mwaiwokonzekera ndondomeko ya bwino ya zokambirana za tsikulina).

7 Pomaliza muwafunse kuti akufuna kuchitapo chiyani atamalizakukambirana za mutu umenewu – aliyense payekha; ndi abaleawo; zibwenzi zawo komanso ndi anthu ena a m’madera awo.Kumapeto kwa ndime ino ndi ndime zina zonse ndi kofunikakwambiri. Choncho onesetsani kuti muli ndi nthawi yokwanira.

Page 20: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

20

Njira ya chiwiri

• Gwiritsani ntchito ndondomeko 1, 2, ndi 4 zimene ziri mu njirayoyamba;

• Aliyense akamaliza kuwona makhadi mufunse mafunso awa:

– Mwaphunzirapo chiyani pa zokambirana zanu?

– Kodi mavuto amene amakambidwa m’makhadi akugwirizanabwanji ndi mavuto amene mumakumana nawo pa moyo wanuwa tsiku ndi tsiku kapena miyoyo ya anthu a m’dera lanu?

– Kodi mukudziwapo anthu kapena mabungwe ena ameneakugwira ntchito yothana ndi mavuto ngati amenewa ku deralanu? Kodi anthu ndi mabungwe amenewa amatani?

– Ndi zinthu ziti zimene mungafune kuti muzisinthe m’dera lanumalingana ndi nzeru zimene mwapeza pokambirana ndi anzanupa mutu umenewu?

– Kodi ndi luso lotani limene mungafune kuti mukhale nalo lakutilikuthandizeni kusintha zinthu zimene mwatchulazi? Nanga lusolimeneri mulipeza bwanji?

• Pomaliza muchite zinthu zimene munakonza.

Njira ya chitatu

• Gwiritsani ntchito ndondomeko 1 ndi 2 ya njira yoyamba;

• Gulu lirilonse likambirane khadi limodzi losiyana ndi la anzawondipo muwapatse nthawi yakuti akambirane. Akamaliza abwereonse pamodzi kudzagawana ndi anzawo zimene akambiranapoyankha mafunso awa:

– Kodi ndi vuto lanji limene limakambidwa pa khadi limenemunali nalo?

– Nanga ndi langizo lotani la bwino limene lingaperekedwe kuvuto limeneli. Apereke chifukwa chani?

– Kodi khadi limeneri ndi lofunika bwanji pa miyoyo yanu?Abwenzi anu? Ndi anthu ena a m’dera lanu?

• Pomaliza imbani nyimbo kapena kuchita sewero, mtsutso kapenachina chiri chonse chokhuzana ndi mutu umene amakambiranawu.

Njira ya chinayi

• Sankhani zoyenera kuchita kuchokera pa makhadi malinga ndi mutuumene mwasankha kuti gulu lonse likambirane.

• Chakumapeto azokambirana zawo, afunseni achinyamata kutiakambirane mafunso otsatirawa. Poyamba akhale awiri awiri ndipoakatha abwere onse pamodzi.

– Kodi mwaphunzirapo chiyani?

– Kodi mukufuna kuchitapo chiyani malingana ndi nzeru zimenemwagawana ndi anzanu pokambirana za mutu umenewu ngatimunthu panokha, ndi abwenzi anu komanso ndi anthu a m’deralanu.

Page 21: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Mafunso oyenera kufunsa mu gawo limeneri

• Tchulani chimene chikumakusangalatsani kwambirikapena pang’ono pa makhadi a Auntie Stella?

• Kodi ndi zinthu ziti za phindu zimene mwaphunzirakuchokera ku makhadi amene mwakhala mukugwiritsantchito? Kodi muli ndi mafunso ena aliwonse pa nkhanizimene mwakhala mukukambirana?

• Tchulani zinthu zimene mukuona kuti ndi zofunikirakwambiri zimene mwakhala mukuchita?

• Kodi pali kusintha kwina kuli konse kumene kwachitikapa moyo wanu (kaya kusintha khalidwe, maganizo ndimachitidwe a zinthu zina) chifukwa cha pulogalamuimeneyi?

• Kodi mwakhala mukugwira ntchito bwanji ntchito ndianzanu kapena mabungwe a m’dera lanu pofunakusintha miyoyo yanu komanso madera anu?

KUWONANSO NDI KUWUNIKA ZIMENE MWAKHALAMUKUKAMBIRANA

Kuwonanso ndi kuwunikazimene mwakhalamukukambirana

(m’magulu aakulu ndiaang’ono)

21

Mu gawo limeneri, achinyamata amakambirana zimene akhalaakuphunzira ndi mmene zikusinthira miyoyo yawo. Akhozakukufunsani mafunso ena aliwonse amene ali nawo. Izi zimakupatsaniinu mwai wodziwa mmene pulogalamuyi ikuyendera ndi kudziwazinthu zimene achinyamata aphunzira. Ndi chinthu cha nzeru kukhalandi gawo limeneri makamaka pakakhala kuti papita nthawi yaitaliachinyamata akukumana m’magulu ang’onoang’ono asanakumaneonse pamodzi. Udindo wanu pa gawo limeneri, ndi kupereka uthengaumene achinyamata ayenera kuwudziwa, kukonza maganizo amenemukuona kuti ndi olakwika komanso kuwaunikira kumene angapitekuti akadziwe zoona zenizeni. Lembani mafunso otsatirawa pachipepala chachikulu kapena pa bolodi gawo limeneri lisanayambe.

Page 22: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

22

Nthawi zambiri chimakhala chinthu cha pafupi kuti anthu akambiranemafunso amenewa mmagulu mwawo kaye makamaka akakhalaochuluka kupitirira 15. Akatha kukambirana mmagulumo abwere onsepamodzi kudzagawana ndi anzawo zimene amakambirana.

Akabwera onse pamodzi, zokambirana zawo, mwachidule, zikhuzemitu itatu iyi:

1 Zimene makhadi akufotokozaNdemanga zawo pa zinthu zimene aphunzira komanso pamafunso amene ali nawo

2 Dongosolo la Auntie StellaZimene akonda komanso zimene sanazikonde

3 KusinthikaNgati pali kusinthika kwa mtundu wina uliwonse, kayammiyoyo yawo, m’mabanja awo kapenanso m’maderaamene amakhala

Onesetsani kuti maganizo awina aliyense akulemekezedwa, kayaakunena zopanda nzeru kaya za nzeru. Komanso muzisiyanitsa pakatipa mfundo ndi maganizo chabe.

Mafunso ena owonjezera amene mungathe kugwiritsa ntchito pagawo limeneri

• Kodi chimene mwachipeza cha phindu mu Auntie Stella ndi chiyani?

• Ngati munalemba kalata yanu, kodi muli ndi nkhani kapena mafunso amenemungafune kuti mugawane ndi anzanu?

• Inu anyamata, kodi munawaona bwanji maganizo a atsikana pa nthawi imenemunali nawo gulu limodzi? Nanga inu atsikana, munawaona bwanjimaganizo a anyamata pamene munali nawo gulu limodzi?

• Kodi Auntie Stella akuthandizani bwanji pa za mmene inu mukumaganiziratsopano za; inu ndi thupi lanu, ubale wanu ndi anzanu, ndi abwenzi anu, apabanja komanso anthu a m’dera lanu?

• Kodi Auntie Stella akusinthani pa zinthu zimene mumachita m’moyo wanu?Fotokozani.

• Mwaphunzira zotani za anthu kapena mabungwe amene amagwira ntchitoyothandiza achinyamata m’dera lanu (kaya a zamaphunziro, a zachipatalakomanso atsogoleri osiyanasiyana a m’dera lanu)? Kodi Auntie Stellaakusinthani maganizo a momwe mumaganizira za anthu kapena mabungweamenewa?

• Kodi ndi njira ziti zimene mwapeza kuti inu ndi anzanu mukhozakuzigwiritsa ntchito kuti musinthe zinthu?

• Kodi tsopano mutha kutengapo mbali pogwira ntchito zimene zimakhudzamoyo wanu zochitika m’dera lanu?

• Kodi ndi zinthu ziti zimene mungafune kuti m’zazisinthe mtsogolomu?

Page 23: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

23

MMENE MUNGAKONZERE MASEWERA OSIYANASIYANA

MaseweroAnyamata amapatsidwa nkhani kapena kuyerekeza kuti china chakechachitika kapena chikufuna kuchitika ndipo iwo amafunsidwa kutiakanakhala kuti iwo ndi amene akhudzidwa mu nkhaniyi akanatanipothetsa vuto limene laperekedwalo. Mwachitsanzo- mtsikanakuyesezera kuuza bwenzi lake kuti agwiritse ntchito kondomu kapenamnyamata kukakamiza bwenzi lake kuti agonane naye. Cholinga charole play kapena sewero la mtundu uwu, ndi kuona zimenezimachitika anthu akamakambirana ndi mmene zochitika msewerolizimakhudzira miyoyo yawo tsiku ndi tsiku osati kuti katswiri ndaniayi.

Role play kapena sewero la mtundu uwu likhoza kupangidwa ndianthu awiri kapena atatu pamene gulu lonse lingoonerera. Kapenansoaliyense akhoza kutengapo gawo m’seweroli kenako onse ndikubwerapamodzi kudzakambirana zimene zimachitika mu sewelo.

Ngati akuchitira mmagulu awo, muwauze kuti adzigwiritsa ntchitomafunso amene ali pa makhadi. Ngati onse akuchitira pamodzionesetsani kuti mukuwathandiza kwambiri. Pomaliza muwathokozeonse amene anapanga nawo role play. Musaiwale kuliwuza gulu lonsekufunika kwake kochitira zimenezi. Nthawi zonse akamaliza kuchitarole play muziwafunsa kuti –mumamva bwanji mu mtima mwanupamene mumachita role play. Nanga anzanu amakuganizirani zotani?

Role play in action

Page 24: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

24

Izi zimathandiza kulekanitsa umunthu wa mu role play ndi umunthuweniweni. Zimathandiza kwambiri ngati mu role play muja munthuamatenga mbali yoonetsa makhalidwe oipa.

Kenaka onse akambirane: Chimachitika ndi chiyani? Chifukwachiyani zimachita zimenezi? Kodi zimenezi zingachitikedi mmoyowathu wa tsiku ndi tsiku? Kodi amene amachita role play aja, anapezanjira ya bwino yothetsera vuto? Kodi mwatolapo kapena kuphunzirapochiyani kuchokera mu role playi? nanga ndi chithandizo cha mtunduwanji chimene mungafune kuti chikuthandizeni kuthana ndi mavutongati amenewa?

Sewero loyimitsaUwu ndi mtundu wina wochitira role play. Chimene chimachitika ndichakuti achinyamata ena amachita sewero ndipo ena amangoonerera.Amene akuonerawa akaona kuti wina sakuchita bwino monga mmeneiwo angachitire pothetsa vuto limene liri museweromo amaimitsaseweroli pokweza dzanja. Akatero iwo amasinthana ndi muthu ameneamamuona kuti samachita bwino uja.

Pomaliza musakambirane kuti katswiri ndani pochita seweroli ayi.Koma mukambirane za njira ya bwino imene ena anagwiritsa ntchitopofuna kukwaniritsa cholinga cha seweroli. Mwachitsanzo, kufunsaakuluakulu kuti akuthandizeni maganizo.

Kugwiritsa ntchito ziganizo pokambiranaMumakhala ndi ziganizo zingapo. Ziganizo zimenezizikawerengedwa, achinyamata amanena kuti akugwirizana nazokapena kuti sakugwirizana nazo. Poyamba aliyense amalemba yankholake payekha. Kenaka amakhala awiri awiri kapena mmagulu awommene amawerenganso ziganizo zimenezi ndi kuona ngati mayankhoawo akufanana. Akasiyana, amayenera kugwirizana chimodzi.

Ngati onse achitire pamodzi, lembani mau akuti ndikuvomereza,sindikuvomereza ndi ndikukaikira. Liwu lirilonse muli khome palokha pa lokha. Mukatero mudziwerenga chiganizo chimodzichimodzi ndipo achinyamatawo aziyankha pokhala kapena kuimapamene palembedwa yankho limene ali nalo. Musachite izi kwanthawi yaitali kuti achinyamata angayambe kutaya chidwi.

Kufunsa ndi kuyankha mafunsoNjira ina yoyambira zokambirana ndi yofunsa mafunso kutiachiyamata aziyankha. Ichi ndi chinthu chokondweretsa ndipotisachite ngati mayeso m’kalasi. Mukhoza kuchita m’magulu a anthuawiriawiri kapenanso kuposerapo pang’ono. Mwinanso mukhozakuwerenga mafunso kuti aliyense ayankhe ndikudzichongerapayekha.. Chofunika kwambiri ndi kukambirana akamaliza kuyankhamafunso chifukwa mafunso ena amakhala okhuza mmene munthuamaganizira pa zinthu zina osati okhuza mfundo zenizeni za zinthu.

From a drawing by Mkhululi Khumalo

Page 25: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

25

Zithunzi ndi zinthu zojambulaAchinyamata akhoza kujambula zithunzi pa pepala, bolodi kapenansopa mchenga. Muwafotokozere kuti chofunika ndi maganizo awo osatikutha kujambula zinthu zokongola ayi. Agwiritse ntchito zimeneajambulazo pofuna kuwonetsa maganizo awo ngati mmeneakanachitira akanakhala kuti akulemba. Mwachitsanzo, pofunakuwonetsa gwero la vuto, ajambule mtengo nawonetsa mizu imeneikuimirira kapena kuonetsa zoyambitsa vuto komanso kuwonetsanthambi za mtengowu zimene zikuimirira zotsatira za vutolo ndipotunthu liimirire vuto lenileni.

MtsutsoSankhani mutu kapena phunziro loyenera makamaka limeneachinyamata samalimvetsetsa bwino. Musankhe awiri ameneadzitsutsa ndiponso ena awiri amene azivomerezana ndi mutu umenewasankhidwawo. Magulu onse awiri muwapatse nthawi yokutiakonzekere mfundo zawo. Musaiwale kusankha wa pampando kutiaongolere mtsutso umenewu.

Ndikudziwa kuti ukufunazimenezo Charlo, Koma kodi

ndife okonzeka kupangazimenezo?

Page 26: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

26

Mukhozanso kuchita mtsutso umenewu ndi ma gulu 6; atatu otsutsaenanso atatu ovomereza. Gulu lirilonse lidzisankhire munthu ameneadziliyankhulira komanso kulithandiza kusonkhanitsa mfundo.Cholinga chochitira motere ndikufuna kupereka mwai kwa winaaliyense kuchita nawo mtsutso umenewu. Onesetsani kuti mwakonzanthawi yokwanira ndithu monga nthawi yokonzekera, nthawi yamtsutso komanso nthawi ya mafunso.

Masewero ndi nkhaniMasewerowa akhoza kukonzedwa ndi gulu lirilonse palokha.Akamaliza abwere kuti adzaonetse ku gulu lonse. Muwapatse mutukapena nkhani yakuti achitire sewero. Mwachitsanzo nkhani yokhuzakutenga pakati mtsikana asanakhwime msinkhu kapena yoyezetsamagazi kuti munthu adziwe ngati ali ndi kachilombo ka HIV kapenaayi. Inu musawapatse maganizo anu kapena tsatanetsatane wake ayi.Gulu lirilonse mulipatse nthawi yokonzekera komanso yakuti lionetsesewero lake. Konzani nthawi yokwanira yakuti magulu aonetsemasewero awo. Ngati nthawi yakutherani konzani nthawi ina kapenatsiku lina kuti muwapatse mwai magulu amene sanaonetse kutiadzaonetse masewero awo nthawi imeneyo. Pomaliza kambirananinawo za zimene aphunzirapo pa masewero amenewa.

Kuitana anthu ogwira ntchito zaachinyamataMukhoza kufufuza ndi kuitana anthu amene amakonda kugwirantchito ndipo ali ndi luso lothandiza achinyamata kuti adzayankhulendi gulu lanu pa za ufulu wa achinyamata komanso pa za mavutoamene achinyamata ambiri amakumana nawo. Muwauze achinyamataanu kuti akonzekeretu mafunso kuti adzafunse pa nthawiyo.

KafukufukuAchinyamata mukamapita nawo kumalo kumene akhoza kukapezachithandizo monga kuchipatala, amalimbikitsidwa kukhala ndi lusolofunsa ndipo pa tsogolo pake amatha paokha kupita kukapezachithandizo chimene akufuna. Inuyo kambiranani ndi mabungweamene amathandiza achinyamata m’dera lanu kuti nawonso akhalegawo limodzi la Auntie Stella. Izi zidzathandiza kwambiriachinyamata kumapita okha kumabungwe amenewa kuti akadziwezinthu zimene zimawavuta pa moyo wawo.

Akabwerako kochita kafukufuku ndipo akufuna kugawana ndi anzawozimene apeza onesetsani kuti mwawapatsa nthawi yokwanira.

Page 27: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

27

MAVUTO AMENE OTSOGOLERA ZOKAMBIRANAANGAKUMANE NAWO

Ngati achinyamata akugawana maganizo ndi uthengaolakwika?Izi zikhoza kuchitika mmagulu pamene inu simumamvetsera zimeneamakambirana. Vuto ngati ili mukhoza kulithetsa pogwiritsa ntchitomayankho odalirika a Auntie Stella. Pa nthawi ija yowunikansozimene mwakhala mukuchita, mukhoza kudziwa zimene anyamataakhala akukambirana ndipo pa nthawi imeneyi mutha kuperekamaganizo kapena mfundo zokhonza kapena zolondola.Komanso onesetsani kuti mukusiyanitsa pakati pa maganizo chabe ndimfundo zenizeni. Muyeneranso kuwonetsetsa kuti achinyamataakudziwa zowona zenizeni (monga mmene kachilombo ka HIVkamafalikira) pakugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana monga kuchitamtsutso, mabuku owerenga ndipo akamaliza kuwerengako abwereonse pamodzi kuti adzakambirane zimene amawerengazo. Koma pazinthu zokhudza achinyamata kuti apereke maganizo awo (mongamwachitsanzo, kuti tidzitsata miyambo ya makolo kapena ayi) palibeyankho lolondola kapena lolakwika. Pamenepa yankho la winaaliyense ndi lanunso ndi lofanana. Chofunika kwambiri ndikuwalimbikitsa achinyamata kulankhula maganizo awo. Inumukaperekapo maganizo anu muwauze kuti ali ndi ufulu owatengakapena ayi chifukwa sakukakamizidwa kutero.

Ngati achinyamata akukambirana zinthu zimene inumukuganiza kuti ndi zochititsa manyazi kapena zolaula

Anthu ambiri amachita manyazi kulankhula pagulu zinthu zimenezimakhudza kugonana. Komabe inu ngati mtsogoleri muyenerakuyesetsa kumatero. Poyamba zimakhala zovuta kwambiri. Komapakapita nthawi, mumayamba kuzolowera. Miyoyo ya achinyamataikhoza kukhala pa chopsyezo chachikulu ngati sitiwathandizakudziwa zinthu zimene zimakhudza miyoyo yawo ndiponso ngatisitiwapatsa luso losiyanasiyana limene lingawathandize kuchitachisankho choyenera ndi kuchita zinthu zimene zingawathandizekuteteza miyoyo yawo. Ayenera kukhala ndi mwai wokambiranazinthu zimene zimakhudza miyoyo yawo komanso zinthu zina zachinsinsi. Choncho khalani omasuka kwambiri powalimbikitsa kutialankhule za kukhosi ndi kuwalimbikitsa kulankhula pamene akuchitamanyazi. Sibwino kungokhala chete chifukwa kutero kumalimbikitsakuti achinyamata azikhalabe ndi maganizo olakwika. Kukhalaomasuka kumathandiza achinyamata kumakambirana zinthu zabwinozimene zingasinthe miyoyo yawo.Nthawi zina zimathandiza kuti pakhale mtsogoleri wa mwamuna ndiwa mkazi. Wa mwamuna azikhala pa gulu la anyamata ndipo wamkazi azikhala pa gulu la atsikana. Zikatha zokambiranam’maguluwa onse adzibwera pamodzi kudzagawana zimeneamakambirana.

Page 28: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

28

Ngati inu kapena achinyamata simukugwirizana ndizimene Auntie Stella akunenaPalibe vuto ngati inu kapena achinyamata simukugwirizana ndizimene Auntie Stella akunena. Dziwani kuti palibe mayankhoolakwika kapena olondola (pokha pokha zikakhala mfundo zenizeni).Mukawonesetsa pa Zoyenera Kuchita Auntie Stella amangofunsa kutimaganizo achinyamata ndi otani. Chofunika kwambiri ndi chakutiachinyamata adzitha kusiyanitsa maganizo osiyanasiyana ndi kuchitachisankho choyenera. Musawakakamize kuti atenge maganizo anu.

Ngati m’modzi wa achinyamata akukwiya kapenakukhumudwa kwambiri?

Maphunziro ambiri a Auntie Stella amakhudza miyoyo ya anthu.Choncho sichikhala cha chilendo kuti wina akhumudwe kapenakukwiya. Ngati wina wakwiya kapena kukhumudwa kwambiri,mutengereni pa mbali kuti mukakambirane naye kapena kukangokhalanaye kuti mwina mtima wake ungakhale pansi. Pezani khansala(munthu opereka uphungu) ngati ndi kofunika kutero. Musanayambentchito yanu, pezeranitu ma khansala abwino amene amapezekam’dera lanu. Ma khansala abwino amapereka uphungu ndikumuthandiza munthu kuti achite chisankho choyenera osatikumulangiza munthu ndi kumuuza zochita ayi.

Ngati achinyamata akutsutsana kwambiri?Ili sivuto ayi. Kumbukirani kuti cholinga cha Auntie Stella ndicholimbikitsa wa chinyamata wina aliyense kumapereka maganizo pazokambirana zina ziri zonse. Ngati onse ali pamodzi ndipo winaaliyense akufuna kupereka maganizo ake nthawi imodzi, ndi chanzerukuti muwagawe akhale mmagulu ndi kuwauza kuti ayenera kutiadzipatsana mpata polankhula.

Njira ina ndi yopereka ka mtengo kwa munthu amene akufunakulankhula. Akamaliza ampatse mnzake. Muchite izi mpaka aliyenseatalankhulapo ndipo muchite izi ngati macheza. Ndi udindo waatsogoleri kuonesetsa kuti izi zatheka. Muwapatse nthawi yakutiakambirane ndipo aonesetse kuti agwirizana chimodzi nthawiyiisanathe.

Ngati ena akuchita phokoso kwambiri lakuti lingasokoneze anzawo,auzeni kuti akakambirane panja.

Ngati achinyamata sakufuna kulankhula?

Izi zikhoza kuchitika pamene achinyamata onse ali pamodzi. Poyambamuonesetse kuti wina aliyense wamvetsetsa chimene chiyenerakuchitika. Kodi kapena mafunso ndi ovuta? Onesetsani kutimwawalembanso bwino kuti asakhale ovuta ndipo ngati zikukanikabe,mungochotsa mafunso amene akuvutawo.

Page 29: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

29

Ngati sakulankhula chifukwa cha manyazi, auzeni akambiranemmagulu awo, kapena awiriawiri, kapena atatu atatu ndipo muwauzekuti onse akamaliza abwere pamodzi kuti adzakambirane ndi gululonse.Ngati sakulankhula chifukwa chakusasangalatsidwa ndi phunziro, inumusadandaule ayi. Mungolisiya phunziro limeneri ndi kutenga lina.

Ngati mulibe nthawi yokwanira yochitira zonse zimenemwakonzaIzi zimachitika nthawi zambiri pamene achinyamata akukambiranakapena kuchitira zinthu pamodzi. Ili sivuto lodetsa nkhawa ayi.Chimene muyenera kuchita ndi chakuti muzisintha zochita malinganandi mmene zikuwasangalatsira kapena akuchitira. Zina mwa zinthuzimene mungachite ndi izi:

• Mukhale ndi nthawi yambiri kapena magawo ambiripokambirana mutu umodzi;

• Mukonze ndime imodzi kuti mudzachite zochitikachitika zakhadi limodzi;

• Mudziyamba mwadziwa zimene achinyamata akufuna kuchita;

• Muziyamba kuchita chinthu chofunika kwambiri;

• Muzigwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana pamene akukambiranamitu ikuluikulu (mwachitsanzo mukhoza kuyamba ndi gawo lakufunsa ndi kuyankha mafunso). Onani gawo la kugwiritsabwino ntchito nthawi pa tsamba 12.

Page 30: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

30

MAPHUNZIRO OYENERA ANTHU OTSOGOLERAZOKAMBIRANA NDI CHITHANDIZO CHIMENE ANGACHIFUNE

Ngati munaphunzitsidwapo kale kutsogolera maphunziro ngati aAuntie Stella ndiponso kuti mukudziwa kale zambiri za mavuto aumoyo wa ubereki wa achinyamata ndiye kuti simuvutika kugwiritsantchito Auntie Stella. Atsogoleri ena akhoza kupindula kwambiri ndimaphunziro apadera okonzedwa bwino owathandiza mmeneangatsogolere maphunziro a Auntie Stella. Zina zimene atsogoleriamenewa ayenera kuchita ndi izi:

• Ayambe kaye aphunzira magawo onse a Auntie Stella ngatimunthu wina aliyense.

• Mukhale oyamba kudziwa mfundo zenizeni zokhudza mituyofunikira kwambiri imene ikupezeka m’makhadi ena. Tiyeneraifeyo kukhala oyamba kuchotsa maganizo athu ena oipa pankhani zimene zimakhudza achinyamata.

• Pezani mwai wokonzekera kutsogolera maphunziro amtundu uwuamene amapereka mwai kwa wina aliyense kutengapo mbali.Ndipo muyese kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zimenezimapezeka m’maphunzirowa ndiponso mukambirane ubwinondi kuipa kwa njirazi.

• Mukhoza kukhala nokha, kapena awiri awiri pamenemukukonzekera kutsogolera maphunzirowa ndipo nonse mukhalendi nthawi yokambirana pamodzi zimene mukuphunzira. Ngatiwina anali ndi vuto, amathandizidwa nthawi imeneyi.

• Kambiranani kufunika kosunga chinsinsi kuti achinyamataadzikukhulupilirani. Miseche ikhoza kuononga maphunziro onsea Auntie Stella.

• Muphunzire kukhala ndi zinthu zomuyenereza mtsogoleri wabwino ndi khansala wa bwino. Kumbukirani kuti khansala wabwino ndi amene amathandiza munthu kupanga yekha chisankhochoyenera osati kumuuza munthuyo zochita.

Chitsanzo cha ndondomeko ya padera ya maphunziro apadera amtsogoleri yaperekedwa pa tsamba 29. Maphunziro ngati amenewaamachitika malinga ndi zimene ophunzira akufuna kudziwa, nthawiimene iripo komanso chuma chimene chiripo.

Ngati atsogoleri sakudziwa china chiri chonse chokhudza umoyo wa achinyamata, ayenera kuphunzitsidwa nthawi yaitali.

Page 31: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

CHITSANZO CHA NDONDOMEKO YA MAPHUNZIRO A ANTHUOTSOGOLERA ZOKAMBIRANA

TSIKU LOYAMBA:

Gawo 1: KudziwanaAnthu ayambe adziwana. Anene zimeneakuyembekezera kupeza pa maphunzirowa komansozimene akuopa. Akambirane ndi kugwirizanamalamulo amene adzitsatira pa nthawi yamaphunziro.

Gawo 2: Kudziwa za kutsogolera maphunzirokumene aliyense amapatsidwa mpataotengapo mbali?

Zimene anthu akudziwa kale (role play), Kodimtsogoleri wa bwino amatani? Kufunika koperekamwai kwa wina aliyense kutengambo mbali pamaphunziro okhudza nkhani za kukula kapena kuthamsinkhu ndi umoyo wa ubereki wa achinyamata.

Gawo 3: Kodi Auntie Stella ndi chiyani?Magulu agwiritse ntchito makhadi a Auntie Stellakwa mphindi 45–60. Akamaliza onse abwere pamodzikudzakambirana zimene aphunzira, zimene akonda,zimene sanazikonde komanso zimene akuona kuti ndizovuta. Kenaka aphunzitsi afotokoze kufunika kwamakhadiwo komanso njira zimene zimagwiritsidwantchito pa ndondomeko ya Auntie Stella.

Gawo 4:Kusanthula thumba la Auntie StellaOtsogolera akhale mmagulu ndipo asanthule thumbalonse la Auntie Stella. Kenaka asankhe makhadi awirikapena atatu kuchokera pa mndandanda wamakhadiwa. Makhadi amene angasankhe akhaleamene maphunziro ake ndi achilendo kwa iwo,akuwadetsa nkhawa kapena amene akuwasangalatsa.Akamaliza kukambirana mmagulu abwere onsepamodzi ndipo akambirane mmene angagwiritsirentchito makhadiwa ku madera a kwawo.

TSIKU LA CHIWIRI MPAKATSIKU LACHITATU

Kudziwa mfundo zenizeni za maphunziro ena amthumba la Auntie Stella (Akhoza kusankha kutiaphunzire kapena ayi).

Nkhani ya kachilombo ka HIV ndi matenda a Edzi,umoyo wa ubereki wa achinyamata, kugwiritsantchito chithandizo chopezeka m’madera komansocha za umoyo ndi achinyamata ngati otsogolerazokambirana pa nkhani yosintha zinthu.Mu gawolimeneri mumagwiritsa ntchito makhadi ena a AuntieStella kuti mumvetsetse.

TSIKU LA CHINAYI:Gawo:1 Kukambirana mwa chidule zimenezinachitika dzuloGawo:2 Udindo wa mtsogoleri

Mgawo ili anthu akhoza kukhala m’magulu kapenaakhoza kukhala pamodzi ndipo amakambirana zandime ya kufunika kwa kuwonanso kapenakuwunikanso zimene achinyamata akhala akuchitakomanso za nthawi ya bwino yokambirana ndimeimeneyi.

Gawo 3: Zoyenera Kukambirana ndiZoyenera Kuchita

Kusiyana kwa zinthu ziwirizi. Zinthu zoyenerakuchita zimene ziri mthumba la Auntie Stella,Kukambirana za anthu kapena mabungwe ameneamagwira ntchito yothandiza achinyamatamongodzipereka.

Gawo 4: Ndime yokambirana mitu ikuluikuluyopezeka mthumba la Auntie Stella

Kukambirana za mitu imeneyi ndi njirazosiyanasiyana za kagwiritsidwe ntchito ka mituimeneyi

Gawo 5: Mavuto amene otsogolerazokambirana angakumane nawo (akhozakusankha kuphunzira kapena ayi)

Awerenge zimene zalembedwa mbukhu lino pankhani za mavuto ngati amenewa. Atsogoleriwaakhale mmagulu ndipo ayesezere kuwonetsa mavutoamene mtsogoleri amakumana nawo pameneachinyamata akukambirana. Ena azichita makanikapena kutsutsana kwambiri ndipo ena aziperekamaganizo a bodza. Akamaliza onse abwere pamodzikuti akambirane njira zimene angathe kugwiritsantchito pothana ndi mavuto ngati amenewa.

Gawo 6: KukonzekeraNthawi yokonzekera mmene adzikagwiritsira ntchitothumba la Auntie Stella akabwerera kwawo kapenakumalo awo a ntchito. Nthawi imeneyi ndiyofunikakuwonanso zimene anthu analemba zokhuza zinthuzimene amayembekezera kuphunzira komansozimene amaopa. Mukatero tsekani maphunziroatsogoleriwa.

31

Page 32: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

32

MABUKU ENA AMENE MUNGAGWIRITSE NTCHITO

Choices:A guide for young people

Bukhu limeneri analemba ndi Gill Gordon ndipo mukhoza kulipeza pawww.talkuk.org

Ngati muli ndi ndalama zokwanira kugula bukhu limodzi lokha, ndiyebukhu lake likhale limeneri. Bukhu limeneri limakamba zinthuzambiri za chinsinsi zokhuza achinyamata ndipo limapereka chikokakwa achinyamata. Ndilophweka kuwerenga ndipo analisindikizamwamakono.

ABC of all the questions we never dare to ask

Bukhu ili linatsindikizidwa ku South Africa ndi Akwela Books(www.kwela.com) komanso ndi a Weaver Press a kuZimbabwe(www.weaverpresszimbabwe.com)

Bukhuli liri ndi mafunso ochokera kwa achinyamata komansolimapereka mayankho osavuta kumvetsa. Ndi losavuta kuwerenga,lokongola, limafotokoza zinthu zimene zingathe kuchitika ndiponsoliri ndi uthenga othandiza kwambiri.

Bodywise: Sex education, health and advice for SouthAfrican youth

Bukhu iri linasindikidwa ndi Sached Books PO Box 396 Cape Town8000 South Africa.

Ndi bukhu losangalatsa kwambiri komanso lomwe liri ndi nkhanizosavuta kuwerenga zimene zimachitikira achinyamata. Bukhuli lirindi maganizo ochokera kwa achinyamata. Chosangalatsa china ndichakuti liri ndi makatuni ndi zithunzi zokomera achinyamata.

You, your life, your dreams:A book for adolescents

Bukhu iri linalembedwa ndi Caroline Watson ndi Ellen Brazier.Linatsindikidwa ndi a Family Care International (Kenya) ndi aStraight Talk (Uganda) Email: [email protected]

Ndi bukhu lalikulu ndithu limene liri ndi uthenga ofunikira kwambiriwokhudza makulidwe.

You asked…We answered! :Answers to questions onHIV and AIDS asked by youth in Southern Africa!

Bukhuli mungalipeze kuchokera ku SafAIDS pa [email protected]

Pali timabuku ting’ono ting’ono titatu tokhala ndi mafunso komansomayankho pa nkhani zosiyanasiyana za HIV ndi Edzi.

Stepping stones

Linalembedwa ndi Alice Welbourn ndipo mungalipeze kuchokera kuTALC pa www.talcuk.org ndi bukhu la bwino kwambiri lophunzitsirankhani za HIV ndi Edzi, kupereka ndi kulandira uthenga, lusolofunika kukhala nalo pa nkhani ya ubale ndi zibwenzi.

Kumbukilrani

Bungwe lina lirilonselikhonza kupereka uthengawina woojezera pamfundozosiyanasiyana zokhudzaumoyo ndi kakulidwe kaachinyamata.

Page 33: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kuthokozakwapadera

Page 34: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

34

Bungwe la YONECO likuthokoza anthu ndi mabungwe a muno m’Malawikomanso kunja kwa dziko lino amene anatengapo mbali ndi kuthandizapakusindikizidwa kwa bukhu la ‘Auntie Stella’ Mchichewa. Thandizolimeneli ndila mtundu wina uliwonse monga, Kafukufuku, Kulemba,kumasulira mchichewa, Kukhala nawo pa misonkhano, kupereka ndemanga,kujambula zithunzi za mubukhuli, kuyesa bukhuli ndi achinyamata komansothandizo la ndalama. Mwapadera, tikuthokoza anthu ogwira ntchitokumabungwe a YONECO ndi TARSC chifukwa cha kudzipereka kwawopantchito yosindikiza bukhuli.

Maganizo a Bukhuli: Barbara Kaim (TARSC)Womasulira Mchichewa: Golden Raphael Kang’omaAlangizi apadera: Mac Bain Mkandawire ndi Senele

DhlomoKafukufuku ndi kuyesara: Felix Limbani ndi Emmanuel KanikeMkozi wa Bukhuli: Margo BedingfieldWojambula: Anxious Katuruza, Mashet Ndhlovu ndi

David Chikoko

Kafukufuku ndi Kuyesera Pakati pa AchinyamataAchinyamata ndi alangizi amene anatengapo mbali pakafukufuku komansontchito yoyesera bukhu la ‘Auntie Stella’ Mchichewa anachokera kumabungwe awa:

Counselling of Adolescents Youth Organization (CAYO)Foundation for Community Support (FOCUS)Hope for LifeKanengo AIDS Support Organization (KASO)Motomoto Youth OrganizationNkhotakota Youth OrganizationRestored Hope Foundation for Rural Development (REFORD)Youth Against AIDS Organization (YOGAO)Youth and Children Rights Shield (YOCRIS)Youth Net and Counselling (YONECO)Youth development and Advancement Organization (YOUDAO)

Mabungwe ena omwe anatengapo mbaliConcern UniversalSafe Schools Programme (SSP)The Story WorkshopMalawi Network of AIDS Servicing Organizations (MANASO)Zomba District AssemblyMachinga District AssemblyMinistry of Education, Science and TechnologyNational Youth Council of Malawi (NYCOM)

KUTHOKOZA KWAPADERA

Page 35: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

35

Anthu omwe athandizapo

Gift ChimbalangaFryson ChodziSmith MnenulaKossam MunthaliNdaona MuyayaChisomo ZileniRichard YohaneEdna NhdlovuEsnart NewaJennings M.M. KayiraPhilemon NdoloPanji KajaniMcGregory AlufandikaCharles SimbiBahati NyirendaVictor Mkolongo

Eunice KutsataSewenthe ChipofyaMarbel MakondetsaEdison ChikokoPatrick MakondeRuth KuwaniSalikani MvulaGertrude ChmbalangaJack PainaTalent PhiriBen WanjaMoses BushaDan MhangoChimwemwe MhangoMrs Murono

Thandizo la NdalamaNtchito yomasulira bukhu la ‘Auntie Stella’ mchichewa yatheka ndi thandizola ndalama zochokera ku mabungwe a Solon and Sida ku Sweden.

Kwa onse amene ayiwalidwa pa mndandanda wa anthu ndi mabungwe ameneathokozedwa, landirani kuthokoza kwathu.

Ofuna Kudziwa ZambiriTili okonzeka kulandira ndemanga iliyonse imene mungakhale nayoyokhudza makhadi komanso bukhu lonse la Auntie Stella.

Tikufuna kudziwa• Mmene mukuwagwiritsira ntchito thumba la Auntie Stella

• Maganizo a achinyamata pa bukhuli

• Njira zina zimene mwatsata pogwiritsa ntchito bukhuli

• Zimene mukukonda kapena simukukonda pa bukhuli

• Mmene tingalisinthire thumbali kuti likhale loyenera kwa inu.

Mukhonza kutipeza pa:Auntie StellaYouth Net and Counselling (YONECO)PO Box 471 Zomba, MalawiKazembe LocationNear Likangala Secondary School

Tel: +265 1 525 674Fax: +265 1 525 560Email: [email protected]:www.yoneco.org.mw

Page 36: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe
Page 37: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

MNDANDANDA WA MA KHADI A AUNTIE STELLA

Kodi ndingathe kugonana naye?

Kodi chokodzera changa ndichaching’ono kwambiri?

Kodi ndigonane naye mwamuna wamchemwali wanga?

Ndikusamalira munthu odwalamatenda a Edzi

Ndine mutu wa banja lathu tsopano

Ndikufuna ndidzichita zogonana ngatimmene amachitira anzanga

Ndinatengapo matenda opatsiranapogonana – Kodi sindidzabereka?

Aphunzitsi anga akufuna kutiadzigonana nane

Mnzanga ndi wamakhalidwe ogonanaamuna okhaokha

Chibwenzi changa chiri ndi mimba

Ndimakhala ndi chilakolako chofunakugonana ndi atsikana pafupipafupi

Kodi sindiyenera kugonana nayengakhale ndi mamuthandiza mu njirazosiyanasiyana?

Ndiri ndi tiziphuphu (totupa) pachokodzera changa

Mwina ndiri ndi kachilombo ka HIV

Ndikuwopa khansa ya m’chiberekero

Ndinagwiriridwapo

Kodi ndiyambe uhule kuti ndipezendalama?

Ndimatulutsa umuna ndikagona usiku

Kodi ma ARV ndi chiyani?

Akufuna kuti ndizigonana nawo.

Papita nthawi yaitali ndisanapangepiriyodi

Kodi ndimuuze kuti ndiri ndikachilombo ka HIV?

Kodi chamba chingandichotsemanyazi?

Makolo anga ndi ovuta

Kodi ndimuuze kuti ndiri ndi matendaopatsirana pogonana?

Ndiri ndi kachilombo ka HIV. Kodindimwalira?

Kodi ndiri ndi mimba?

Bwenzi langa akukwatiwa

Aphunzitsi anapereka mimba kwamnzanga

Mwamuna wanga ndiwachimasomaso

Ndimakhala ndi nkhawa popandachifukwa

Sindikumfuna mwana ameneyu

Chipembedzo changa chimaletsamakondomu

Ndimafuna kukhala mchikondi ndiakazi okha okha – kodi alipoangandikonde

Ndimamva ululu kwambiri ndikakhalakuti ndiri kumwezi (ndikusamba)

Achidya makanda anga amandizunza

Chikondi chimandilepheretsakuwerenga

Mai anga ali ndi kachilombo ka HIVndipo samabisa

Ndingathane nazo bwanji ziphuphuzanga?

Ndine oyembekezera komnso ndirindi kachilombo ka HIV

Mchimwene wanga anachitamdulidwe

Ndiri ndi zibwenzi zambiri zogonananazo

Page 38: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Mitu khumi ikuluikulu

Ubale ndi makolo komanso akuluakulu3, 10, 24, 28, 38

Kugwiritsa ntchito zithandizo zaumoyo komanso zoperekedwa mudzi mwathu:

4, 13, 14, 15, 19, 21Kuchita mgwirizano ndi athu ena po-

funa kupeza chithandizo3, 5, 8, 26, 34

Kusintha kwa malingaliro:9, 16, 17, 22, 38, 41Kuchitapo kanthu:

4, 16, 28, 29, 35Kuchita mgwirizanos:

5, 19, 20, 29, 35

1, 5, 14, 16, 23, 30

Kusintha kwa matupi athu:2,11,18,21,35,39

Kusintha kwa kaganiziridwe kathu:23,31,37

Kusangalatsidwa ndi mmene tiliri:2,6,39

14, 19, 22, 26, 40Kukhala ndi zotsatira za kachirombo ka HIV ndi

matenda a edzi:4, 5, 38, 41, 42

7, 13, 25

Chikondi ndi kugonana:1,6,12,22,30,34, 42

Mgwirizano wa pakati pa mwamuna ndi mkazi:

3,12,16,23,30,36

AuntieStella

10,27,29,32

1,11, 22, 25, 27, 33, 41, 42

Kugonana chifukwa cha umphawikapena khalidwe la mderalo

3,12,17,20Kugwiliridwa:8,16,20,29,36

10 1

2

3

56

8

47

9

Page 39: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

������������

Chichewa Question Cards

Page 40: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi ndi koyenera kuti ndigonane naye

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mtsikana wa zaka 17 ndipo ndiri ndi chibwenzi chazaka 19. Vuto langa ndi lakuti amafuna kuti ndizimuonetsachikondi mu njira imene ine sindimagwilizana nayo.Tikakumana timapyomphyonana zinthu zomwezimandisangalatsa kwambiri. Ngakhale timachita izi,sindimamulora kugonana nane. Iye amandiuza kutindikamamusiya m’malere choncho zidzamuchititsa kutiadzakhale osabereka.

Atsikana anzanga amandiuza kuti ndiyenera kuti ndizigonananaye ngati ndikufuna kuti akhalebe wanga. Ine ndikuopa kutindikapitirira kukana kugonana naye ayamba kugonana ndiatsikana ena. Kodi ndigonane naye? Iye akuti aliyense wamsinkhu wathu amachita zogonana.

Zione

©TARSC

1

QF1

Ndionetsekuti umandikonda

Page 41: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

• Kodi inuyo ndi anzanu munayamba mwakumanapo ndizimene Zione ndi chibwenzi lake akukumana nazo zakutiwina akufuna mugonane pamene wina sakufuna? Inumumachita chiyani?

• Uzani anthu awiri agulu lanu kuti wina akhale Zione ndipowina akhale bwenzi la Zione ndipo apange kasewero. Zioneauze chibwenzi chake kuti amamukonda koma sakufunakupanga zogonana. Bwenzi lake ayesetse kukambilana nayekuti alole kugonana nacho. Pamapeto pa kukambilanakuafunseni kuti anamva bwanji kukumana ndi zomwe Zionendi bwenzi lake akukumana nazo. Kodi kusagwirizanakwawoko anakuthetsa? Ngati sanagwirizane kanthu, auzenikuti abwerezenso mpaka agwirizane chimodzi.

• Kodi chibwenzi cha Zione chikunena kuti chidzakhalachosabereka ngati zione apitiriza kumamusiya m’malere.Kodi chibwenzi cha Zione chikutanthauza chiyani chikamatim’malere? Kodi ndi zinthu zina ziti zimene anyamataamanena kuti ziwachitikira ngati:

a) Atota chifukwa chogwiranagwirana ndikupyomphyonana koma osagonana chifukwa winasakufuna

b) Sakuchita zogonana?

Kodi mwa zinthu zimenezi, ndiziti zimene ziri zoona? Kodizimenezi amaneneranso atsikana?

• Kodi pali njira zina ziti zimene zibwenzi zingasangalatsanendi kumvana kukoma kupatula kugonana? Kodi inumungavomereze kuti izi zidzichitika?

ZOKAMBILANA

©TARSCQB1

Page 42: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi chokodzera changa ndichaching’ono kwambiri?

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mnyamata amene ndili pafupifupi kukwanitsa zakakhumi ndi zinayi (14) ndipo ndili ndi vuto lomwelimandizunguza. Vutoli ndi chokodzera kapena kutimaliseche anga omwe ali aang’ono kwambiri. Ndiliodandaula chifukwa sakukula monga mmene maliseche aanthu ena ndawaona amakulira ndipo ndimaona kutindidzakhala ndivuto ndikadzayamba zogonana kutsogolokuno. Choonde auntie, tandiuzani kodi chokodzera chamnyamata wa zaka khumi ndi zinayi (14) chimayenerakukhala chachikulu bwanji pakuti izi zikundisowetsamtendere.

Peter

©TARSC

2

QF2

Page 43: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

• Kodi ndi chifukwa chiyani anyamata amadandaula akakhalandi chokodzera chaching’ono? Kodi kuchepa kapena kukulakwa chokodzera cha a mwamuna ndi kofunika kwambirikwa mkazi?

• Ndi chifukwa chiyani anyamata amakhala ndi zokodzerazosiyanasiyana? Kodi zimatengera:

– zaka zawo?– maonekedwe a msinkhu kapena thupi lawo monga

kunenepa, kuonda?– Mtundu wa munthu kapena chibadwa monga muja

ena amakhalira ndi danzi ngakhale abambo awo alibedazi

– ngati anagonanako kapena ayi?– zinthu zina?

• Kodi pali msinkhu weniweni wa chokodzera cha mnyamatawa zaka khumi ndi zinayi monga peter?

• Kodi mukuganiza kuti msinkhu wa chokodzera chamwamuna chingapangitse kuti mwamunayo asachimvetsekukoma mokwanira chibwenzi chake nthawi yogonana?Kodi china chingavute chaphindu ndi chiyani?

• Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe anyamata ndi atsikanaamadandaula zokhudzana ndi matupi awo? Gawananimagulu amuna okhaokha komanso akazi okhaokha.Jambulani papepala matupi anu. Sonyezani malo a thupi lanuomwe inuyo ndi anzanu mumada nawo nkhawa kapena kutisimusangalatsidwa nawo. Kodi tingamuuze chiyani munthuamene ali ndi nkhawa zoterezi kuti nkhawa zake zithe.Kambilanani maganizo anu ndipo yesetsani kusankhazomwe zili zoposa zinzake ndipo ndichifukwa chiyani?

ZOKAMBILANA

©TARSCQB2

Page 44: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi ndigone naye mwamunawa mchemwali wanga?

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mtsikana wa zaka khumi ndi zinayi (15) ndipondimakhala ndi mchemwali wanga ndi mwamuna wake.Alamu angawa ndi ochezeka kwambiri komansoamapatsidwa ulemu ndi anthu a kwathu. Nthawi zonseamaseleulana kapena kuti kuchita nane nthabwala ndikumanena za chilamu. Posachedwapa anandiuza kutiakufuna kuti ndikagone kuchipinda kwawo, ndipo akutindiyenera kutero chifukwa ndi chikhalidwe (traditional)chathu.

Kodi ndipange chiyani? Kodi zimenezi ndizoyenera?Ndikuopa kuti akungofuna kuti agonane nane. Komandikanenanso kuti toto, andiuza kuti ndichoke pakhomopawo.

Patricia

©TARSC

3

QF3

Page 45: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB3

• Kambilanani zomwe mukudziwa za chilamu? Kodi khalidwelamdera lanulo lili ngati lomwe lili kwa Patricia? Kodichoyenera kuchitika ndi khalidwe limeneli ndi chiyani?Chimachitika kwenikweni ndi chiyani?

• ‘Lemekezani akuluakulu’-kodi mukuganiza kuti nthawi zonseana azilemekeza akuluakulu ngakhale kuti akuuzidwa kuchitazinthu zoti zingaononge moyo wawo? Kodi achinyamataangapeze kuti thandizo atakumana ndi zoterezi?

• Kodi Patricia mungamulangize kuti chiyani? Angamuthandizendi ndani?

Page 46: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndikusamalira munthu odwalamatenda a Edzi

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mtsikana wa dzaka 15 za kubadwa ndipo ndimaopakwambiri matenda a Edzi. Dzaka dziwiri zapitazo akaziamalume anga anamwalira ndipo malumewo anabwerakumadzakhala kwathu. Panopa akudwala kwambiri. Mai angaanandiuza kuti malumewa akudwala matenda a Edzi.Chifukwa cha kudwalaku, malumewa anaonda kwambirindipo nthawi zonse amakhalira kugona.

Nkhawa yanga ndi yakuti ndikuopa kuti mwina ndikhozananenso kutenga matendawa kuchokera kwa malumeangawa chifukwa timadyela nawo mbale imodzi,timagwiritsanso ntchito chimbudzi chimodzi ndiponsonthawi zambiri ndimathandiza mai anga kumawasamaliramalumewo. Chonde ndithandizeni chifukwa ndikuopa kutindikamakhala pafupi ndi malumewa, ndikumapuma mpweyaumodzi nanenso ndikhoza kutengerako matendawa. Kodiauntie ndichokepo pakhomopa?

Maria

©TARSC

4

QF4

Page 47: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB4

• Kodi mumadziwa njira zimene kachilombo ka HIVkamafalira? Lembani mndanda wa njira zimene inu ndianzanu mungatengere kachilombo ka HIV. Mukamalizaonetsetsani kuti mwakhwatcha njira zonse zimenemukuona kuti ndi zabodza. Muonetsetsenso kuti inu ndianzanu mukudziwa kusiyana kwa HIV ndi Edzi.

• Kodi Maria akulondola kunena kuti akuopa kutengakachilombo ka HIV kuchokera kwa a malume ake? Kodiiyeyu ali pa chiopsezo chachikulu bwanji?

• Kodi anzake a Maria ndi anthu ena onse amene amakhalanawo pafupi angathandizepo bwanji pa matenda a malume aMaria? Ena ndi ndani amene angathandizepo pa vutolimeneri?

• Ngati pali anthu amene akudwala matenda a Edzi m’deralanu:

a) Amasamaliridwa ndi ndani?b) Kodi amakumana ndi mavuto otani? Nanga ndi

chifukwa chiyani amakumana ndi mavuto amenewa?c) Nanga anthu amene amasamalira anthu odwala

matenda a Edzi amenewa, amakumana ndi mavutootani? Kodi ndi chifukwa chiyani amakumana ndimavuto amenewa?

d) Kodi mavuto amenewa angathe bwanji?

Page 48: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndine mutu wa banja lathutsopano!

Okondedwa Auntie Stella

Ine ndine mnyamata wa zaka 15 ndipo wamkulu m’banjalathu. Bambo athu anachoka kalekale ndipo mayi athuanamwalira ndi matenda a Edzi mmiyezi ingapo yapitayi. Paliana amuna ndi akazi anayi omwe anabadwa ine nditabadwakale ndipo onsewa ndikuyenera kumawayang’anira ndiineyo.

Mai anga mmene amamwalira sanalembe chikalatachosonyeza mmene katundu wawo angagawidwire, iwoatamwalira, choncho amalume anga anatenga katunduyense. Anangotisiyira kanyumba, tizovala ndi timapoto basi.

Nthawi zina abusa a kuchalichi amatipatsa chakudya ndiponthawi zina ndimathandiza azimayi ntchito zakumunda,koma izi sizimatikwanira. Nthawi zambiri sindigonachifukwa ndimakhala ndili ndi nkhawa kuti tikhala bwanji.Pali ana ena amene ali ndi vuto ngati langali komasitimalankhulana.

Chonde ndithandizeni auntie, pakuti vutoli likundivutamasana ndi usiku omwe.

Lovemore

©TARSC

5

QF5

Page 49: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB5

• Mukudziwapo achinyamata ena omwe ali ndi mavuto mongaamenewa?Akuchita chiyani podzithandiza okha komansomabanja awo? Akuwathandiza ndi ndani?

• Chingachitike ndi chiyani kwa ana monga amenewa m’deralanulo. Angathandizidwe ndi ndani?

• Kodi wilu ndi chiyani? Kodi anthu a m’dera lanu amalembama wilu? Chimachitika ndi chiyani ngati munthu amwaliraasanalembe wilu.

• Kodi ana ndi achinyamata amafuna chiyani kuti azipezazofunikira ndikukula mosangalala ndi mwathanzindikuyesetsa kupanga zabwino pamoyo wawo? Lembanimndandanda wake. Lembani maganizo anu kuyambira ndichoyambana kwambiri pa zonsezo.

• Kodi ndi malangizo otani mungampatse Lovemore.

Page 50: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndikufuna ndizichita zogonanangati mmene amachitira anzanga!

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mnyamata wa zaka 16 za kubadwa ndipo ndiri muform 3 pa sekondale sukulu ina yake yogonera komweko.Vuto langa ndi la kuti: Ndimadziwa atsikana ambiri komandimafuna kupeza mtsikana wa makhalidwe abwino wakutindizidzakondana naye. Anzanga onse amanena kutiamagonana ndi zibwenzi zawo ndipo inenso ndikufuna kutindizichita zimenezi.

Munthune ndikukula ndipo ndikuopa kuti ndikadzakwatiramkazi wanga azizandiseka kuti sindimatha kugonana ndimkazi

Pakadali pano ndikuganiza zokatenga mankhwala a chikondi(konda ine) kwa a sing’anga kuti atsikanawa adzindikondakwambiri.

Titus

©TARSC

6

QF6

Page 51: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB6

• Kodi pali kusiyana kotani pakati pa chikondi ndi kugonana?

• Kodi mukukhulupirira kuti anzake a Titus anayamba kalekuchita zogonana ndi zibwenzi zawo? Ngati sizoona,mukuganiza kuti ndi chifukwa chiyani akumanamizira kutiamagonana ndi zibwenzi zawo?

• Kodi ndi zinthu ziti zimene mumanamizira kuti mumachita?Kodi zimenezi ndi zothandiza kwa inu kapena kwa anzanu?

• Ndichifukwa chiyani inu ndi anzanu mumafuna kukhala ngatiamodzi ndi kumachita zinthu zofanana? Kodi ubwino wazimenezi ndi otani? Nanga kuipa kwake ndi kotani?

• Kodi ilipo nthawi ina imene simumagwirizana ndi zochita zaanzanu? Kodi inu mumawauza anzanuwo za maganizo anukapena mumangokhala chete?

• Kodi Titus apitedi kwa a sing’anga? Kodi Titusmungamulangizenso zotani?

Page 52: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndinatengapo matenda opatsirana pogonana – Kodisindizabereka?

Okondedwa Auntie Stella

Ndinathetsa chibwenzi miyezi ingapo yapitayo chifukwandinazindikira kuti chibwenzi changa chimagonananso ndiatsikana ena. Chokhumudwitsa ndi chakuti sabata latha iyeanabwera kudzandiuza kuti ali ndi ma STI kapena ndinenekuti matenda opatsirana pogonana. Iye anandiuza kutindipite kuchipatala kuti akandiyeze poopa kuti mwinaanandipatsira matendawa.

Ku chipatala atandiyeza, anandipezadi kuti ndiri ndi matendaopatsirana pogonana ndipo anamwino ( Nurse) anandiuzakuti ndiyenera kumwa mwankwala onse amene anandipatsachifukwa ngati sinditero ndikhoza kudzakhala munthuosabereka.

Izi, zikundiopsa kwambiri! Ndimalakalaka nditadzakhala ndiana ambiri ndikadzalowa m’banja. Ndimakhulupirira kuti ndibwino kungofa ngati munthu uli osabereka.

Kodi zimenezi ndi zoona Auntie? Kodi mukuganiza kutisindidzabereka? Chonde ndithandizeni maganizo.

Eda

©TARSC

7

QF7

Page 53: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

• Kodi ndi zoona kuti wa chinyamata amene wakhala ndimatenda opatsirana pogonana nthawi yaitali akhoza kudzakhalaosabereka? Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zimachititsa kutimunthu akhale osabereka?

• Kodi chingakudandaulitseni kwambiri ndi chiyani mutakhala kutimwapezeka kuti mudzakhala osabereka?

• Pamene banja likulephera kubereka mwana, kodi inumumaganiza kuti ndi chifukwa chakuti:

– Mwamuna ndi osabereka? – Mkazi ndi osabereka? – Kapena kuti onse mwamuna ndi mkazi ndi osabereka?

• Kodi mukuganiza kuti banja likhoza kukhala losangalala ngatiliribe mwana? Fotokozani mayankho anu.

• Kodi mumadziwako njira ina iriyonse imene imathandizakuchiritsa kusabereka?

ZOKAMBILANA

©TARSCQB7

Page 54: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Aphunzitsi anga akufuna kutiadzigonana nane

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mtsikana wa zaka 15 za kubadwa ndipo ndiri muform 2 pa sekondale sukulu ina yake yogonera kumweko. Aphunzitsi athu a Science abwera chaka chomwe chino.Chaka chatha tinalibe aphunzitsi a Science . Atabweraaphunzitsiwa anadzipereka kuti akhoza kumatithandizaenafe pomatiphunzitsa zina ndi zina zomwe sitidaphunzirechaka chatha, tikaweluka.

Tsiku lina titamaliza kuphunzira anandiuza kuti nditsalirekuti ndiwathandize kunyamula mabuku. Anzanga onseatapita anayamba kumandigwira mabere ndi ku malisechendi kumandiuza kuti amandikonda. Ndinachita manyazikwambiri ndipo ndinali ndi mantha akulu kuti ndiwauze kutiasiye zimene amandichitazo.

Panopa ndinasiya kumakaphunziranawo phunziroli chifukwa ndimaopa kuti mwinaakandichitanso zimenezi. Kodipamenepa nditani? Ndikuopakuti nditsalira kwambiri paphunziro limeneli.

Cecelia

©TARSC

8

QF8

Page 55: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB8

• Kodi zimenezi zinachitikirapo wina aliyense amenemumamudziwa? Kwa atsikana okha kapenanso anyamata .Kodi chinachitika ndi chiyani kwa a phunzitsi?

• Kodi Cecelia

– Asiye kudandaula chifukwa inu mukuganiza kutipalibe nkhani yodandaulitsa pamenepa?

– Akhale chete ndi kusunga chinsinsi ndiponso asiyekupita kumakaphunzira nawo phunziro la Scienceli?

– Ayenera kuulula zimenezi msanga pomuuza mnzake,kapena makolo ake, kapena aphunzitsi ake enaalionse ngakhalenso mphunzitsi wa mkulu wa pasukulupa?

– Ayenera kuulula kwa aliyense kuphatikizapo a polisikuti mphuntsitsi ameneyu amumangitse komansoamuchotse ntchito?

– Awakakamize a phunzitsi amenewa kuti amukwatire?

– Achite china chake? Ngati chiyani?

• Kodi Cecelia angachite chiyani ngati aphunzitsi amenewaatafuna kuti abwerezenso zimene anamuchitazi?

Page 56: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Mnzanga ndi wamakhalidwe ogonana amuna okhaokha (gay)

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mnyamata wa zaka 15. ndiri ndi mnzanga dzina lakemisheck yemwe ndinadziwana naye kale kale. Timakhalammudzi umodzi. Tili kalasi impodzi ndipo tonse timasewerampira limodzi.

Sabata latha iye anandiuza kuti iye ndi mmodzi wa anthuamene amachita zoganana amuna okha okha ndipo amafunakuti ineyo ndikhale mamuna wake. Izi zinandidabwitsakwambiri! Misheck amaoneka munthu wabwinobwinondipo ndi katswiri pa mpira. Zitheka bwanji kukhala munthuochita zogonana amunan okha okha?

Sindikudziwa kuti ndichite chiyani? Ndikufuna kuti akhalemnzanga chabe basi. Osati mamuna wake ayi. Ndikuopansokuti mwina tsiku lina akhoza kudzandikisa kapena kuchitachinthu china choipa. Komanso, ndikuopa kuti anthuakadziwa kuti iyeyu ndi otere, adzayambansokundiganiziranso ine ngakhale ndiri ndi chibwenzi.

Sindikufuna kuti akhalebe mnzanga. Vuto ndi lakuti tili kalasiimodzi ndipo tonse timasewera mpira limodzi. Nditanipamenepa? Ndimuulule kwa anzanga kapena makolo ake?Chonde ndithandizeni.

Samuel

©TARSC

9

QF9

Page 57: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB9

• Kodi Misheck anachita bwino kumuuza Samuel za mmeneiye aliri? Chifukwa chiyani mukuganiza choncho? Kodimukuganiza kuti misheki amamva bwanji asanamuuzeSamuel? Nanga panopa akumva bwanji atamuuza Misheki?

• Kodi inu mukuganiza bwanji za zimene Samuel akudandaula?Kodi akumvemvera chiso mnzakeyo kapena wakwiya naye?Kodi mungamulangize zotani Samuel?

• Kodi anthu ali ndi maganizo otani a anthu ameneamagonana amuna okha okha kapena akazi okha okha? Kodianthu oterewa amapatsa maina otani? Kodi zimeneamawaganizirazo ndi zabwino kapena zoipa? Koti ndi zitizimene mukuona kuti ndi zoona?

• Chitani sewero pa mitu ili munsiyi:

– Samuel auze wina aliyense za Misheck (mukhale anaikapena kupitirirapo)

– Samuel auze Misheck kuti sangathenso kukhalamnzake (anthu awiri)

– Samuel auze Misheck kuti akhalabe mnzake komaosati mwamuna wake (anthu awiri)

Pomaliza onse amene amachita masewerewa anene zimeneamamva pamene amchita sewero. Kenako kambiranani kutinjira yabwino inali iti?

Page 58: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Chibwenzi changa chiri ndi Mimba

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mnyamata wa zaka 17 zakubadwa ndipo ndiri mufomu 4. Ndine wamkulu ndithu mwakuti nditha kufunsiramtsikana ngakhale ndiri pa sukulu. Nthawi zonse bamboanga amandichenjeza kuti akadzangondiona kapenakungomva chabe kuti ndiri ndi chibwenzi adzakhala mapetoamaphunziro anga.

Nditafika pa msinkhu wokhwima ndinayamba kumakhala ndichilakolako chofuna kumakhala ndi atsikana ndipondinayamba kusamvera zimene bambo anga amandilangiza.Ndinayamba kumafunsira atsikana kuti ndizichita nawozibwenzi ndipo mmodzi wa atsikanawa ndinagonana naye.Vuto ndi lakuti mtsikana amene ndinagonana nayeyuwandiuza kuti ali ndi mimba kapena ndinene kuti ndiwoyembekezera ndipo abwera kuti adzikhala ndi ine ngatimkazi wanga. Bambo anga sindinawauze za nkhaniyichifukwa ndi kuopa kusiya maphunziro anga

Chonde Auntie ndithandizeni chifukwa nkhaniyiikundisowetsa mtendere kwambiri.

Zalimba

©TARSC

10

QF10

Page 59: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB10

• Kodi mukuganiza kuti ndi chifukwa chiyani Zalimbasanamvere malangizo a bambo ake? Kodi achinyamataamamvera malangizo a makolo awo nthawi zambiri?

• Kodi ndi chiyani chimene Zalimba ndi chibwenzi chakeangachite tsopano?

• Onani chithunzi chiri mmunsichi. Malingana ndi zimenemukuona pa chithunzi, kodi ndi zotheka kusangalala ndimoyo wako uku ukumvera malangizo amakolo? Kodi izizingatheke bwanji?

Baibulolimandiuza kuti

ndizilemekeza makolo anga komanso ndisangalale ndi

unyamata wanga koma ndizi-kumbukila kuti ndizaweluzidwa

ndi zintchito zanga

Makolo angaakundilimbikitsa kuti

ndilimbikire maphunziro ndi kuyiwala chiri chonse mpaka nditaphunzira.

Anzanga akundiuza kuti

ndisangalale ndi unyamatawanga ndi kuchita chirichonse chifukwa moyo

umabwera kamodzikokha.

Ndikungofuna kusangalala ndi moyo

wanga komanso kukhalandi udindo. Chifukwa

chiyani izi ndi-zovuta?

Page 60: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndimakhala ndi chilakolakochofuna kugonana ndi mtsikanapafupipafupi

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mnyamata wa zaka 15 zakubadwa ndipo ndiri mufomu 2 . Vuto langa ndi lakuti ndikangoona mtsikana kapenandikangoganiza za kugonana chokodzera changa chimatotakwambiri ndipo sichimaphwerapo moti ndimaopa kutianthu andiona. Ena mwa anzanga amandiuza kuti ndizibunyula kapena ndinene kuti ndizichita ka m’manja kutindithetse vutoli. Pamene azinzanga ena amandiuza kutikubunyula kukhoza kundichititsa kuti ndidzakhale osaonakapena kudzakhala osabereka. Chinanso chimenechikundisautsa maganizo ndi chakuti akuluakuluazipembedzo amanena kuti kubunyula ndi tchimo ndipoaliyense wochita zimenezi akalangidwa kumwamba

Kodi kubunyula ndi kwabwino? Ndidzakhala osangalalamukandiuza kuipa kwake ndisanayesere kubunyulaku.

Yohane

©TARSC

11

QF11

Page 61: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB11

• Kodi mukuganiza kuti anyamata ambiri amatotaakamaganiza za kugonana ndi mtsikana? Kodi mukuganizakuti akhoza kuchita chiyani kuti asamatote popeza ndichimodzi mwa zinthu zimene zimawachititsa manyazi?

• Kodi kubunyula ndi chiyani? Kodi mchimwene kapenam’longo wanu wa m’ng’ono atakufunsani kuti mumuuzekuti kubunyula ndi chiyani inu mungamufotokozere bwanji?

• Kodi Yohane mungamulangize zotani?

Mafunso: KUBUNYULA

Gwiritsani ntchito mayankho awa oyankha mafunso amene alimunsimu: Zoona; Zabodza kapena Ndikukaikira(Mayankho a mafunsowa mungawapeze pa khadi lomwe liri ndimayankho okhaokha)

1 Kubunyula kumamuchititsa munthu kuti adzifuna kumachitazogonana nthawi zonse

2 Kubunyula ndi imodzi mwa njira imene imathandiza anyamatakuthetsa chilakolako chogonana ndi mtsikana komanso ndinjira yabwino yomwe imathandiza mnyamata kulidziwa bwinothupi lake.

3 Anyamata amene amabunyula amamaliza umuna m’matupimwawo ndipo chifukwa cha ichi sangapereke mimba kwamkazi.

4 Kubunyula kukhoza kukuchititsa munthu kukhala osaberekakapena kuchita misala

5 Atsikana sangathe kubunyula

6 Kubunyula kukhoza kuchititsa kuti tsitsi limere mmanja mwako

7 Kubunyula kukhoza kukuchittisa kuti usadzathe kugonana ndimkazi wako ukadzalowa m’banja.

Page 62: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi sindiyenera kumagonananaye ngakhale ndimamuthandizamu njira zosiyanasiyana?

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mnyamata wa pa sukulu. Ndimalakalaka ndi tagonanandi chibwenzi changa koma iye amandikaniza. Komatu inendimamuthandiza pa zosoweka zake. Nthawi zinandimamugulira mphatso zosiyanasiyana koma ndikamuuzakuti tikagonane iye amakana. Anzanga amandiuza kutiatsikana ambiri sachita khalidwe losayamikali. Kodi ndichifukwa chiyani chibwenzi changachi sichifuna kumagonanandi ine ngati njira imodzi yondithokozera pa mphatsozosiyanasiyana zimene ndimamupatsa?

Themba

©TARSC

12

QF12

Page 63: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB12

• Atsikana: Kodi mumaona kuti ndi kofunika kugonana ndichibwenzi chanu akakupatsani mphatso kapena ndalama:

• Anyamata: Kodi mumayembekezera kuti chibwenzi chanuchizigonana nanu mukamachigulira zinthu?

• Kodi mukuganiza kuti ndi chifukwa chiyani chibwenzi chaThemba chikukanira kugonana naye? Kodi mungamulangizezotani Themba? Nanga mungachilangize zotani chibwenzicha Themba?

• Anthu ena amanena kuti zinthu zimene anyamata ndiatsikana amafuna akakhala pa chibwenzi ndi zosiyana. Kodianyamata amayemebekezera chiyani akakhala pa chibwenzi?Nanga atsikana amafuna chiyani akakhala pachibwenzi?

Taonani chithunzi chimene chirim’munsichi. Kodi mukuganizazotani za malingaliro kapenachikhulupiriro cha Themba?Lembani malingaliriro anu kapenachikhulupiriro chanu chokhudzakugonana, moyo wanu komansokuchita zibwenzi?

Bo magaye? Anzanga akuti ndizigonana ndimatchikiwa. Koma

mukudziwa? sindingagonane ndi tchikiiliyonse panopa chifukwa nthawi ikadalipo."Ndibwino kukhala wotetezedwa panopa

kusiyana ndi kudzadandaula patsogolo.

Page 64: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndili ndi zotupa pa chokodzerachanga!

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mnyamata wa zaka 17 za kubadwa. Vuto langa ndilakuti kutsogolo kwa chokodzera changa kukutuluka zotupa(tiziphuphu). Ndili fomu 2 ndipo aphunzitsi anatiuza kutimunthu akatuluka zotupa chonchi ndiye kuti ali ndimatenda opatsirana pogonana mosadziteteza ndiponsomunthu akhoza kupenga misala ngati salandira chithandizokuchipatala msanga. Kodi ndi zoona? Ndikuopa kupitakuchipatala chifukwa aliyense amanena kuti madokotalaamawakalipira achinyamata ngati ali ndi matenda opatsiranapogonana. Kodi nditani Auntie?

Kondwani

©TARSC

13

QF13

Page 65: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB13

• Kodi mukuganiza kuti vuto la Kondwani ndi chiyani? Kodialidi ndi matenda opatsirana pogonana? Kodimungamulangize zotani?

• Kodi ndi chifukwa chiyani anthu ena ogwira ntchitokuchipatala amakalipira achinyamata akapita kukapezachithandizo cha matenda opatsirana pogonana? Kodi titanikuti zimenezi zithe?

Mafunso: MATENDA OPATSIRANAPOGONANA

Kodi ziganizo zili mmusizi ndi zoona kapena zabodza. (Mayankhoakupezeka pakhadi la ZOCHITA)

1 Sungatenge matenda opatsirana pogonana ngatisunagonaneko ndi aliyense.

2 Matenda opatsirana pogonana akhoza kuchizika ngatiugonana ndi munthu yemwe sanagonane ndi aliyense.

3 Kugwiritsa ntchito kondomu moyenera nthawi zonse ndinjira yokhayo yopewera kutenga matenda opatsiranapogonana.

4 Matenda onse opatsirana pogonana amapweteketsa munthuukamakodza.

5 Matenda ambiri atha kuchizika ngati talandira chithandizokuchipatala mwansanga.

Page 66: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Mwina ndili ndi kachiromboka HIV

Okondedwa Auntie Stella

Ndili ndi zaka 18 za kubadwa ndipo bwenzi langa ali ndizaka 20. Takhala tikugonana kwa miyezi inayi tsopano.Poyamba tinali kugwiritsa ntchito makondomu komachibwenzi changacho sichimasangalatsidwa nazo. Patapitamiyezi iwiri, adandiuza kuti tidzikhulupilirana ndipo tisiyekugwiritsa ntchito makondomu. Zitatero ine ndidaganizazoyamba kumwa mankhwala olerera chifukwa sindimafunakutenga mimba.

Panopa ndadziwa kuti m’modzi wa zibwenzi zake zakale alindi matenda a Edzi ndipo ndikuopa kuti bwenzi langayuanatenga kachirombo ka HIV ndipo anandipatsira. Ndagwiranjakata! Ndidamvako pawailesi zoti anthu amapitakukayezetsa magazi kuti adziwe ngati ali ndi kachirombo kaHIV koma ndidamva kuti amafunsa mafunso ovutakwambiri, zotsatira zimatha kukhala zolakwika ndipo anthuena atha kudziwa zotsatira zanga.

Sindingamuuze bwenzi langayo ngakhale munthu aliyense zankhani imeneyi. Sindikudziwanso ngati ndikufunadi kudziwazotsatira zamagazi anga. Ndichite chiyani?

Auntie, chonde ndithandizeni, ndikumangokhala wodandaula.

Florence

©TARSC

14

QF14

Page 67: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB14

• Kodi zimachitika anthu pa chibwezi kuyamba kugwiritsantchito makondomu kenaka ndi kusiya? Amasiya chifukwachiyani? Kuopsya kwake ndi kotani?

• Kodi Florence achite chiyani tsopano?

– Kodi amuuze bwenzi lake zoona kutiamangodandaula ndipo ayambirenso kugwiritsantchito makondomu?

– Akayezetse mwachinsinsi osauza bwenzi lake kenakoapange chisankho payekha?

– Amuuze bwenzi lake kuti onse akayezetse?– Apitilize kugonana osadziteteza?

Fotokozani ubwino ndi kuyipa kwa chisankho chimeneFlorence angapange?

• Kodi mumadziwa zotani zokhudza kuyezetsa magazi kutimudziwe ngati muli ndi kachilombo ka HIV? Chimachitikandi chiyani kumalo oyezetsera magazi? Kodi zimatenganthawi yayitali bwanji kuti mudziwe zotsatira za kuyezetsamagazi anu?

Ukayang’anathupi langa

lokongolali, kodi ukuganiza kuti HIV

ingalowemo?

Ayi, Memo,chonde tiyeko

tipite tikayezetse magazisiti-kudziwa zakachilombo

ka HIV

Page 68: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndikuwopa khansa yam’chiberekero!

Okondedwa Auntie Stella

Ndili ndi zaka 15 za kubadwa ndipo ndiri ndi nkhawapazimene ndinamvapo. Azakhali anga anandiuzako za mzawoyemwe akudwala kwambiri yemwe akuti ali ndi khansa yam’chiberekero ndipo ndinamva kuti nthendayi ikhoza kuphamzimayi.

Ndinali ndisanamvepo za matendawa ndipo ndili ndinkhawa. Kodi anthu amatenga bwanji nthenda imeneyi?Kodi eti ndi zoona kuti itha kupha munthu?

Lusibiro

©TARSC

15

QF15

Page 69: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB15

• Kodi munamvapo za khansa ya m’chiberekero?

• Kodi mukudziwa kuti imayamba bwanji?

• Kodi mukudziwa kuti ndi anthu ochuluka bwanji amene alinayo kuno ku Malawi?

• Kodi atsikana ndi amai achite chiyani kuti ayipewe?

• Kodi itha kuchiritsika?

Page 70: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndinagwiriridwapo

Okondedwa Auntie Stella

Ndikusowa mtendere ndipo sindikudziwa kuti ndiuze ndani!Ndine mwana, pamodzi ndi azing’ono anga, amalume angaamatikonda kwambiri ndiponso ankatipatsa mphatso. Komachaka chathachi, pamene ndinakwanitsa zaka 12, anayambakumanditsatira kudambo kumene timakatunga madzi ndipoamandigwira mabele ndi kumaliseche. Ndinali ndi manthakwambiri koma ankandiuza kuti zimenezi tidziwe anthuawiri basi ndipo ndikaulura, tonse zitivuta.

Sabata yathayi anabwera kumaliro ndipo madzulo ake anthuanali kumwa mowa. Kutada usiku, ndikuchokera kukakodza,anandidikilira panjira. Anandigwira, kundikankhira pansindipo anandigona. Ndinamva kuwawa kwambiri komandikati ndilire amandimenya.

Atatha anandiuza kuti linali vuto langa chifukwa ndinatulukakupita kukakodza nditangovala kamisolo yokha opandazovala zina ndiye zinawapangitsa kuti akhale ndi chilakolakochogonana nane.

Auntie, chonde ndithandizeni. Zikundipweteka ndipondikungoona ngati zaumve zimene zandichitikirazo.Ndikumangokumbukirabe zimene andichita amalume.Ndikuopa kuuza makolo anga chifukwa ndikuganiza kutiandikalipira chifukwa chakuti amalumewo amatithandiza ndichakudya ndi ndalama kwathu. Koma nangaakadzandigwililiranso? Ndikuopa, auntie! Ndichite chiyani?

Regina

©TARSC

16

QF16

Page 71: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB16

• Kodi kugwililira ndi chiyani? Kodi mchitidwe umenewu ndiochuluka bwanji m’dera lanu? Kodi anthu ameneamagwililira amakhala achilendo kapena owadziwa? Kodiamakhala am’banja mwathu momwemo?

• Kodi mu nkhani tawerengayi, amene analakwitsa ndi ndani?Ndi chifukwa chiyani a malume a Regina anachita zimenezi?

• Kodi tingamunene mtsikana kapena mzimayi kuti ndiolakwapamene wagwiliridwa chifukwa chakuti anavala zovalazochititsa amuna kukhala ndi chilakolako chogonana ndimkazi ? Chitani mtsutso pa nkhani imeneyi.

• Kodi Regina mungamulangize kuti chiyani?

• Kodi inu mutagwiliridwa mungachite chiyani? (anyamata ndiatsikana onse ayankhe). Mungakanene kupolisi? Kodiubwino ndi kuipa koulula ngati wagwiliridwa ndi chiyani?

Chetechetesautsa nyama

koma suyo suyo

Page 72: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi ndiyambe kuchita uhulekuti ndipeze ndalama?

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mtsikana wa zaka 19 za kubadwa ndipo ndili Form 4. Makolo anga adamwalira ndipo ndikukhala ndi agogo angaamene sangakwanitse kundilipilira ndalama zakusukulu.Amalume anga ankanditumizira ndalama koma chakachathachi, nawonso adamwalira ndipo ndilibenso winayemwe angandithandize. Ndikufunitsitsa nditamaliza sukuluyanga ndikupeza ntchito koma ndilibe munthu ameneangandithandize. Ngakhale kuti ndilembe mayeso,pakufunika ndalama zambiri kotero kuti sindingakwanitse.

Kodi ndi bwino kuti ndiyambe kugonana ndi amuna kutindizipeza ndalama pakuti sindikuonanso njira yina yakutindidzilipilire sukulu kuti ndimalize maphunziro anga?Kwathu kuno kuli azibambo ambiri amene akhozakundilipilira sukulu koma pokhapokha nditagonana nawo.Koma izi zikundiopsa chifukwa mzanga wina wake yemweamagonana ndi azibambowa adandiuza kuti nthawi zinaamakana kulipira ndalama yokwanira ndipo nthawi zinansoamamumenya. Chonde, auntie, ndithandizeni.

Janet

©TARSC

17

QF17

Page 73: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB17

• Khalani awiriawiri. Wina akhale Janet, ndipo wina akhalemzibambo yemwe akufuna kumulipira Janet kuti agonanenaye. (Mwina Janet akufuna agwiritse ntchito kondomu,koma mzibamboyo akukana)

a) Kambiranani. b) Kenaka auzeni anzanu zimene mwakambiranac) Muwauzenso mmene mumamvela nthawi imene

mumapanga kaseweroka.d) Pomaliza, kambiranani kuti mwaphunzirapo chiyani

pazokambiranazi.

• Jambulani chithunzi ngati chiri mmunsichi kuti muonetseubwino ndi kuipa kogonana kuti mupeze ndalamamakamaka kwa munthu yemwe ali ndi mavuto ngati a Janet.Kodi ndikoyenera kupeza ndalama munjira imeneyi?

• Kodi Janet atakhala kuti akuchokera kudera lanu, achitechiyani kuti apeze ndalama zolipilira sukulu ndi mayeso ake?

UBWINO KUIPA

UHULE

kuthandizirapakhomo

kupezandalama

kulipilirasukulu

kupezantchito kupwetekedwa/

kugwililiridwa

kutengamimba

kusakondedwa/ kusapatsidwa

ulemu

kutengaHIV

kudwala

Page 74: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndimatulutsa umuna ndikagonausiku

Okondedwa Auntie Stella

Ndili ndi zaka 15 za kubadwa ndipo ndili ndivuto limenendikukhulupilira kuti inu mukhoza kundithandiza mosavuta.Sindinagonanepo ndi mtsikana aliyense koma ndimalotalotandi kugonana ndi atsikana ndikagona usiku. Ndikadzukam’mawa ndimapeza pogona panga panyowa nditimadzitomata toyera timene timatuluka kuchokera ku chokodzerachanga ndiri mtulo. Izitu zimachitika ngakhalasindikuganizako zogonana.

Ndikuopa kuti ndikadzakwatira, izi zitha kudzaonongaubwenzi wathu ndi mkazi wanga chifukwa zimachitikakatatu kapena kanayi pasabata iliyonse. Sindikupezamtendere mumtima chifukwa chavutoli ndipo sindikudziwakuti ndingathane nalo bwanji.

Kodi ndiye kuti mwina ndili ndivuto ndi thupi langa kapenaolakwa ndine kuti ndimangolotalota maloto ngati amenewa?

Edison

©TARSC

18

QF18

Page 75: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB18

• Kodi mukudziwa ngati izi zimawachitikira anyamatakawirikawiri?

• Kodi mukuganiza kuti zimayambitsa maloto amenewa ndichiyani?

• Kodi mukuganiza kuti maloto amenewa akutanthauzakuti….

– Edison ali bwinobwino?– Edison apite kuchipatala?– Edison agonane ndi mtsikana kuopa kuti angadwale?

• Kodi Edison adzidzakhalabe ndi maloto amenewaakadzakwatira kapena akadzayamba kuchita zogonana?

Ndizichotseletuizi anthu

asanadzione

Page 76: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi ma ARV ndi chiyani?

Okondedwa Auntie Stella

Ndili ndi zaka 19 za kubadwa ndipo ndili ndi mwanawamkazi m’modzi yemwe ali ndi zaka zitatu. Bwenzi langaanali wamkulu kuposa ine ndipo chibwenzi chinatha. Panopaakudwala Edzi.N dimakhala kumudzi ndi agogo anga akazi.Timalima chimanga ndipo timakolola bwino kukakhalamvula yokwanira. Ndimagulitsanso matemba koma ndalamazimene ndimapeza ndizosakwanira.

Miyezi yapitayo, azakhali anga adapita nane ku chipatalakukandiyezetsa ngati ndili ndi kachilombo ka HIV ndipo ndipamene ndinadziwa kuti ndili ndi kachilomboka

Mzimayi wina kumpingo kwathu adandiuza kuti kulimakhwala ena otchedwa ma ARV ndipo atha kundithandizakupezako bwino koma vuto ndi lakuti, amadula kwambiri.

Komabe ine ndikufunitsitsa mankhwala amenewa. Vuto langandi lakuti sindikudziwa kumene ndingakawapezemankhwalawa. Kuonjera apo, ndiribe munthu wina aliyenseamene angadzandilerere mwana wanga ine nditamwalirachifukwa agogo anga akalamba komanso amadwaladwala.Ndikufunitsitsa mwana wanga atapita ndikumaliza sukulukuti asadzavutike m’moyo wake.

Ngati alipo malo amene ndingapeze mankhwalawa, chondeauntie, ndiuzeni.

Thandi

©TARSC

19

QF19

Page 77: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB19

• Kambiranani zimene mukudziwa zokhudza ma ARV. Kodipali uthenga okwanira okhudzana ndi ma ARV?

• Ngati palibe uthenga okwanira, ndi chifukwa chiyani? Inumungatani kuti mudziwe zambiri.

• Kambiranani za malo kumene mungapezeko chithandizocha mankhwala a ma ARVs

• Ngati ma ARV ndi osowa, Thandi achite chiyani kutiakhalebe ndi moyo wathanzi?

Ma ARV amatipatsa chiyembekezo!

Page 78: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Akufuna kuti ndizigonana nawo

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mnyamata wa zaka 15 ndipo ndinapeza malo ogonapafupi ndi sukulu yimene ndimaphunzira. Makolo angaamagwira ntchito ku esiteti ya mzunguwina ndipo ndikutalindi kusukulu kumene ndili. Nthawi zina makolo angaamachedwa kunditumizira ndalama zakuti ndilipire rentindipo akazi awo a eni ake nyumba yimene ndikugonaamabwera mnyumba mwangamo ndikumandiuza kutindigonane nawo ndipo ndikatero sindiripira renti mweziumenewo. Ndimaopa kuti ndikawakanira akhozakunditulutsa mnyumbamo ndipo kulibe kwina kwakutindikhoza kupita. Pakadali pano, ndimanamizira tizifukwatosiyanasiyana kuti atuluke mnyumba mwangamo asanafikepachimake pakuti agonane nane. Ndikusowa munthu wakutindimuuze za nkhaniyi ndipo sindikudziwa chakuti ndichite.A eni nyumba, amene ndi amuna awo, akhoza kundinenaatawapeza akazi awo ali mnyumba mwanga.

Patrick

©TARSC

20

QF20

Page 79: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB20

• Kodi mukuganiza kuti anyamata akhoza kugwililiridwa? Ndindani yemwe angawagwililire, amuna kapena akazi?

• Kodi anthu amati chiyani za anyamata amene agwiliridwa?Kodi zimakhala zosiyana ndi zimene amanena akagwiriridwamtsikana?

• Kodi pali kusiyana pakati pa kugwilira ndi kugonana ndimwana ?

• Kodi Patrick auzeni ndani za nkhani imeneyi? Nangaapangenso chiyani?

• Kodi makolo a Patrick angathandize bwanji?

Page 80: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Papita nthawi yaitali ndisanapange msambo

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mtsikana wa zaka 15 za kubadwa ndipo ndinayambakusamba (kupanga piriyodi) ndili ndi zaka 13. Vuto ndi lakuti,miyezi inayi yapitayi, sindinapange msambo. Sindinagonanekondi mwamuna ndipo ndilibe chibwenzi. Anzanga ena akutindine wosabereka, eti ndi zoona? Kodi ndili ndi vutolililonse pamenepa? Chonde, azakhali, ndili ndi nkhawa kutimwina sindidzabereka.

Irene

©TARSC

21

QF21

Page 81: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB21

• Kodi atsikana ambiri amene mukuwadziwa inu amasambakapena kupanga piriyodi kangati pamwezi?

ATSIKANA: Auzeni anzanu zokhudza msambo wanu!

ANYAMATA: Auzeni anzanu zimene mukudziwa zokhudzamsambo!

Pelekani zifukwa zimene atsikana ena amapezeka kutiakupitilira miyezi ingapo osasamba ngati Irene?

• Kodi ndi zoona kuti ngati mtsikana sanasambe ndiye kutindi osabereka?

• Kodi m’dera lanu muli zikhulupiliro zanji zokhudzana ndiachinyamata pa nkhani zogonana, mimba ndi nkhani zinazokhudzana ndi zimenezi? Mwachitsanzo, anthu enaamakhulupilira kuti ngati mtsikana akusamba kawiripamwezi ndiye kuti adzabereka mapasa. Enansoamakhulupilira kuti mnyamata akakhala ndi tsitsi pankhopeyake ndiye kuti anachitapo zogonana. Enansoamakhulupirira kuti kugonana ndi mkazi pamene akusambakapena akuchita piriyodi akhoza kukupha kapena ukhozakudwala kwambiri.

• Lembani zikhulupiliro zonse zimene mukuzidziwa ndipomunene kuti ndi ziti zimene mukugwirizana nazo ndipo ndiziti zimene mukutsutsana nazo.

Page 82: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi ndimuuze kuti ndili ndikachirombo ka HIV?

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mtsikana wa zaka 19 za kubadwa ndipo chaka chathandinapezeka kuti ndili ndi kachirombo ka HIV. Nditamvasindinakhulupilire ndipo ndinali wamantha koma nditamuuzamkulu wanga anandithandiza kuwafotokozera amai anga.Sitiulula kwa anthu ena za nkhaniyi. Sindinayambe kudwalandipo ndimagwirabe ntchito yanga yosoka bwinobwino.

Ndinayamba kuyimba kwaya ya kumpingo kwathu ndipokumeneko ndinakumana ndi mnyamata wina dzina lakeGobede yemwe anandifunsira kuti tikhale pa chibwenzi.Koma vuto ndi lakuti, sindikufuna kumuuza kuti ndili ndikachirombo ka HIV poopa kuti andisiya sitikhalanso pachibwenzi ndipo mwina akhoza kuuza anthu ena. Izi mwinazikhoza kuchititsa anthu ena kusiya kumadzasoketsa zovalazawo kwa ine.

Kodi nditha kukhala ndi chibwenzi? Kumalo kumenetimakumana anthu amene tili ndi HIV amatilangiza kutipalibe chovuta kugonana koma tiyenera kugwiritsa ntchitomakondomu. Kodi ndidikire kudzapeza mnyamata yemwenayenso ali ndi kachilombo ka HIV poganizira kuti mwinaiye angadzamvetse vuto langa?

Vuto langa ndi limeneli: ndimuvomere Gobede? Nangandikamuvomera, ndimuuze kuti ndili ndi HIV tisanakhale pachibwenzi? Chonde azakhali, ndithandizeni.

Emily

©TARSC

22

QF22

Page 83: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB22

• Mungagule kapena kusoketsa malaya anu kwa munthuyemwe ali ndi kachilombo ka HIV? Chifukwa chiyani? Kodimumadziwa bwino mmene kachilombo ka HIV kamafalikira?

• M’maganizo mwanu, ndi achinyamata angati ameneamagonana osadziwa ngati wina ali ndi HIV kapena ayi?Kodi kugonana ndi munthu yemwe simukudziwa ngati alindi kachirombo ka HIV ndi koopsya bwanji kapena ndikosaopsya bwanji?

• Kodi palibe chovuta Emily kugonana ndi Gobede ngatiGobede alibe HIV? Pali kuopsya kwina kulikonse?Angapewe bwanji kuopsya kumeneku?

• Kodi ndi zotheka kuti mwina Gobede nayenso ali ndi HIV?Ngati ndi choncho, apange chiyani awiriwa?

• Nanga Emily aulure liti kwa Gobede kuti ali ndi HIV?

– Asaulure– Asanayambe kugonana– Pokhapokha Gobede atafunsa– Akadziwana kwambiri – Pokhapokha atafuna kukhala ndi ana

Pelekani zifukwa pamayankho anu onse.

Kodi payankho lililonse laperekedwa m’mwambalo, chimenechingachitike ndi chiyani? Ganizirani chabwino ndi choipachimene chingachitike.

Page 84: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi chamba chingandichotsemanyazi?

Okondedwa Auntie Stella

Ndili ndi zaka 16 za kubadwa ndipo ndili Form 3. Ndili ndivuto lalikulu chifukwa ndimachita manyazi ndi atsikana.Nthawi zina ndimachita manyazi ngakhale kuwayang’ana.Anzanga amandiuza kuti nditasuta chamba, manyazi akhozakuchoka ndipo nditha kumawalankhulitsa atsikana. Anzangaonse ali ndi zibwenzi ndipo ndimaziona otsalira pakati paanzanga. Ndimafuna nanenso nditakhala ndi chibwenzi komasindimafuna kusuta chamba. Kodi ndingatani?

Jack

©TARSC

23

QF23

Page 85: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB23

• Kodi manyazi ndi vuto lalikulu pakati pa achinyamataachichepere? Kodi vutoli ndilalikulu pakati pa anyamatakapena atsikana?

• Kodi anthu ambiri amene mukuwadziwa inu, amafunaatakhala ndi chibwenzi chifukwa chakuti anzawo ali ndichibwenzi? Kodi ichi ndi chifukwa choyenera chokhalira ndichibwenzi?

• Kodi chamba chingamuthandize Jack? Pelekani chifukwa payankho lanu? Nanga kumwa mowa kapena kumwamankhwala ozunguza bongo, kukhoza kumuthandiza Jack?

• Kodi Jack mungamulangize chiyani

a) Kumbali yochotsa manyazi? b) Kumbali yopanga ubwenzi ndi atsikana?c) Kumbali yosuta chamba?d) Kumbali yokhala ndi chibwenzi pa msinkhu wake?

Page 86: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Makolo anga ndi ovuta

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mnyamata wa zaka 18 za kubadwa ndipo vuto langandilakuti makolo anga akundiuza chilichonse chimenendiyenera kuchita. Amandisankhira anzanga ocheza nawondipo amandiopsyeza zogonana ndikadali wamng’ono.Amachita kundiuza kuti ichi nditha kuchita ndipo ichi ayisindiyenera kuchita. Zimenezi zimandilepheretsa inekuwafunsa mafunso kapena kuwafotokozera mavuto amenendili nawo. Amalume anga amakhala kutali kotero kutindilibenso munthu wina wamkulu yemwe ndingapite kutiandilangize kapena ndimufunse mafunso. Kodi nditani?

Davie

©TARSC

24

QF24

Kuwona masoankhono ndi

kudekha (sungakhosi mkanda

woyera udzavala)

Page 87: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB24

• Kodi achinyamata ambiri amakangana ndi makolo awokapena amagwirizana nawo?

• Nanga inu, makolo anu mumagwirizana nawo kapenamumakangana nawo?

– Kodi ndi kwapafupi kukambirana ndi makolo anu?– Kodi pali mavuto otani pakati pamakolo anu ndi inu?– Kodi amene mumagwirizana nawo ndi ndani pakati

pa amayi anu ndi atate anu?

• Kodi makolo anu amakuthandizani moyenera? Kodimukuganiza kuti ndi chifukwa chiyani makolo anuamakuthandizani mmene mwafotokozera? Kodi anyamataamawathandiza mosiyana ndi atsikana? Ngati ndi choncho,inu mukuganiza kuti ndi chifukwa chiyani?

• Kodi mungapereke malangizo otani kwa achinyamataanzanu kuti azimvana ndi makolo awo?

• Kodi kupatula makolo anu, pali akuluakulu ena amenemukhoza kumasuka nawo? Ndi ndani? Ndi chifukwa chiyanimumamasuka nawo?

Page 88: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi ndimuuze kuti ndili ndi matenda opatsirana pogonana?

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mnyamata wazaka 17 ndipo ndili pa sukulu. Ndili ndichibwenzi ndipo tinayamba kugonana miyezi ingapoyapitayo. Nthawi ya tchuthi chapitacho ndinapita kukachezakwa amalume anga ku Blantyre ndipo kumenekondinakumana ndi mtsikana wina panja pamalo omweramowa. Titakambirana tinagwirizana zogonana ndipotinagonana kamodzi kokha. Nditabwelera kumudzindinazindikira kuti ndili ndi matenda opatsirana pogonana.

Kusukulu aphunzitsi anatiuza kuti tidziuza bwenzi lathungati tili ndi matendawa. Zimenezi ndinayambandawerengakonso m’malo ambiri. Koma ndi chifukwachiyani ndiyenera kumuuza bwenzi langayo? Ndikuopa kutiakhoza kundikwiyira. Kodi sangadziwe pamene tikugonanakuti ndili ndi matendawa ngati sindimuuza? Sindikufunabwenzi langa andisiye. Kodi nditani?

Alex

©TARSC

25

QF25

Page 89: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB25

• Kodi Alex amuuze bwenzi lake za matenda amene ali nawo?Kodi chingachitike ndi chiyani atapanda kumuuza? Nangaatamuuza?

• Alex akanakhala chibwenzi chako, iwe ukanafuna kutiapange chiyani?

• Kodi mungamve bwanji bwenzi lanu atagonana ndi mtsikanakapena mnyamata wina? Mungapange chiyani?

• Kodi matenda opatsirana pogonana ndi ochuluka pakati paachinyamata amene mukuwadziwa inu? Kodi chimayambitsamatendawa ndi chiyani? Kodi matendawa atha kupewedwa?Mungatani kuti muwapewe?

• Kodi mungadziwe kuti munthu ali ndi matenda opatsiranapogonana? Ndi zizindikiro ziti zimene mukuzidziwa inuzimene zimaoneka pakati pa akazi? Nanga pakati pa amuna?

Kodindimuuze?

Page 90: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndili ndi kachirombo ka HIV.Kodi ndimwalira?

Okondedwa Auntie Stella

Ndili ndi zaka 18 za kubadwa ndipo ndimagulitsa ndiwozamasamba kumsika wapafupi ndi kwathu. Masiku apitawandinapita kukayezetsa ngati ndili ndi kachirombo ka HIVndipo ndinapezeka kuti ndili nako. Ndimakhala ndi azakhalianga chifukwa amayi anga anamwalira ndipo abambo angaanachoka ndili wamng’ono kwambiri. Ndili ndi manyazi kutindiwauze azakhali anga, anzanga komanso aliyensekumsikako chifukwa amakonda kuwanyoza anthu amene alindi Edzi. Ndikuopanso kuti azakhali anga akwiya kwambiri.

Sindikukumbukira zimene anandilangiza mlangizi pazamatenda a Edzi nditapita kukayezetsa magazi. Ndingatanikodi? Pali zakudya zapadera zimene ndiyenera kudya? Kodikuli magulu a anthu amene ali ndi HIV okhaokha?Ndikuphunzira luso la ulimi wa njuchi. Kodi ndipitirizekapena ndingosiya ndizingodikira kuti ndife?

Sindikudwala ayi koma ndimangodandaula kotero kutindimalephera kudya kapena kugona bwinobwino.Ndikungoona ngati ndafika pamathero a moyo wanga.Ndikadakonda nditakhala ndi moyo monga amakhalira winaaliyense, kupeza wa chikondi, kukhala ndi ana, ndi zinazotero koma zonsezi sizingatheke tsopano. Penandimaganiza kuti ndi bwino kungodzipha kusiyanandikudikira kuti ndidzafe ndi Edzi. Auntie, chondethandizeni, palibenso wina amene ndingamuuze.

Charity

©TARSC

26

QF26

Page 91: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB26

• Kodi kusiyana kwa HIV ndi Edzi ndi chiyani?

• Kodi m’dera limene mumachokera, kuli anthu ambiri ameneali ndi HIV kapena Edzi? Kodi amakamba mosabisa kuti alindi Edzi? Chifukwa chiyani amakamba? Chifukwa chiyanisamakamba?

• Mutapezeka lero kuti muli ndi HIV, chimene mungaopekwambiri ndi chiyani?

• Kodi Charity azingodikira kufa kapena pali njira zina zimeneangachite kuti akhale ndi moyo wabwino? Mungamuyankhemotani funso lake lokhala ndi moyo monga amakhalira winaaliyense koma ali ndi HIV?

• Lembani mndandanda wa zinthu zimene anthu amanena zaanthu amene ali ndi HIV kapena Edzi. Zigaweni muzigawoziwiri: zolimbikitsa ndi zokhumudwitsa. Kodi ndi ziti zimenezili zambiri? Mukuganiza kuti ndi chifukwa chiyani zilichonchi?

Page 92: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi ndiri ndi mimba?

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mtsikana wa zaka 16 za kubadwa ndipo ndakhalandiri pa chibwenzi ndi mnyamata kwa miyezi inayi tsopano.Nthawi zonse amalimbikira zakuti tigonane koma inendimakana. Koma tsiku lina, tinagonana ndipo sindinamvekukoma ngakhale pang’ono. Izi zachitika miyezi iwiriyapitayo. Chichitikireni izi sindinapange msambo. Komatutinagonana kamodzi kokha ndipo sitinagwiritse ntchitokondomu. Anzanga akuti sindingatenge mimba pogonanakamodzi kokha, eti ndi zoona?

Ndinamvakonso anzanga akunena za mankhwala amenemunthu umamwa mmawa mwatsiku limene wagonana kutimunthu usatenge mimba ngati wagonana mwangozi kapenawakakamizidwa. Kodi nditha kumwa mankhwalawo panopakapena ndachedwa? Sindikufuna kuchotsa mimba ayi. Ndizoopsya!

Chonde ndithandizenindikusowa chochita.

Doreen

©TARSC

27

QF27

Page 93: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB27

Mafunso: OKHUDZA KUTENGA MIMBA

Tchulani ziganizo zimene zili zoona ndipo zina zimene sizoona:(Mayankho ali komalizira kwa khadi lino)

1 Mtsikana sangatenge mimba pamene akugonana koyamba 2 Sungatenge mimba pamene mukugonana choimilira3 Sungatenge mimba ngati mwamuna atulutsa chokodzera

asanathire umuna 4 Sungatenge mimba ngati utsuka maliseche kapena kukodza

utangotha kugonana5 Mtsikana sangatenge mimba ngati sanayambe kusamba 6 Sungatenge mimba ngati mnyamata ali ndi zaka zochepera 15

• Kodi mumadziwa mmene mungapewere kutenga mimba?Yankhani mafunso ali mmusiwa.

• Kodi munamvako za mankhwala amene munthu akhozakumwa m’mawa mwa tsiku limene mwagonana?Pachingerezi amatchedwa morning after pill.. Kodi ntchitoya mankhwala amenewa ndi chiyani? Kodi mukhozakuwapeza kuti?

• Lembani zinthu zimene anyamata amanena powanyengeleraatsikana kuti agonane nawo. Lembani mayankho ake. Kodiamene angakane motsimikizadi kuti sakufuna zogonana ndindani? Chimene chingakuthandizeni kukana ndi chiyani?

Ziganizo zonse zimene zapelekedwa pamwambapo ndi zabodza. Tetezani bwenzi lanu kusatenga mimba.

Page 94: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Bwenzi langa akukwatiwa

Okondedwa Auntie Stella

Ndine m’nyamata wa chisodzera, ndipo ndili pa ubwenzi ndimtsikana wotchedwa Suzeni. Tonse timalimbikiramaphunziro, ndipo tinagwirizana zodzakwatiranatikadzamaliza maphunziro athu a fomu 4. Vuto lathu ndilakuti makolo a bwenzi langalo akuyendetsanso zakuti iyeakwatiwe ndi munthu wina. Iye adawauza kuti akufunakukwatiwa ndi ine, koma iwo adamuuza kuti akuyenerakutsata zomwe makolo akewo adanena.

Kodi pamenepa titani? Iye akapitiliza kusamvera za makoloakezo adzamuuza kuti si mwana wawonso. Mwamunayemwe akuti akwatiwe nayeyo ngwachikulire komansowachuma zedi. Ndikudziwa kuti makolowo akufuna kutiSuzeni akwatiwe ndi mwamunayo chifukwa cha chumachimene ali nachochi. Pakali pano ayamba kale kukambiranazakuti apereka ndalama zingati za malowolo.

Kodi azakhali, makolo ndi ololedwa kukakamiza mwanawawo wa mkazi kukwatiwa ndi mwamuna yemwe iyesakumufuna? Tithandizeni azakhali.

Joshua

©TARSC

28

QF28

Page 95: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB28

• Kodi pachikhalidwe chanu , pamakhalanso mabanja ochitakukonzeredwa? Kodi zimakhala ngati zimene akumuchitiraSuzenizi kapena zimakhala zosiyana?

• Anthu ena amaganiza kuti kulowola kumakulitsa ubalepakati pa mbali ziwiri,(kuchimuna ndi kuchikazi), ena amatikumaphwanya ufulu wa munthu wa mayi, pamene ena amatimasiku ano kulowola kwangolowa bizinezi. Nanga inumukuti chiyani?

• Fotokozani ubwino ndi kuyipa kwa:

a) Mabanja ochita kukonzeredwa.b) Mabanja omwe eni ake achita kusankhana okha.

• Kodi Joshua ndi Suzeni angachitepo kanthu kuti Suzeniasakhale pa banja lomwe sakulifuna? Kambilanani njirazomwe angatsate, ndipo pambuyo pake kambilanani njirayomwe ndi yabwino koposa.

• Inuyo mungamve bwanji makolo anu atakukonzerani ukwatiomwe simumafuna?( Apa anyamata ayankhe, atsikanansoayankhe)

Page 96: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Aphunzitsi anapeleka mimbakwa mnzanga

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mtsikana wa zaka 17, ndipo ndikulemba mayeso a fomu4 chaka chino. Mnzanga weniweni dzina lake Loveness wazaka16, tinali kalasi imodzi, mpaka mwezi wathawu. Mchigawochotsiliza cha sukulu, mphunzitsi wathu wa masamu anamuuzakuti azimuphunzitsa mwa padera, popeza sankakhoza bwinomasamu. Koma atamuphunzitsa kwa masiku ochepa,mphunzitsiyo anamufunsira chibwenzi. Iye analephera kukanachifukwa anali mphunzitsi wake kotero kuti sanafunekumuonetsa ngati woyipa. Atatenga mimba, Lovenessanathamangitsidwa sukulu, pamene aphunzitsiwosanapatsidwe chilango chilichonse.

Ine ndi anzanga tikuona kuti nkhaniyi siyinayende mwachilungamo. Ndichifukwa chiyani mphunzitsiyu sanalandirechilanago chifukwa chopereka mimba kwa mwana? Panopatikukambirana ndi anzanga, chifukwa tikuona kutimphunzitsiyu ndiye olakwa kwambiri. Tikufuna kutimphunzitsiyu alangidwe, ndipo Loveness aloledwe kubwerakudzalemba mayeso ake. Panopo tikuganiza kuti tikapelekenkhaniyi kwa sukulu komiti.

Anthu ena akuganiza kuti ife sitikuyenera kuchitapo kanthupankhaniyi, popeza akulu akulu oyendetsa sukulu ino pamodzindi makolo ndiamene awone zoti achitenaye mphunzitsiyu.Koma nanga ngati sachitapo kanthu? Ife tikuganiza kutitikuchita zinthu zolondola, koma anthu ena akuti zimenezizisatikhudze. Nanga inu azakhali mukuti bwanji?

Cynthia

©TARSC

29

QF29

Page 97: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB29

• Kodi mukuganiza kuti maganizo a Cynthia ndi anzake ndiolondola? Chifukwa chiyani?

• Mukuganiza bwanji za maganizo awo ofuna kuchitamsonkhano? Kodi mukuganiza kuti njira imeneyi ithandizapa vutoli? Fotokozerani maganizo anu

• Kodi chikalata cha dandaulo ndi chiyani? Kodi kulembachikalata cha dandaulo kungamuthandize bwanji Loveness?

• Kodi kwanuko chimachitika ndi chiyani, mtsikana wapasukulu akapatsidwa mimba? Kodi angathe kupitilizamaphunziro ake? Nanga mwamuna wopeleka mimbayo,zimamukhudza bwanji?

FORM FOUR EXAMINATIIONMaths Paper I

Page 98: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Mwamuna wanga ndi wachimasomaso

Okondedwa Auntie Stella

Ndinakwatiwa zaka ziwiri zapitazo ndiri ndi zaka 19 zakubadwa. Nthawi imeneyo tinali pachikondi kwambiri ndipopanopa tiri ndi mwana wokongola ndithu. Ndisanakwatiwendinali ndisanagonanepo ndi munthu wina aliyense kupatulamwamuna yemwe anandikwatira, Charles. Koma kuyambiramiyezi 6 yapitayo iye anayamba kubwera kunyumbamochedwa. Akamabwera chonchi amandinamiza kutiamachokera ku ntchito, koma ine ndimadziwa kutiakuchokera ku chibwenzi. Ine ndimaopa kwambiri matendaopatsirana pogonana ndipo tsiku lina ndinamuwuza kutiagwiritse ntchito kondomu ngati akufuna kugonana nane. Iyeanakwiya kwambiri ndikumandiuza kuti sindikumukhulupirira

Kenaka, ndinadziwa kuti amayenda ndi mkazi wina ameneamakhala chapafupi ndipo nditamufunsa mwamuna wanga zaizi, iye anavomeradi kuti chinali chibwenzi chake.Anandiuzanso kuti athetsa chibwenzi chimenechi chifukwaamandikonda. Koma nditamuuza kuti sindidzagonana nayensopokhapokha atakayezetsa magazi kuti adziwe ngati ali ndikachilombo ka HIV, iye anakana ati chifukwa sakufuna kutiadziwe.

Izi zakhala zikuchitika kwa mwezi umodzi tsopano. Nthawizambiri ndimamuuza kuti akagone m’khichini ngakhale iyeamadana nazo zimenezi. Koma ine ndingatani azakhali.Mwamunayu ndimamukondabe. Koma ndikuopa kuti mwinaakhoza kundipatsira kachilombo ka HIV. Mwina ndinalakwitsakukwatiwa ndikanali wa mng’ono msinkhu.

Josephine

©TARSC

30

QF30

Page 99: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB30

• Josephine anakwatiwa ali ndi zaka 19 zokha. Kodi anthuambiri mdera lanu amakwatiwa ali ndi zaka ngati zimenezikapena zocheperapo? Kodi ubwino ndi kuipa kwakukwatiwa munthu ukanali wa mng’ono msinkhu ndikotani?

• Ndi chifukwa chiyani amuna kapena akazi amachita zachimasomaso ngakhale kuti ali pa banja? Lembanimndandanda wa zimenezi ndipo mupeze njira zimenemungathetsere khalidwe limeneri.

• Ku chigawo chino cha kumwera kwa Africa, amai ambiriokwatiwa amapezeka kuti ali ndi kachilombo ka HIV. Kodiinu mukuganiza kuti ndi chifukwa chiyani izi ziri chonchi?

Kodi Josephine achite chiyani tsopano? Nanga Charlesachite chiyani?

Kanthu n'khamaphwiti adakwatira

njiwa

Sunga khosimkanda oyera

uzavala

Page 100: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndimakhala ndi nkhawapopanda chifukwa

Okondedwa Auntie Stella

Ndili ndi zaka 15 ndipo ndili ndi vuto lomwe likundipangitsakukhala moyo wosasangalala. Nthawi zina ndimakhala ndinkhawa koma palibe chifukwa chenicheni choti ine ndikhalendi nkhawa choncho.

Anzanga onse amakhala akusangalala, kotero kuti inendimangodziumiliza kuti ndikhale ngati nanensondikusangalala. Ndikovuta kuchita izi, koma ndikudziwansokuti ngati sindingatero ndiye kuti sindingakhale ndi anzangaocheza nawo. Kodi pamenepa, vuto langa ndi chiyani?Chonde azakhali, ndithandizeni.

Lucy

©TARSC

31

QF31

Page 101: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB31

• Kodi alipo achinyamata ambiri omwe amamva mthupimwawo ngati zimene zikumuchitikira Lucy? Ngati ndichoncho, ndichifukwa chiyani? Jambulani makwelero.Lembani zinthu zomwe kawiri kawiri zimapangitsaachinyamata Kukhala osasangalala pa sitepe yapamwambakwambiri ya makwelero anu. Kenakanso mulembe zifukwazotsatira, m’musi mwa sitepe yoyambayo motsatana mpakapansi peni peni.

• Ma dotolo amati achinyamata amatha Kukhala okhumudwandi opanda chikhulupiliro nthawi zina chifukwa chazochitika mthupi mwawo pamene akukula. Makamakaatsikana amatha kukhala ndi nkhawa, komanso amathakukwiya mwa msanga akayandikira kupanga msambo. Kodiizi zimakuchitikirani? Kodi zikuthandizani bwanji, pozindikirakuti zimenezi zimachitika chifukwa cha chilengedwe?

• Ichi ndi chiyani ndi kulinga muli awiri. Mwambi umenewuumatanthauza kuti nthawi zonse munthu uyenera kugawanandi anzako za vuto lako. Kodi inu mukugwirizana nawomaganizo amenewa, poyang’ana nkhani ya Lucy, kapena pazochitika za moyo wathu watsiku ndi tsiku?

• Kodi Lucy angapange chiyani pofuna kuthana ndi vuto lake?Kodi inu mumapanga chiyani mukaona kuti muli ndi nkhawa,kapena vuto?

Page 102: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Sindikumfuna mwana ameneyu

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mtsikana wa zaka 16. Ndikanali pa sukulu koma ndilindi mimba. Panopo ndikufuna kudzipha. Ndinatenga mimbangakhale ndinagonana ndi chibwenzi changa kwa masikuowerengeka . Nditamuuza bwenzi langalo, anandifunsa kutindikudziwa bwanji kuti anandipatsa mimba ndi iyeyo. Ndiposakundilankhulanso. Ndikawauza makolo anga akhozakundithamangitsa pa khomo pawo. Mayi anga amavutikakwambiri kuti apeze ndalama zondilipilira sukulu, ndipo kutiamve zimenezi adzakhumudwa kwambiri.

Ine sindikufuna mwana ayi, ndipo sindikufuna kusiyiramaphunziro anga panjira. Zinthu zandivuta komasindikufunanso kumuuza aliyense za nkhaniyi. Njira yokhayoyomwe ndikuiganizira ndi yakuti ndipeze munthu wotiandithandize kuchotsa mimbayi, koma vuto ndi lakutindilibe ndalama zotindingakalipire kochotsamimbako. Chondeazakhalindithandizenimaganizo.

Patuma

©TARSC

32

QF32

Kodi mwini wake wamimbayo ndine?

Page 103: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB32

• Lembani zisankho zoyenera zomwe mukuganiza kutiPatuma akhoza kuchita mmene ali ndi mimbamu. Kenakojambulani chithunzi choonetsa zotsatira za zisankhozimenezi- zabwino ndi zoipa zomwe. Onani chitsanzo chilim’munsimu.

Kodi inu mukanakhala Patuma, mukanatani?

• Patuma akuganiza zochotsa mimba. Kodi kuopya kochotsamimba mozembera malamulo ochotsera mimba ndi kotani?

• Kodi mukuganiza kuti bwenzi lake la Patuma anasiyakulankhula naye chifukwa chiyani? Mukuganiza kuti bwezilakelo amamva bwanji za nkhaniyi? Kodi nanga mnyamatayundi makolo ake akuyenera kupanga chiyani pa nkhani ngatiimeneyi?

• Kodi Patuma angatsate njira yotani kuti adziwitse makoloake za nkhaniyi ndi cholinga chakuti avomereze za vutolo,komanso amuthandize?

NGATIATASUNGA

MWANA

Zitha kusokoneza maphunziro ake

Mavuto azachuma

Akhala mzimayiakadali wamng’ono

KUIPAKWAKE

UBWINOWAKE

Apewa kuchitachinthu choopsya

komanso cholakwiramalamulo

Akula akumukondamwanayo

Page 104: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Chipembedzo changa chimaletsamakondomu

Okondedwa Auntie Stella

Ine ndine m’nyamata wa zaka 18, ndipo ndimamukondakwambiri mtsikana yemwe ndili naye pa chibwenzi. Takhala pachibwenzi kwa miyezi khumi tsopano, ndipo timathakutengana kupita kukayenda ngati anthu okondana. Pakalipano sitinagonanepo, koma timagwirana-gwirana ngakhalensokukisana kwambiri. Koma ndikudziwa kuti tidzayambakugonana posachedwapa chifukwa tonse timafuna kutero.

Koma ine ndili ndi vuto limodzi. Ndine munthu wopemphera,ndipo abusa athu amatiuza kuti kugwiritsa ntchitomakondomu pogonana , ngakhale kwa anthu amene alim’banja ndi tchimo. Iwo amanenanso kuti kugonana pamenemusanalowe m’banja ndikolakwika, zomwe sindimagwirizananazo, popeza ine ndikudziwa kuti zingavute motani, ine ndibwenzi langa tidzakwatirana. Ndisanayambe kupempherandinayambako ndagonana ndi atsikana angapo, ndipondimadziwa kuti izi zinali zolakwika. Koma tsopano ndikudziwa kuti kugonana ndi bwenzi langayu silingakhalensotchimo popeza pakali pano ndili mchikondi cheni-cheni, ndipondikufuna kuliwonetsa bwenzi langalo kuti ndimalikondadi.

Komanso pali nkhani ina. Anthu ena kutchalitchi kwathuamanena kuti ma kondomu ali ndi timabowo ting’onoting’ono tosaoneka ndi maso tomwe tizilombo ta HIVtimatha kudutsamo, kotero kuti munthu sumatetezedwa ndikondomu. Kodi zimenezi ndi zoona? Chonde a Zakhalindithandizeni. Kodi ine nditani pamenepa?

Juma

©TARSC

33

QF33

Page 105: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB33

• Kodi chipembedzo chanu chimaphunzitsa zotani pa nkhanizokhudza kugonana ndi za zibwenzi? Lembani zomwemukudziwa. Kodi mumagwirizana nazo zonsezi? Nanga ndiziti zomwe inu simugwirizana nazo, nanga ndi chifukwachiyani simugwirizana nazo zimenezi?

• Juma ali ndi nkhawa ngati kondomu imatetezadi kukachilombo ka HIV- Kodi inu mungamupatse malangizootani pa nkhani imeneyi?

• Kodi chimene chingachitike ndi chiyani ngati Juma ndichibwenzi chake angagonane mosadziteteza ndi kondomu?

• Kodi mungamupatse malangizo otani Juma ndi chibwenzichake?

Page 106: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndimafuna kukhala mchikondindi akazi okha okha – kodialipo angandikonde

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mtsikana wa za 16. Vuto langa ndi lakuti ndimafunakukhala mchikondo ndi atsikana anzanga basi. Anyamatasindimawafuna. Ndiri folomu 1 ndinali pa ubwenzi ndimnyamata wina wake chifukwa sindimafuna kukhala osiyanandi atsikana anzanga. Zimenezi sizimandisangalatsa ndiposindimamulola mnyamatayo kuti adzindikisa. Chifukwa chaichi chibwenzichi chinatha.

Zimenezi zimandichititsa manyazi. Panopa ndikuopakumuuza munthu wina aliyense kuphatikizapo makolo angakapena akulu a mpingo athu. Makolo anga akhozakundithamangitsa pakhomo pawo. Ku mpingo amati munthuamene amagonana ndi mamuna mnzake kapena mkazimzake ndi wa Satana. Sindingawauzenso anzanga chifukwasangandimvetse. Panopa amandiseka chifukwa ndiribechibwenzi komanso chifukwa chakuti sindimavala ma diresi.

Kodi chikundichitikira ndi chiyani? Sindikufuna kukhalaosiyana ndi anthu ena. Sindikufuna kumakhalandekhandekha chonchi. Nthawi zina ndimalakalaka nditakhala ndi mwawi oyimbira foni munthu wina aliyenseamene samandidziwa kuti ndi muuze za zimenezikundichitikira. Chimene ndikufunitsitsa ndikupezawachikondi wanga koma vuto ndi lakuti sindinakumanekondi mtsikana ngati ine. Ndithandizeni!

Alice

©TARSC

34

QF34

Page 107: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB34

• Kodi mukuganiza kuti alipo achinyamata mdera lanu ngatiAlice amene amafuna kukhala mchikondi ndi akazi okhaokha kapena amuna okha okha?

• Kodi azizibisa kuti iwo ndi otere? Perekani zifukwa zake.Ngati mmodzi wa inu ali ngati Alice (ali pa chikondi ndimkazi kapena mamuna mnzake) auze gulu za zimeneamakumana nazo?

• Alice akuopa kuti palibe amene angagwirizane nayeakadziwe za mmene iye aliri? Kodi zimenzi sinkhanza? Kodianzanu ndi a pa banja panu atadziwa kuti inuyo muli ngatiAlice angatani?

• Kodi mungamulangize chiyani Alice? Adzisungire chinsinsikapena auze anthu ena? Kodi Alice angachitenso chinachiyani?

• Kodi ndi chifukwa chiyani kuli kofunika kudziwa kusiyanakwapati pa mfundo zeni zeni ndi nkhamba kamwa chabe?

Mafunso: Mtsutso

Kodi ndi ziganizo ziti zimene ziri zoonadi zeni zeni (mfundo)ndipo ndi ziti zimene ziri Nkhamba kamwa chabe?

1 Ndi zolakwika kugonana ndi amuna okha okha kapenaakazi okha okha

2 Anthu ogonana amuna okha okha kapena akazi okha okhaamapezeka kwina kuli konse pa dziko la pansi?

3 Maiko ena ali ndi malamulo oyendetsera ziko ameneamavomereza kuti amuna kapena akazi akhoza kumagonanaokha okha.

4 Anthu ogonana okha okha akhoza kutionengera ana.

Page 108: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndimamva ululu kwambirindikakhala kuti ndiri kumwezi(ndikusamba)

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mtsikana wa zaka 17. Nthawi zonse pamene ndili kumwezi ndimamva ululu wambiri, kotero kuti ndimalepherakuyenda bwino-bwino ndipo ndimajomba kusukulu.

Nthawi zonse ndimamva nseru, komanso nthawi zinandimamva kuzizira, kapena kutentha. Izi zimandichitikiramwezi ndi mwezi, kotero kuti anzanga onse amadziwa kutindikupanga piriyodi (ndiri kumwezi) ndikajomba kusukulu.Izi zimandichititsa manyazi kwambiri.

Ndikapita kusukulu, vuto ndilakuti malo okataya thonjelomwe ndayipitsira kulibenso. Ndikakataya thonje langa kuchimbudzi cha madzi, limangotsalira mu mtondo mom’mo.Ndimachita manyazi kwambiri anthu akadziwa kuti ndili kumwezi, chifukwa aliyense amatha kundiseka.

Choncho ndithandizeni azakhali. Ine ndimadandaula kutindimalephera kuphunzira nawo zinthu zambiri mkalasi,kotero kuti ndikhoza kudzalephera mayeso anga.

Agness

©TARSC

35

QF35

Page 109: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB35

• Kodi mukudziwa atsikana ena amene amalephera kupita kusukulu pamene akupanga piriyodi (ali kumwezi)? Kodi izizingakhudze bwanji maphunziro awo?

• Kodi Agness angachite chiyani pa vuto lake la kumva ululupamene ali ku mwezi. Lembani njira zonse zomwemukuganiza kuti zingamuthandize Aginesi.

• Kodi Agness ndi anzake angachite chiyani kuti nthawi zonsem’chimbudzi mwa atsikana muzipezeka motaya thonjelowonongela pamene atsikana ali kumwezi/ akusamba?

• Kodi inu (anyamata kapena atsikana) kapena anzanuanayamba asekapo atsikana amene akusamba / ali kumwezi?Chifukwa chake ndi chiani?

• Kodi mukuganiza kuti Agness amachita manyazi anthuakadziwa kuti iye ali ku mwezi, kapena kuti akusambachifukwa chiyani? Kodi anzanu enanso izi zimawachitikira?Kodi inu kapena anzanu (anyamata kapena atsikana)amaganiza motani pankhani zokhudza kusamba kwaatsikana:

– Amaona ngati ndi za umve ndi zochititsa manyazi?– Amaona ngati ndi chilengedwe chabwinobwino cha

munthu wa mkazi ? – Kapena amaona bwanji?

Kodi maganizo amenewa ndi othandiza pa miyoyo yanukapena ayi? Nanga ngati simaganizo othandizamungawathetse bwanji?

Page 110: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Achidyamakanda anga amandizunza

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mtsikana wa zaka 16. Ndinasiya sukulu chifukwa chofunakukhala modelo?. Bambo yemwe ndili naye pa chikondi, ndimunthu wa bizinezi komanso ali ndi esiteti ya fodya yaikulu.Mkuluyu ndinakumana naye miyezi itatu yapitayo,pamenendinapita ku sitolo kwake, ndipo anandifunsira kuti tikhalepachibwenzi . Anzanga anandilimbikitsa kuti ndimulore popeza alindi chuma . Anandilimbikitsanso kuti abambo ngati amenewoamapereka kwa atsikana zinthu monga zovala , komanso zakudyazabwino, ngati nkhuku.

Poyambilira ankandipatsa mphatso, ndiponso analonjeza kutiandithandiza kuti ndidzakwaniritse maloto anga okhalamodelo?Kuonjezera apo, anamulembanso ntchito mchimwenewanga pa esiteti yawo. Kunena zoona takhala tikuyendapagalimoto lake ngakhalenso kukagona ku malo odula ngatikumahotelo. Koma tsopano chimene akufuna iye ndikutitizigonana basi. Ndipo ndikafunsa china chilichonse,amangondikalipila, kumandinena kuti ndine hule.

Mulungu wathawu, ndinapempha kuti agwiritse ntchito kondomupofuna kudziteteza, koma anakwiya kwambiri mpaka kundivulazapamene timagonana. Anandiuza kuti ngati ndikufuna mphatsokuchokera kwa iwo , ndiyenera kugonana nawo mosadzitetezandi kondomu. Anandilonjeza zakuti akhoza kundipezeramankhwala azitsamba ngati ndingawafune, koma ine ndimaopa.Panopa samalankhulanso nkhani zondithandiza kuti ndikhalemodelo?

Ndikudziwa anzanga sindingawafunse kuti andithandize maganizo,chifukwa andiseka. Poyamba ndinkawanyaditsa kuti azichita nanensanje. Kodi azakhali pamenepa nditani?

Veronika

©TARSC

36

QF36

Page 111: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB36

• Khalani anthu awiriawiri, ndipo mujambule chithunzi cham’bambo ali pa chibwenzi ndi mtsikana. Ngati mungafunemuonetse pachithunzicho zomwe zikuchitika. Pomalizaafotokozereni anzanu za chithunzi chanu.

• Kodi ndi chifukwa chiyani abambo akuluakulu amakondakukhala pachibwenzi ndi atsikana ang’onoang’ona ngatiVeronika ?

• Kodi ndi chifukwa chiyani, atsikana ena achisodzera amafunakukhala pa chibwenzi ndi azibambo akuluakulu. Kodi palizifukwa zina zabwino, kapenanso zoyipa?

• Kodi mungamupatse malangizo otani Veronika?

Page 112: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Chikondi ChimandilepheretsaKuwerenga

Okondedwa Auntie Stella

Ine ndine mnyamata wa zaka 17, ndipo ndiri pa chibwenzindi mtsikana wina pa sukulu pathu. Panopa ndiri fomu 4ndipo ndikufunitsitsa kuti ndidzapambane bwino mayesoanga a MSCE. Vuto limene ndiri nalo ndi lakutindimamkonda bwenzi langalo kwambiri mpaka ndayambakulephera m’kalasi. Palibe chirichonse chimenechikundisangalatsa. Zowerenga ndinasiya chifukwa nthawizonse ndi maganiza za iye basi. Nthawi ina ndinaganiza kutindingothetsa chibwenzi koma ndinaona kuti sindikanachitabwino ayi, chifukwa iye sanandilakwire chilichonse. Kodipamenepa nditani? Chonde ndithandizeni. Ndiri ndi nkhawakuti mwina ndikhoza kulephera nazo mayeso.

Mussa

©TARSC

37

QF37

Page 113: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB37

• Kodi mukuganiza kuti vuto la Mussa ndi lalikulu pakati paachinyamata a chisodzera m’masukulu?

• Kodi chikondi chinayamba chakuchititsani kuti musakhalendi chidwi pa chinthu china chirichonse? Ngati ndi choncho:

a) Zinakutengerani nthawi yaitali bwanji kuti zithe?b) Kodi munapeza njira yothetsera vuto limeneri?c) Kodi chinachitika kumapeto chinali chiyani?

• Kodi malangizo omwe mungamupatse Mussa ndi otani?Kodi akuyenera kumusiya okondedwa wakeyu? Kodiangapange chiyani ngati akufuna kuti akhale nayebe pachikondi koma asalephere mayeso?

• Werengani ndakatulo yotsatirayi, yolakatulidwa ndi Laurandi Monika. Kodi munayamba mwamvako chonchi?

Dzanja langa liri gwa! Silingathe kulemba kanthu kupatulaDzina lako – chinthu chokhacho chimene chiri cha nzeru kwa ineMaganizo anga akundiuza kuti, ‘phunzira’Mtima wanga ukuti’Paulo’Chomwe chinali chofunikira kwa ine poyamba chapita tsopanoKuseri kwa utsi wa chikondi choyaka ndi moto.Yaphimba mitambo tanthauzo la moyo wanga ndi maphunziro anga.Koma iwe!Chikondi sichingakutsegulire khomoLa tsogolo la moyo wako Dzuka! Ino ndi nthawi yokonza tsogolo lako

Laura Moyo and Monica Masukusa

Page 114: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Mai anga ali ndi kachilombo kaHIV ndipo samabisa

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mnyamata wa zaka 22. Mai anga ali ndi kachilombo ka HIVndipo amanena poyera za momwe iwo aliri. Mai angawo amagwirantchito ku bungwe lomwe limagwira ntchito za HIV ndi Edzi, ndipoamanena poyera kuti; ‘kukhala ndi kachilombo ka HIV si chinthuchochititsa manyazi konse ayi’.

Ndinali ndili mu sitandade 4 pamene mayi anga anandiululira kutianali ndi kachilombo ka HIV. Poyamba ndinali ndi mantha kwambiri,kuopa kuti mwina atha kufa msanga, koma panopa ndinazindikirakuti sichoncho ayi, munthu utha kukhala ndi kachilombo ka HIV, ndikukhala ndi moyo kwa nthawi yaitali. Mayi anga panopa akhala ali ndikachilomboka kwa zaka khumi ndi mphambu ziwiri. Amadzisamalirabwino lomwe pakudya zakudya zopatsa thanzi, komanso pokhalaosangalara, kotero kuti amakhala ndi moyo wathanzi nthawi zambiri.Mayi anga amati sayenera kubisa kalikonse za matendawa, pofunakuthetsa mantha omwe anthu amakhala nawo pa zamatendawa,komanso kusalana.

Koma ine sindimagwirizana nawo maganizo awowa, popeza nthawizonse anthu samawaona bwino anthu omwe ali ndi kachilombo kaHIV, kotero sikoyenera kuwauza. Anthu amene ungathe kuwauza ndiachibale apafupi kwambiri, komanso pokhapokha ngati angathekukusungira chinsinsi.

Chimodzi chokha chomwe sitimasemphana maganizo ndi mayiangawo ndi chakuti ana ako okha ayenera kuuzidwa, chifukwangakhale usawauze, amathabe kuzindikira okha. Ana ayenera kudziwachilungamo chenicheni, komanso kukamba momasuka za nkhaniyi.

Nanga pamenepa maganizo anu ndi otani? Inetu ndimakonda mayiangawa ndipo ndi mawanyadira, koma nanga ndi ndani mwa ifeamene akulondola pa nkhaniyi.

Paulo

©TARSC

38

QF38

Page 115: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

QB38

• Kodi mukuganiza kuti ubwino kapena kuyipa konena poyerangati munthu uli ndi kachilombo ka HIV ndi kotani?Lembani maganizo anu, ndipo mugawe mayankho anuwom’magawo awiriwa:

• Kodi inu mukanakhala kuti munapezeka ndi kachilombo kaHIV, mukanamuuza ndani- phungu, banja la kwanu, anzanu,ogwira nawo ntchito ndi ena? Kodi ndi ndani amenesimungafune kuti mumuuze nkomwe?

• Kodi makolo anu akamakubisirani zinthu mumamva bwanji?Auzeni anzanu mmene mumamvera, osati zomweankakubisiranizo. Kodi mukugwirizana ndi maganizo akutiana ayenera kuuzidwa chilichonse, ngakhale chitakhalachomvetsa chisoni?

• Kodi mukuganiza kuti makolo angathandize bwanji ana awokuvomereza kuti makolowo ali ndi kachilombo ka HIV,kapena m’modzi mwa anawo ali ndi kachilombo ka HIV?Auzeni anzanu za maganizo anu. Afunseni ma bungweamene amagwira ntchito yothandiza pa nkhani za HIV ndiEdzi kuti mudziwe zambiri.

Kukhala ndi kachilombo ka HIV, sichinthu chochititsa manyazi.

©TARSC

Page 116: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndingathane nazo bwanji Ziphuphu zanga?

Okondedwa Auntie Stella

Ndili ndi zaka 15, ndipo ndili ndi vuto la ziphuphukunkhope kwanga, zomwe ndikamasamba mnthupizimandipweteka. Vuto limeneli linayamba chaka chatha,koma palibe kusintha kulikonse.

Tsiku lina nditawafunsa azakhali anga, anandiuza kutichimenechi ndi chizindikiro cha kukula, ndipo palibe njirailiyonse yomwe angandithandizire kuti vutoli lithe. Mwaanthu onse ndakhala ndi kuwafunsa za vutoli palibe aliyenseanandithandiza. Koma tsiku lina ndinafunsa anamwinokuchipatala, ndipo anandilangiza kuti ndizigwiritsa ntchitosopo yocheperapo mphamvu. Kuchokera pamenepa sopondimagwiritsa ntchito ndiyokhayo yopanda mphamvu basi.Koma vuto ndi lakuti ziphuphu sizikuthanso, ndipo pakalipano ndi pamene zikuchuluka kwambiri kotero kuti nkhopeyanga sikuonekanso bwino. Chifukwa cha chimenechi, inesindikuthanso kumayenda ndi anzanga chifukwandikumachita manyazi.

Chonde azakhali, ndithandizeni mankhwala oyenera omwendingagwiritse ntchito kuti vuto langa lithe, ndisanaganizezopita kwa a sing’anga.

Joana

©TARSC

39

QF39

Page 117: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB39

• Kodi mukuganiza kuti gwelo la ziphuphu za Joana ndichiyani?

• Kodi chimene chimayambitsa kapena kuthetsa ziphuphu ndichiyani?

a) Kodi pali zakudya zina zimene zili za bwino kapenazoyipa ku khungu lanu?

b) Kodi pali zakumwa zina zimene zili zabwino kapenazoyipa pa khungu lanu?

c) Kodi pali mtundu wa sopo kapena mafuta amene aliabwino kapena oyipa pa khungu lanu?

• Kodi angathandize pa vuto limeneri ndi ndani? A dotolo?Asing’anga? Kapena wina aliyense?

Page 118: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndine woyembekezera komansondili ndi kachilombo ka HIV

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mtsikana wa zaka 21, ndipo ndili ndi mimba yamiyezi 6. Mwamuna wanga anakhala akudwala kwa nthawiyaitali, ndipo wangomwalira posachedwapa ndipo tsopanondinabwerera kwa makolo anga.

Nditayamba sikelo, a namwino anandifotokozera zandondomeko yomwe ndingatsate kuti ndiyezetse magazipofuna kudziwa ngati ndili ndi kachilombo ka HIV kapenaayi. Ndinavomera kuti andiyeze ndipo anandipeza kuti ndirindi kachilombo ka HIV ngakhale kuti thupi langasilikuonetsa kudwala. Ndinakhumudwa kwambiri makamakapoganizira mwana yemwe ndikuyembekezera. Sindikufunakuti mwanayu ndidzampatsire kachilomboka.

Anamwino anandiuza kuti akhonza kundipatsa mankhwalaotchedwa Neverapini pofuna kuteteza mwanayo kutiasatengere kachilomboka. Analankhulanso za nkhaniyoyamwitsa mwana kwa nthawi yaitali, koma inesindinamvetse popeza ndimangolira.

Kodi pamenepa azakhali, ndingachite chiyani kuti nditetezemwanayu? Kodi adzabadwa ali odwala kale? Nanga pamenendili ndi kachilombo ka HIV chonchi, ndibwinokumuyamwitsa mwanayo?

Namoyo

©TARSC

40

QF40

Page 119: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB40

• Kodi Namoyo akuchita bwino kukhala ndi nkhawa ndimwana wake? Kodi chimachitika ndi chiyani pamene mayiali ndi kachilombo ka HIV kapena akudwala matenda aEdzi? Kodi mwana angatenge kachilomboka? Kodi izizingachitike nthawi yake iti?

• Kodi ubwino kapena kuopsya koyamwitsa mwana pamenemayi ali ndi kachilombo ka HIV ndi kotani? Kodi Namoyomungamulangize chiyani ?

• Kodi mwambo wanu umati chiyani zokhudza amayi omweasankha kusayamwitsa mwana? Kodi anthu angachite chiyanipofuna kusintha maganizo olakwika omwe anthu amakhalanawo okhudza amayi omwe amasankha kusayamwitsa?

Page 120: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Mchimwene wanga anachitamdulidwe

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mnyamata wa zaka 15 zakubadwa. Ndiri ndimchimwene wanga wa zaka 22 Ndimamunyadira kwambiri.Ndiwamakhalidwe abwino, okhulupirika, ozindikira zinthumsanga mwakuti anthu anthu ambiri amamukonda ndipoanamusankha kukhala Peer educator.

Koma dzulo anandidabwitsa kwambiri. Anandiuza kutianapita kuchipatala kukachita mdulidwe. Izi zinandithetsanzeru kwambiri chifukwa sindikudziwapo munthu winaaliyense amene anachita mdulidwe. Ndinawerengapopenapake kuti anthu a mitundu ina ndi zipembedzo zinaamachita zimenezi.

Mchimwene wangayu akuti mdulidwe umachititsa kutichokodzera chidzikhala cha ukhondo komansokumathandiza kuti munthu asatenge matenda opatsiranapogonana ndi HIV. Anandiuzanso kuti akadzabereka mwanawa mwamuna adzamuchita mdulidwe akanali wamg’ono.

Kodi mchimwene wangayu akufuna kundiuza chiani? Kodiakufuna kuti nanenso ndikachite mdulidwe? Ndikuopakwambiri ndipo sindikufunanso kumaganizira za izi. Atatialakwikwa ndi kukudula chokodzera zingathe bwanji!Ndikuopa!

Sunganani

©TARSC

41

QF41

Page 121: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB41

• Auzeni anzanu zimene mukudziwa za mdulidwe. Ndichifukwa chiani anyamata ena amachita mdulidwe?

Tsopano taonani chithunzi chiri munsimu ndipo muyankhemafunso otsatirawo.

– Kodi chithunzichi chikufotokozanji pa mgwirizanoumene ulipo pakati pa mdulidwe ndi HIV? Kodi izizasntha maganizo ano pa mdulidwe?

– Sankhani maiko awiri pa chithunzichi. Kodimukudziwapo chiyani za mdulidwe mumaikoamenewa? Kodi Sunganani mungamulangize chiani?

Zam

bia

Zim

babw

e

Moz

ambi

que

Sout

h A

fric

a

Mal

awi

Tanz

ania

Ang

ola

Gha

na0

5

10

15

20kuchuluka kwa anthu amene ali ndi HIV

kuchuluka kwa anthu amene anadulidwa

perc

enta

ge

Page 122: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndiri ndi zibwenzi zambiri zoganana nazo

Okondedwa Auntie Stella

Ndine mtsikana ndipo ndinamaliza sukulu yanga chakachatha. Zotsatira za mayeso anga sizinatuluke ndipondikugwira ganyu pa golosale ya munthu wina wake dzinalake Amon Ndiri ndi chibwenzi ndi Michael, nyamata amenendimamukonda komanso makolo anga amadziwa za iye.Tinayamba kale kuchita zogonana ndi chibwenzi changachi.

Masiku apitawa abwana anga anayamba kundifunsira ndipondinawalola ngakhale kuti ndi akulu kwambiri kuposa ine.Amandipatsa ndalama ndi mphatso zosiyanasiyana zimenechibwenzi changa sichingakwanitse kundipatsa. Panopandinayamba kale kumagonana nawo. Zakuti ndiri ndichibwenzi amadziwa ndipo iwo amangofuna kutindidziwaonetsa chikondi ndi kumagonana nawo.

Chandikhumudwitsa kwambiri ndi chakuti abwana angawandazindikira kuti ali pa banja. Ndinafuna kuti ndithetsechibwenzi ndi iwo koma anandikumbutsa kuti nanenso ndirindi chibwenzi china choncho panalibe vuto. Ndikudziwakuti sandikwatira komabe sindingathe kuti ndithetsechibwenzi ndi a bwanawa chifukwa adzasiya kundipatsandalama zimene chibwenzi changasichingathe kundipatsa. Izizikundisowetsa mtenderekwambiri. Nditani?

Grace

©TARSC

42

QF42

Page 123: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOKAMBILANA

©TARSCQB42

• Kodi mukuganiza zotani za nkhani ya Grace. Kodi anyamatandi atsikana a mdera lanu amakumana ndi vuto ngatilimeneli?

• Lembani zifukwa zimene atsikana ena amakhalira ndizibwenzi zambiri zogonana nazo nthawi imodzi? Kenakalemebani zifukwa zimene anyamata amachitira zimenezi?Kodi zifukwa zimene mwapeza ndi zosiyana? Ngati ndichoncho mukuganiza kuti ndi chifukwa chiyani?

• Chithunzi chiri munsimu, chikuonetsa mmene zibwenzi zaGrace zimayendera. Zikuonetsanso kuti Grace samadziwakuti Amon anali ndi chibwenzi china dzina lake Lilian.

– Kodi ndi zibwenzi zina zitizimene zingaonekemchithunzi ichi? Jambulanichithunzichi pa pepala ndipo munonetse maubwenziamene angaoneke pa tchithunzichi.

– Chibwenzi cha lillian chiri ndi HIV komasichikudziwa. Chibwenzi chimenechi sichimakongakugwiritsa ntchito kondomu pogonana. Kodi ndianthu ena ati amene angate HIV ? Perekani zifukwazake.

– Kodi chithiunzi chikutiuza zotani zokhala ndizibwenzi zambiri zogonana nazo nthawi imodzi?

• Kodi Auntie Stella amulangize zotani Grace za zibwenzizake ziwirizi?

GraceMichael

Lillian

Amon’swife

Amon

Lillian’sboyfriend

Page 124: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

������������

Chichewa Answer Cards

Page 125: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi ndi koyenera kuti ndigonane naye?

Okondedwa Zione

Ndizovuta pamene anthu awiri akufuna zinthu zosiyana kuchokerakwanzake, komabe akuluakulu amati: kuthamanga sikufika. Anthuambiri amadikira mpaka atakula kapena kulowa mbanja ndi pameneamayamba kuchita zogonana. Ubwino wodikira kuyamba kugonanampaka utakula ndi wambiri. Munthu akakhala wamkulu amakhalaokonzeka mmaganizo kukhala ndi chibwenzi. Komanso ngatisimugonana simungatenge matenda opatsirana pogonana,kachilombo ka HIV, komanso mimba zosakonzekera.

Pakali pano, ndi zabwino ndithu kuti inu awiri mumathakukumbatirana ndi kukisana (kupyompyonana) kenaka ndikusiya. Iyindi njiri yapamwamba yoonetserana mmene inu awirimumakonderana. Iwe usadandaule, anyamata komanso atsikana,amatha kumangokumbatirana osapitiriza kuchita zogonana popandachoipa china chiri chonse kuwachitikira.

Komabe, achinyamata ambiri amakhulupilira kuti pamenemwayamba kugwiranagwirana ndi kukisana mumayenera kutimugonane basi- choncho ndi bwino kuti nthawi zambiri muzikhalandi anzanu, kusiyana kuti muzikhala nokha kumagwiranana ndikukisana.

Pomaliza achinyamata azitha kuzisankhira zinthu zoyenera kwa iwopopanda kukakamizidwa ndi munthu wina aliyense. Ukambiranenacho chibwenzi chakocho ndipo ngati chimakukondadichikumvetsetsa

Ngati ungaganize zogonana nacho m’tsogolo mudzagwiritse ntchitokondomu (kaya kondomu ya amuna kaya kondomu ya amai).Kondomu ingakutetezeni ku matenda opatsirana pogonanakuphatikizapo HIV ndi kutenga mimba yomwe sukuifuna ngatiwaigwiritsa ntchito bwino pamene mukugonana. Zabwino zonse.

Auntie Stella

©TARSC

1

AF1

Page 126: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB1

• Kodi ndi zotheka kumangogwiranagwirana ndi kukisana kenakandikusiya osapitiriza kugonana? Ngati sichoncho, mungachitechiyani? Mutakhala kuti ndinu Zione, kodi mungatani kutimuonetsetse kuti mukusangala koma simukugonana?

• Pagulu lanu lembani zifukwa zonse zimene zimachititsaachinyamata kuyamba kugonana. Ndipo lembaninso zifukwazimene zimachititsa achinyamata ena kuti azidikira mpaka atakula.

Kodi inu mungasankhe chiyani? Fotokozani

MAFUNSO: Kodi ndife okonzeka kuyambakuchita zogonanaYankhani mafunsowa nokha kapena ndi chibwenzi chanu. Yankhani kuti EYA,IYAYI kapena SIKWENIKWENI

1 Kodi timadziwana bwinobwino ndi kukhulupilirana wina ndi mzake?

2 Kodi ndife a bwenzi?

3 Kodi tikhoza kukambirana mosavuta za nkhani yogonana ndikudziwapamene tingailekezere osafika poti tigonane ?

4 Kodi tinakambiranako ndi kugwirizana za mmene tingadzitetezerekumatenda opatsirana pogonana, kupewa mimba komansokachilombo ka HIV?

5 Kodi tinayamba takambirana zokayezetsa magazi kuti tidziwe ngatitiri ndi ka chilombo ka HIV mmatupi mwathu kapena ayitisanayambe kugonana?

6 Kodi tinayamba takambilanapo kuti tidzachita chiyani tikadzapatsanamimba?

Mayankho: Ngati mwayankha AYI kapena SIKWENIKWENI kufunso lina lirilonse pa mafunso awa, ndiye kuti inuyo ndi chibwenzi chanu simuliokonzeka kuyamba kugonana. Kuyamba kugonana sichisankho chamasewera.

Page 127: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi chokodzera changa ndichaching’ono kwambiri?

Okondedwa Peter

Usadandaule – ulibe vuto lina lililonse. Chokodzera cha anyamata chimayamba kukula pamene ayamba kumela tsitsi kukhwapa ndi kumaliseche. Izi zimachitika pakatikati pa zaka 11 ndi15 koma zitha kuyambika mwa msanga kapena mochedwa.Sichachilendo anyamata kufananitsa maliseche awo ndi a anzawo.Anthu timayamba kumela tsitsi malo atchulidwa aja nthawizosiyanasiyana choncho sichachilendo kuti achinyamata a zakazofanana akhale ndi zokodzera zosiyana makulidwe ake.

Ngakhale thupi lako litakhala kuti ndilokhwima, palibe msinkhuweniweni omwe maliseche amunthu amayenera kukhalira. Anthuali ndi matupi ooneka mosiyanasiyana, choncho maliseche awoamasiyananso.

Komanso maonekedwe a maliseche amakhudzana pang’onochabe ndi mmene mkazi angamvere kukoma pamenemukugonana. Chinsinsi cha kupanga mkazi komanso iweyo kutimunve kukoma pamene mukugonana chagona mmene iweyoumngagwiritsire ntchito malisechewo komanso magawo enaathupi lako. Akazi kwambiri amakonda zogwiranagwirana ndikukisana kugonana kusanayambike, chifukwa iwo amayambakumva kukoma mochedwelapo kusiyana ndi amuna. Komansoanthu amamva bwino akamagonana ndi munthu amene amaganizaza moyo wawo nthawi zonse ndipo amadziwa zomwe iwoamakonda kapena kudana nazo. Ndikosavuta kukhala pa ubwenziwamtundu umenewu pamene uli wankulu bwino ndipo mungathekukambilana zomwe mukufuna.

Auntie Stella

©TARSC

2

AF2

Page 128: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB2

• Maonekedwe kapena kukula kwa chokodzera sikungapangitsekuti mukhale ndi ubwenzi omwe mungasangalale nawo, komandichiyani chingapangitse izi? (Ganizani mmene inuyo mulili ndipomumakhala bwanji osati maonekedwe anu okha)

• Aliyense alembe dzina lake pamwamba pa pepala ndiposinthanitsani mapepalawo pagulu lanulo. Papepala lomwemwalandiralo lembani zomwe zili zosangalatsa za mwini wake wapepalalo (Mwachitsanzo: mumamwetulira bwino, mapewa anu ndiakulu bwino amandisangalatsa, tsitsi lako ndi lokongola). Muthakulemba dzina lanu pomaliza ngati mungafune. Pepala lanu lijalikakupezani muona zomwe anthu amasilira za inu.

• Kodi kumalo komwe mumakhala kuli malo ena monga sukulu,tchalichi, chipatala kapena anthu ena mwinanso achibale omweamazipeleka kukupatsani malangizo oyenera okhudzana ndi thupilanu, kugonana komanso zibwenzi. Kambilanani kapena pitanikumalo amenewo kuti muone ndi malo ati amene amamvetsa ndikuthandiza. Muli ndi ufulu ofunsa funso lina lililonse ndi kupezamayankho oona komanso chithandizo chenicheni.

• Ngati mdela lanulo mulibe thandizo lokwanira ndipo achinyamatasatha kudziwa zambiri, mungapangepo chiyani? Muli ndi malo aachinyamata (Youth Centre) pafupi nanu kapena mungathekuyambitsa? Uzani anzanu maganizo anuwo ndipo sankhani njiraimene ili yotheka.

Page 129: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi ndigone naye mwamunawa mchemwali wanga?

Okondedwa Patricia

Mlamu wakoyo akunama zachikhalidwe. Pachikhalidwe chathu,chilamu chimakhala choseleulana pakati pa tsikana ndi alamu akea amuna. Sizitanthauza kuti mtsikanayo akuyenera kugonachipinda chimodzi ndi mlamu wakeyo kapena kugonana naye; izisizololedwa muchikhalidwe chathu. Muli nawo ufulu onena totongati alamu anu akufuna kugonana nanu.

Afunse achibale amene umamasuka nawo, anthu amene banjalanu limacheza nawo kapena wamkulu wina aliyense ameneangamve chisoni kuti akuthandize. Sichikhala chovuta kuthanandivuto limeneli utapeza thandizo. Komanso yesa kuyankhula ndinchemwali wakoyo.

Sizololedwa kwathu kuno kuti munthu agonane ndi mwanaosakwana zaka 16. Munthu wamkulu opanga izi atha kupitakundende. Sizololedwa kuumiliza munthu aliyense kugonana naye.Kumeneku kumatchedwa kugwililira ndipo muyenera kukanenaku Polisi. Kuipitsitsa kwa izi ndi kwakuti mutha kutenga mimbakapena matenda opatsirana pogonana ngakhalenso kachilomboka HIV.

Khalidwe lathu ndilabwino ndipo limapangitsa kuti anthutizigwirizana monga banja kapena mudzi. Anthu asamalakwireanthu anzawo nkumanena kuti chikhalidwe ndichomwechapangitsa.

Auntie Stella

©TARSC

3

AF3

Page 130: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB3

• Maiko ambiri aku mmwera kwa Africa ali ndi miyambo ndimachitidwe ambiri amene amakhudza achinyamata ndi mchitidwewogonana monga kuyamba kugonana, kuona ngati sunagonaneko,kukwatira mkazi wa m’bale wako yemwe anamwalira ndi zinazambiri. Lembani m’ndandanda wanu wa zinthu monga zimenezi.Kambilanani zomwe mumagwilizana nazo komanso zomwesimugwirizana nazo zokhudza makhalidwewa. Mwachitsanzo,ndiziti zomwe zimateteza kapena kulimbikitsa kufalitsakachilombo ka HIV.

• Kodi chikhalidwe chanu chimafanana pa akazi ndi amuna. Ngatisichoncho, mumanva bwanji pa zimenezi? Mungapangepo chiyani?

• Mungagwire bwanji ntchito limodzi ndi mafumu komansoakuluakulu yosintha chikhalidwe chomwe chili choonongaachinyamata masiku ano? Ndi ndani wina/ena angakuthandizeni?

• Mudzi ulionse umayenda osati ndi chikhalidwe cha mudzi okhawoayi komanso makhalidwe ena ochokera ku midzi ina. Jambulanichithunzi (kapena lembani mndandanda) kuonetsa zomwemumazikonda kwambiri za chikhalidwe chanu KOMANSO zachikhalidwe cha makono. Mungathe kutenga zabwino zokhazokhakuti zizikutsogolerani pa moyo wanu?

Page 131: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndikusamalira munthu odwalamatenda a Edzi

Okondedwa Maria

Palibe chifukwa chakuti uchokere pakhomopo. Iwetu siuli pachiopsezo cha mtundu wina uliwonse. M’mene malume akoakudwaliramu akusoweka chikondi ndi chisamaliro chochekerakwa abale ngati iwe.

Pali njira zenizeni zitatu zimene munthu angatengere kachilomboka HIV. Njirazi ndi monga kugonana ndi munthu amene ali ndikachilombo ka HIV mosagwiritsa ntchito kondomu; Kupyoleram’magazi, mmajakisoni kapena malezala; kapena kuchokera kwamai kupita kwa mwana pa nthawi yobereka kapena pa nthawiimene mai akuyamwitsa mwanayo. Mai angathenso kupatsirakachilomboka kwa mwana wake pa nthawi imene mwana alim’chiberekero.

Sungatenge HIV podyera mbale imodzi kapena kugwiritsa ntchitoziwiya zosiyanasiyana ndi munthu amene ali ndi kachilomboka,kapena kugona chipinda chimodzi ndi munthu amene ali ndikachilombo ka HIV. Munthu umakhala pa kachiopsezokakang’ono ngati uli ndi bala m’dzanja lako ndipo magazi amunthu amene ali ndi HIV akagwera pa bala lakolo nalowam’thupi mwako. Kuti udziteteze kwa thunthu ndi bwino kumavalama gulovesi, mapepala kapena majumbo a pulasitiki pameneukugwira china chirichonse chimene chiri ndi magazi. Nthawizonse udzisamba mmanja ndi sopo komanso udzichapila sopozovala ndi zogonera zina ziri zonse.

Ntchito yosamalira munthu wodwala ndi yovuta kotero ndipofunika kuti anthu ena adzikuthandiza. Kumbukira kuti malumeako akufunika kuwaonetsa chikondi ndikuwapatsa chisamaliro ndichithandizo choyenera ndi chokwanira. Choncho usaope. Limbamtima!

Auntie Stella

©TARSC

4

AF4

Page 132: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB4

• M’mabanja ambiri, udindo wosamalira ndi kudwazika wodwalaumakhala wa amai ndi atsikana. Kodi abambo ndi anyamataangathandizepo bwanji posamalirira ndi kudwazika odwala? Kodindikofunikira bwanji kuti amuna adzitengapo mbali posamalirandi kudwazika odwala? Lembani mndandanda wa zinthu zimenemungachite kuti muthandize kusamalira ndi kudwazika odwala.Mwa chitsanzo kusesa pa khomo la munthu odwala, kuchezanaye, kusewera ndi ana ake, kukatchola nkhuni kapenansokuwaphikira kumene

• Fufuzani mabungwe (kaya mabungwe a boma, mabungwe omwesi a boma, mabungwe a za chipembedzo) komanso zipatalazomwe ziri m’dera lanu omwe amathandiza ma banja amene alindi munthu amene ali ndi kachilombo ka HIV kapena ameneakudwala matenda a Edzi. Kodi mabungwe amene mwapezawoamathandizapo pophunzitsa anthu mmene angasamalire munthuodwala ku mudzi? Kodi inu mungakondweretsedwe kutimuphunzitsidwe kasamaliridwe ka munthu amene akudwalira kumudzi? Gawanani ndi anzanu za nkhawa zanu komansozakupambana kwanu pa ntchito imeneyi.

• Khalani m’magulu ndipo kambiranani zifukwa zimene zimachititsakuti achinyamata ambiri adzitenga kachilombo ka HIV(Kambirana zifukwa zokhudza chikhalidwe, chipembedzo,umphawi, kusowa kwa ntchito, mavuto okhudza ku chipatala ndiena otero)

a) Ndi mavuto ati amene mungawathetse? Fotokozanimayankho anu.

b) Ndi mavuto ati amene ali akulu kwambiri kotero kuti ndiofunika mabungwe akuluakulu kuti achitepo kanthupothetsa mavuto amenewa

c) Kodi pali china chiri chonse chimene achinyamataangachite pothandiza mabungwe akuluakulu amenewa?

• Kodi inuyo pa nokha mungatani kuti mudziteteze komanso kutimuteteze anzanu kuti asatenge kachilombo ka HIV?

Page 133: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndine mutu wa banja lathutsopano!

Okondedwa Lovemore

Ndizomvetsa chisoni kuti mayi ako sanasiye wilu. Akanasiya,moyo wako sukanakhala ozunzika chonchi panopa.Amalume akoakhale munthu wamanyazi potenga katundu wanu.

Ndi msinkhu wakowo suyenera kuthetsa vuto limeneli wekha.M’dera lililonse mumakhala anthu komanso mabungwe omweamayang’anira komanso kuthandiza achinyamata omwe alibemakolo. Ufufuze anthu kapena mabungwe oterewa kutiakuthandize. Funsira malangizo kwa abusawo. Ukambirane ndianthu kapena mabungwe mdera lanulo makamaka magulu omweamathandiza mabanja okhudzidwa ndi matenda a Edzi.Ukhozanso kulankhula ndi mphunzitsi wankulu, a nesi, mafumukapena anthu ogwira ntchito boma mdera lanulo.

Usatope kapena kuchita manyazi kupempha thandizo –achinyamata akuyenera kusamaliridwa ndi kukhala ndi chakudya,zovala, malo okhala, maphunziro komanso chitetezo.

Inde, achinyamata ambiri ali ndimavuto ngati omwewa. Yankhulanawo. Muli ndizambiri zoti mungagawane – chisoni chanu,kuvutika kwanu komanso kukwaniritsa kwanu. Muthansokugawana maganizo mmene mungathetsere mavuto anu. Muthakugwirizana zoyamba kupanga zinthu monga dimba lamasamba.Pemphani kuboma kapena kumabungwe zinthu zomwemungafune; mugulu muli mphamvu kusiyana ndi kuchita zinthupayekhapayekha.

Ndikukufunira iwe pamodzi ndi achimwene ndi achemwali akonthawi yabwino.

Auntie Stella

©TARSC

5

AF5

Page 134: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB5

• Ana amafuna chikondi, chakudya, malo okhala, maphunziro ndimoyo otetezedwa. Kodi kudera lanulo kuli ana ambiri omwealibe zinthu zatchulidwazi? Akukhala bwanji ana amenewa?

• Kodi ana ndi achinyamata monga Lovemore angapeze kutichithandizo m’dera lanulo? Mukuganiza kuti amapeza thandizolokwanira? Ngati samapeza, inuyo ndi anthu a mdera lanulomungatani kuti azikhala moyo osavutika?

• SEWERO: Pangani sewero lomwe gulu la achinyamata amasiyeaitanidwa kukakumana ndi bungwe (committee) la zaumoyo paboma kukakambirana za thandizo lomwe akufuna kuchokeramdera lawo. Taganizani ndindani angakakhale kumsokhanoumenewu ( mwachitsanzo a nesi, ogwira ntchito m’boma, ogwirantchito ku bungwe lothandiza anthu okhudzidwa ndi matenda aEdzi). Likatha sewero, kambiranani mafunso awa:

a) Chinachitika ndichiyani ku msonkhanowu? Kodiakuluakulu amamvera achinyamata? Chifukwa chiyaniamamvera kapena ayi?

b) Kodi achinyamata angatani pakuonetsetsa kuti a zaumoyokomanso othandiza mdera lawolo akuwamvera maganizoawo okhudzana ndi zofuna zawo zenizeni? Ndithandizolanji mungalifune kuti izi zichitike ndipo ndindaniangapereke thandizoli?

Page 135: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndikufuna ndizichita zogonanangati mmene amachitira anzanga!

Okondedwa Titus

Chimene ndingakuuze ndi chakuti palibe chifukwa chokatengerakonda ine kwa a sing’anga kuti mtsikana akukonde nakhala nawepa chibwenzi.

Kukhala ndi chibwenzi sachita kukakamiza. Zikamachitika,zimangochitika zokha basi. Anthu ena amapeza chibwenzi pamsinkhu wako pamene ena amadzapeza chibwenzi atakula.Komatu ngakhale kuti atapeza chibwenzi chokondana nachosikuti nkhani yake imakhala yogonana ngati mmene ukuganiziraiwemu.

Iwe usamadandaule ndi zimene anzako amakamba zakutiamagonana ndi zibwenzi zawo. Chomwe uyenera kudziwa ndichakuti nkhani zawozo zikhoza kukhala za bodza. Anyamataambiri amangofuna kuwonetsera kuti iwo amagonana ndizibwenzi zawo pamene sanagonanepo

Iwetu ndiwe munthu pawekha ndipo suyenera kuti uzichita chinachirichonse chimene anzako akumachita. Iwe uzichita zinthuzimene ukuwona kuti zikuthandiza pa moyo wako.

Choncho usiye kumadandaula kuti ulibe chibwenzi- Iwe ukhalechonchi mpaka pamene udzapeze mtsikana wako wa chikondi.Zakuti sunagonanepo ndi mkazi zimenezo zilibe ntchito. Pajaamatitu kuthamanga sikufika!

Pakadali pano, iwe limbikira maphunziro ako ndipo upezechochita china. Uphunzire kumacheza ndi atsikanamosamawaganizira zoti ukagonane nawo.

Auntie Stella

©TARSC

6

AF6

Page 136: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB6

• Lembani mndandanda wa zinthu zimene mumachita chifukwachotsanzira anzanu.Kuchokera pa mndandanda umenewu,sankhani zimene zili za bwino komanso zimene zili zoipa. Kodimathero ochita zinthu zoipa zimene mwalembazi ndi otani? Kodimukulingalira kusiya kutsanzira anzanu kuchita zinthu zimenemwanena kuti ndi zoipa? Kambiranani ndi anzanu mmenemungachitire izi.

• Kodi mutati mudzipatse malikisi pa mlingo wa 10 (out of 10)podziyesa kuti mumadzikhulupilira bwanji pochita zinthu ndipochita chisankho china chiri chonse, mungadzipatse maliksiangati? Afunseni anzanu ngati akugwirizana ndi malikisimwadzipatsawo. Ngati munadzipatsa malikisi ochepa, mungachitechiyani kuti muyambe kumadzikhulupirira kwambiri? Ngatimunadzipatsa ma malikisi ochuluka kwambiri, mungatani kutimudzionesetsa kuti mukumamveranso zonena kapena maganizo aanthu ena.

• Lembani mndandanda wa zinthu zonse za bwino zokhudza inueni monga; Ndine opatsa, ndine wanthabwala, ndimatha kupezamayankho amavuto amene ndi makumana nawo, ndimavinabwino, ndimatha kulima, ndimatha kusewera bwino mpira,ndimatha kukamba nthano ndi ana. Mndandanda umenewumuuike pamalo amene mukhoza kumauona nthawi zonse ndipomukakumbukira zinthu zina muzikaonjezera pa mndandandaumenewu.

• Kodi ndi chachilendo anyamata ndi atsikana kumangochezaosachita zogonana? Kodi mukuganiza kuti zimenezi ndi za bwinokuti zizichitika kawirikawiri? Ngati ziri za bwino, taganiziranimitundu iwiri kapena itatu ya masewero amene mungachitirelimodzi (atsikana ndi anyamata) sabata ino. Pamapeto a sabata inokambiranani zimene mwaphunzira pokhala pa gulu limodzi ndianyamata kapena ndi atsikana.

Page 137: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndinatengapo matenda opatsir-ana pogonana – Kodi sindizabereka

Okondedwa Eda

Kukanakhala kuti chibwenzi chako chakalecho sichinakuuze kutichinali ndi matenda opatsirana pogonana, iweyo sukanadziwamsanga kuti nawenso unatenga matendawa. Koma chifukwaunalandira chithandizo chamankhwala msanga, ndi kotheka kutiulibe vuto lina liri lonse.

Amai samadziwa kuti ali ndi matenda opatsirana pogonanachifukwa matendawa samaonekera msanga kwa munthu wa maindi mmene Chauta analengera thupi la mkazi. Ngati salandiramsanga chithandizo cha mankhwala njira za chiberekerozimaonongeka ndipo izi zimachititsa kuti munthu akhaleosabereka.

Kukhala ndi matenda opatsirana pogonana pafupipafupi,kumachititsa kuti munthu adzakhale osabereka komanso kutiatenge HIV mosavuta. Kudziteteza kwake ndi kugwiritsa ntchitokondomu nthawi zonse pogonana.

Pali zifukwa zambiri zimene zimachititsa munthu kuti akhaleosabereka osati matenda opatsirana pogonana okha ayi. Ukafunakudziwa zambiri kafunse kwa alingizi a za umoyo, ku Banja LaMtsogolo komanso zipatala zina za boma.

Nthawi zambiri ngati banja likulephera kubereka mwana, anthuamanena kuti mai wa mnyumbamo ndiye amene ali ndi vuto. Izisizoona ayi chifukwa vutoli litha kupezeka mwa a mayi kapena abambo Tiyenera kuwathandiza ndi kuwaonetsa chikondi Ma banjaamene samabereka. Tisamawasale.

Ndiri ndichikhulupiriro kuti wathandizidwa

Auntie Stella

©TARSC

7

AF7

Page 138: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB7

• Kodi anthu amawaganizira zotani amuna amene sabereka? Nangaamai amene sabereka amaganirizidwa zotani? Mukhale ndimitundu iwiri ya mayankho. Wina ukhale wa amuna ndipo winaukhale wa amai. Kodi ndi ndani amene anthu amamumverachisoni pakati pa mwamuna ndi mkazi? Kodi mukuganiza kuti ndichifukwa chiyani izi zimakhala chonchi?

• Kambiranani njira zimene mungathandizire anthu amenesamabereka. Kodi mungachite chiyani kuti musinthe mchitidweoipa wa anthu am’dera lanu womaseka anthu amene sabereka?

• Kodi inu ndi wokondedwa wanu mutakhala kuti mukulepherakubereka, mungaganize zotenga mwana amene alibe makolo kutimudzikhala naye ngati wanu? Fotokozani chifukwa chake. Kodianthu a m’dera lanu amaopa chiyani kutenga mwana wa masiyekuti adzikhala naye ngati wawo, makamaka mwana amene si wam’bale wawo?

• Onani kadi 13 ndi 25 kuti mudziwe zambiri za matendaopatsirana pogonana

Page 139: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Aphunzitsi anga akufuna kutiadzigonana nane

Okondedwa Cecelia

Iwetu sukulakwa kukana kuchita zogonana ndi a phunzitsi ako.Zimene akuchita a phunzitsi akozi ndi zolakwika kwambirikomanso ndi za ufiti. Anthu ambiri akhoza kugwiirizana nane kutimphunzitsi ameneyu sayenera kuphunzitsa pa sukulu ina ili yonsem’dziko muno chifukwa cha khalidwe lake loipali. Chomwendingakupemphe Cecelia ndi chakuti usasiye kumakaphunziranawo phunziro limeneri. Koma uyenera kuchitapo kanthu msangazinthu zisanafike poipa. Kugwiriridwa kwa mtundu wina ulionsendi koletsedwa ndi malamulo a dziko lino. Uyenera kuululazimene zinakuchitikirazi pomuuza mnzako kapena kuwauza aphunzitsi anu ena aliwonse kuti akuthandize.

Ngati ukuona kuti palibe amene angakuthandize, ndi bwino kutiupeze mnzako amene ayenera kudziwa za vuto lakoli.Udzionetsetsa kuti mnzako ameneyu nayenso adzikhalira pamenea phunzitsi ako akakuwuza kuti utsalire. Ngati aphunzitsi akoangalimbikile kuti utsalire wekha, mnzakoyo adzionetsetsa kutisanapite kutali kuti adzitha kumamva zimene adzikambaaphunzitsi akowo. Ngati aphunzitsi akowo ayambanso kuchitazomakugwiragwira kumaliseche, udzakuwe ndipo mzakoyoadzakhala mboni yako. Ndipo nthawi yomweyo ukanene kwa aheadmaster anu ndi kukaitula nkhaniyi ku Polisi, kumabungwemonga a YONECO ndi ena onse amene amathandiza ana ameneamachitiridwa nkhaza zosiyanasiyana monga zogwiriridwa

Auntie Stella

©TARSC

8

AF8

Page 140: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB8

• Ngati mphunzitsi wina aliyense kapena wachikulire wina aliyenseakuchitirani zinthu za mtundu umenewu, onetsetsa kuti mwauzamnzanu kapena munthu amene mumamukhulupirira ndipoonetsetsani kuti mwakanena ku Polisi msanga

• Mukhozanso kupeza chithandizo choyenera pogwiritsa ntchitonjira ya “Helpline” yomwe mabungwe ena monga YONECO ndiBanja La Mtsogolo amagwiritsa ntchito. Mukhozanso kukapezachithandizo ku mabungwe amene amagwira ntchito mdera lanu(ma CBO) komanso kwa anthu amene amagwira ntchitozothandiza a Polisi (community Polisi)

• Gwirizanani ndi anzanu kuti muitanitse a Polisi kapena anthu enaamene amagwira ntchito yothandiza a chinyamata kuti abwere pasukulu panu adzakufotokozereni zina ndi zina zokhudzamtchitidwe wogwirirana komanso nkhanza zina za mtunduumenewu.

Page 141: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Mnzanga ndi wamakhalidwe ogonana amuna okhaokha

Okondedwa Samuel

Ngakhale zinakudabwitsa zimene Misheck anakuuza, zinthuzimene zimakuchititsa kuti akhale mnzazo sizinasinthe. Palibechifukwa chakuti usiyire kumacheza naye ayi. Sichapafupi kutimunthu amuuze mnzake kuti iye amangofuna kukhala mchikondindi anyamata anzake basi. Izi zikusonyeza kuti Misheckamakudalira kwambiri.

Iweyo ungomuuza Misheck kuti suli ngati iyeyo ndipo chifukwacha ichi sungathe kukhala mwamuna wake. Umuuze mwachikondindipo iye adzamvetsetsa. Ngati ungathe, umuonetsa kuti zimenezisizisokoneza mgwirizano wanu.

Umuthandize kuti akuuze zambiri zimene akukumana nazo.Anthu ambiri otere amasowa anthu omakamba nawo za kukhosi.Izi zimachitika ngati anthu ambiri savomereza za makhalidweotere.

Chiri chonse chimene ungaganize pa za mgwirizano wako ndiMisheck usauze munthu wina aliyense. Iye mwini ndi ameneangaganize zouza munthu wina wa ku mtima kwake. Anthuambiri savomereza za mchitidwe ngati uwu choncho adzayambakumamulankhulira kapena kumuchitira zosakhala bwino. Ichi ndichifukwa anthu ngati Misheck safuna kubwera poyera. Micheckndi mnzako ndipo asoweka chithandizo chako.

Auntie Stella

©TARSC

9

AF9

Page 142: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB9

• Kodi mukuganiza bwanji za mmene Auntie Stella ayankhira?

• Kodi Samuel atha kuchita zimene Auntie Stella anena?

• Tangoganizani kuti munthu wina aliyense anali ochita zogonanandi mamuna kapena mkazi mnzake ndipo inu nokha simunalichoncho. Kodi anthu bwenzi akukunenerani chiyani? Ndipomukanawatsimikizira bwanji kuti izi sizolakwika? Mukudziwabwanji? Mukanamva bwanji anthu akumakunyazani?

• Kodi inuyo ngati simuli ngati Misheck, ndi koyenera kuti mudziwezambiri za anthu ngati amenewa? Kodi ndi chiyani chimenemungafune kudziwa kuti mukhale munthu ovomereza zamakhalidwe ngati a Misheck? Kodi inuyo ndi achinyamata anzanu,mungachite chiyani kuti muthandize anthu ambiri kuvomereza zamakhalidwe ngati a Misheck?

• Taganizani za magulu ena a anthu (monga anthu osauka, olumala,odwala matenda a Edzi) amene amasalidwa ndi kunzunzidwamnjira zosiyanasiyana. Kodi ndi chifukwa chiyani anthu amachitirazimenezi?

Page 143: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Chibwenzi changa chiri ndi Mimba

Okondedwa Zalimba

Nthawi zambiri timazindikira kulakwa kwathu pamene tachitachinthu cholakwika. Choyenera kudziwa ndi chakuti munthu winaaliyense amalakwa. Anthu ena amalakwa kwambiri kuposa anthuena. Ndipo zinthu za mtundu umenewu zikachitika, ndi bwinokuvomereza ndi kufunafuna njira ya bwino yothetsera kulakwakwathu kapena vuto lathu.

Malingana ndi mmene zinthu zachitikiramu, malangizo aja abambo ako sangagwirenso ntchito koma choyenera kuchita ndichakuti ukambirane ndi chibwenzi chakocho kuti mupeze njirayabwino imene ingakuthandizeni nonse. Uyeneranso kuti upezenthawi yokuti ukambirane ndi azakhali ako kuti akawafotokozeremakolo a chibwenzi chako komanso abambo ako za zimenewachitazi. Sindikudziwa kuti akailandira bwanji nkhani imeneyi,komabe zivute zitani ayenera kuidziwa nkhani imeneyi chifukwamwana mukuyembekezerayo ndi wako basi ndipo adzasowachikondi ndi chisamaliro chako. Udindo umenewu siwachibwenzichako chokha ayi.

Ndiri ndi chikhulupiriro kuti ukwanitsa kumaliza maphunziro akondi kudzakhala bambo odalirika. Ndiri ndi chikhulupirironso kutimwana wako akadzakula udzidzamuthandiza kuti adzakule bwinondi kudzakhala munthu ochita chisankho chabwino nthawi zonse.

Auntie Stella

©TARSC

10

AF10

Page 144: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB10

• Kodi mukudziwapo wa chinyamata wina aliyense amene analowam’banja kapena anabereka mwana akadali pa sukulu? Kodizimenezi zinawakhudza bwanji?

• Chitani sewelo: Khalani anayi anayi; Chitani sewero loonetsaZalimba ndi malume ake kapena azakhali ake akufotokozeramakolo a Zalimba za zimene za chitikazi. Kodi awafotokozerabwanji makolo a Zalimba? Kodi a bambo kapena amai a Zalimbaanenapo ndi kuchita chiani?

• Kodi makolo anu amakupatsani malangizo otani? Kodimumawamvera? Ngati simumawamvera fotokozani zifukwa zake?

• Taganizirani za nthawi imene munachita chinthu choopsakwambiri monga kuyenda usiku kwambiri muli nokha nokha,kuledzela kwambiri kapena kuchita zogonana mosadziteteza.

a) Munachitiranji zimenezi?b) Kodi zotsatira zake zinali za bwino kapena zoipa?c) Kodi ndi zisankho zina ziti zimene munali nazo?d) Kodi khalidwe limeneri mumachita kawirikawiri?

Page 145: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndimakhala ndi chilakolakochofuna kugonana ndi mtsikana pafupipafupi

Okondedwa Yohane

Usamadandaule chifukwa sichachilendo kuti anyamata adzitotapafupipafupi ndikukhala ndi chilakolako chofuna kugonana ndimtsikana akamaganiza za mkazi. Njira yophweka yothetseravutoli ndi kubunyula komatu uyenera kumabunyula kwa wekhakwakuti munthu sangakuone.

Kubunyula ndi kudzisangalatsa wekha pomadzigwira gwirakumaliseche kuti utote kwambiri mpaka utulutse umuna. Panthawi imeneyi munthu umamva kutsekemera thupi lonse.Mnyamata akamabunyula ndipo akafika pa chimake, chokodzerachake chimatulutsa umuna. Mtsikana akamabunyula nafika pachimake, maliseche ache amafufuma komanso amanyowa.

Aliyense kaya mnyamata kaya mtsikana amamva kukomaakamadzigwiragwira ku maliseche. Nthawi zina akuluakulu ameneali pa banja nawonso amatha kubunyula ngati njira imodziyodzitetezera ku matenda ( amagwiranagwira kumaliseche kutiasangalatsane mpaka mwamuna atatulutsa umuna komanso mkaziatatulutsa chikazi) .

Kubunyula kulibe vuto lina liri lonse pa thupi lathu. Kubunyulakumathandiza kuti uthetse chilakolako chogonana ndipo ndi njirayabwino yodziwila mmene thupi lako limagwirira ntchito. Anthuamisinkhu yonse kaya osakwatira kaya okwatira amabunyula.

Ngakhale azipembedzo zina amanena kuti kubunyula ndi tchimo,aliponso adzipembezo zina amene amapereka ufulu kwa anthuotsatira zipembezo kuti adzidzisankhira chochita.

Auntie Stella

©TARSC

11

AF11

Page 146: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB11

• MAYANKHO

Ziganizo zonse ndizabodza kupatulako chiganizo chachiwirichokha. Kodi ndi zinthu zina ziti- kaya zabodza kaya zoonazimene munamvapo zokhudza kubunyula? Kodi mwa zinthuzimenezi, zoona zenizeni ndi ziti?

• Kodi anthu a mdera lanu amaganiza zotani za kubunyula? Kodiamaona kuti kubunyula ndi kwabwino pa moyo wa munthukapena amaona kuti ndi koipa. Kodi maganizo awowa amafananaakamanena kubunyula kwa anyamata ndi kwa atsikana. Kodianthu amamasuka akamanena za kubunyula kapena amaitengankhaniyi ngati ya chinsinsi. Ngati mukuganiza kuti achinyamataamayenera kukhala omasuka ndi kumakhala ndi maganizo abwinookhudza kubunyula, kambiranani zimene achinyamata angachitekuti izi zitheke.

• Nthawi zambiri achinyamata amakhala ndi chilakolako chofunakugonana. Kupatulapo kubunyula komwe mwakambirana kale, ndichiyaninso chimene achinyamata angachite kuti athetsechilakolakochi mosagonana ndi mkazi kapena myamata. Lembanimndandanda wa maganizo anu (monga kukathamanga mtundawautali) ndipo inu mudzisankhire njira zokukomerani

Page 147: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi sindiyenera kumagonananaye ngakhale ndimamuthandizamu njira zosiyanasiyana?

Okondedwa Themba

Nthawi zambiri chibwenzi sichimayenda bwino ngati inu amene mulipaubwenzi mukufuna kumapeza zinthu kuchokera ku chibwenzi ndipopa nkhani yakoyi zikuonekeratu kuti mchitidwe wogonana ndiwofunikira kwambiri kwa iwe kuposa kwa chibwenzi chako. Uyenerakudziwa kuti ndi atsikana ochepa amene amafuna kumachita zogonanaakakhala pa chibwenzi. Atsikana ambiri samasangalala anyamataakamawavutitsa kuti adzigonana nawo ngati njira imodzi yothokozera kumphatso zimene amalandira

Anyamata ndi atsikana ambiri amayesetsa kupewa mavuto ameneamabwera chifukwa cha mchitidwe wogonana munthu usanakhwimemsinkhu monga kukhala ndi mimba zosakonzekera, matenda opatsiranapogonana monga chindoko komanso kachilombo ka HIV. Chonchoatsikana ndi anyamata amenewa amadziletsa kwa thunthu ku mchitidwewogonana. Iwo amadikira mpaka atadzakula nalowa m’banja.

Mwina ndikufunse, kodi cholinga cha chibwenzi ndi kugonana basi?Kapena kukhala ndi mnzako weniweni amene amakukonda ndikuganizira za moyo wako nthawi zonse? Ngati ukufuna kukhala ndichibwenzi cha mtundu umenewu uyenera kuyamba kulemekeza zimenechibwenzi chako chimafuna. Usiye kumamukakamiza kuti udzigona nayechifukwa iye samafuna kuchita mchitidwe woipawu.

Anthu ena amaganizabe kuti cholinga chokhalira pa chibwenzi ndiatsikana ndi chomangogonana nawo basi. Anyamata amatengedwakukhala a pamwamba kuposa atsikana. Koma masiku ano zinthuzikusintha chifukwa anyamata ndi atsikana amaonedwa chimodzimodzi.Ndiri ndi chikhulupiriro kuti tsopano usiya za kale ndi kuyambakumuona bwenzi lako ngati mnzako ndipo mudzakhala moyowosangalala.

Auntie Stella

©TARSC

12

AF12

Page 148: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB12

• Mukuganiza zotani pa yankho limene apereka Auntie Stella? Kodimukugwirizana nazo zimene amuuza Themba? Ngatisimukugwirizana nazo, malangizo anu ndi otani?

• Atsikana: Lembani mndandanda wa zinthu zimene anyamataayenera komanso sayenera kuchita ngati akufuna kukhala ndichibwenzi chopambana?

Anyamata: Lembani mndandanda wa zinthu zimene atsikanaayenera komanso sayenera kuchita ngati akufuna kukhala ndichibwenzi chopambana?

• Tsopano sinthanani, anyamata atenge mndandanda umeneanalemba atsikana ndipo atsikana atenge mndandanda umeneanalemba anyamata. Pangani gulu limodzi ndipo mufunsanemafunso kuti mudziwe zambiri zimene anzanu amaganiza

• Tsopano chitani mtsutso pa mutu umodzi mwa mitu iyi:

– Mtsikana ayenera kugonana ndi chibwenzi chakeakamugulira zinthu

– Chikondi chosagonana chiri ngati kumwa tiyi opandashuga. Mukugwirazana nazo?

– Sibwino kugonana musanakwatirane.

Page 149: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndili ndi zotupa pa chokodzerachanga!

Okondedwa Kondwani

Wachita bwino kulemba kalatayi. Zotupa kumaliseche amwamuna kapena mkazi zitha kungokhala zotupa ngati mmenemunthu amakhalira ndi ziphuphu kunkhope komanso chithakukhala chizindikiro chamatenda opatsirana pogonana.

Ngati sunachitepo zogonana, zitha kutheka kuti simatendaopatsirana pogonana. Koma ngati wagonanapo ndi aliyenseposachedwapa mosadziteteza utha kukhala ndi matendawa ndipoatha kukhala mauka, chizonono, mabomu kapena chindoko.Aphunzitsi ako ayenera amanena chizonono chifukwa munthuamapengadi ngati sachizidwa msanga. Chimene ndinganene ndichakuti upite kuchipatala mwamsanga kuti akakuone ngatidi ulindi matenda opatsirana pogonana. Izi zikuthandiza kuti ulandirechithandizo cha mankhwala oyenera.

Akakakuuza kuti uli ndi matenda opatsirana pogonana, ndi bwinoumuuzenso yemwe unagonana naye kuti nayenso akayezetse.Nthawi zambiri akazi atha kukhala ndi matendawa komaosaonetsa zizindikiro zilizonse.

Pita kuchipatala msanga (monga ku Banja La Mtsogolo) chifukwamatenda ambiri opatsirana pogonana amachizika tikalandilachithandizo msanga. Utha kupita ndi munthu wina wamkulu ngatikuchipatala amakalipira kapena samawathandiza achinyamata.Dziwa kuti uli ndi ufulu wolandira chithandizo mopandakulalatilidwa. Zabwino zonse!

Auntie Stella

©TARSC

13

AF13

Page 150: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB13

• MAYANKHO: MATENDA OPATSIRANAPOGONANA

Ziganizo 1 ndi 5 ndi zoona ndipo ziganizo 2, 3 (kudziletsansokumathandiza) ndi 4 (matenda opatsirana pogonanaosiyanasiyana ali ndi zizindikiro zosiyana ndipo akazi nthawizambiri saonetsa zizindikiro msanga) ndi zabodza.

• NTCHITO: Pezani mabuku kapena zolemba zilizonse zimenezikufotokoza za matenda opatsirana pogonana. Gulu lililonselisankhe nthenda yopatsirana pogonana imodzi ndipomukawerenga mukonzekere kufotokozera anzanu. Muwauzeanzanu zinthu izi:

– Kodi dzina la nthendayo ndi chiyani? – Kodi zizindikiro za nthendayo ndi ziti (kwa amuna

komanso kwa akazi)?– Kodi ingachilitsidwe bwanji?– Kodi ingapewedwe bwanji?

Kenako lembani mafunso asanu kapena khumi okhudza matendaopatsirana pogonana ndipo mulembe mayankho ake papepalalosiyana ndi lamafunso. Apatseni anzanu a gulu lina mafunso ajakuti ayankhe ndipo inunso yankhani mafunso awo. Mutachonga,amene wayankha zambiri bwino ndani, inu kapena anzanu?

• Itanitsani namwino kapena ogwira ntchito za umoyo kutiadzakuuzeni zambiri zokhudza matenda opatsirana pogonanakomanso ufulu wanu wolandira chithandizo mosalalatilidwa.Fufuzani ngati achinyamata amalandilidwa bwino kuchipatalachimene muli nacho pafupi ngati wapita ndi matenda opatsiranapogonana. Ngati amalalata kapena kukalipa, kodi titani kutitithetse kuphwanyirana ufulu kumeneku? Kodi ndi ndaniangatithandize?

Page 151: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Mwina ndili ndi kachiromboka HIV

Okondedwa Florence

Pepa Pepa kuti wakumana ndi vuto limeneli. Koma ndatindikuyamikire chifukwa chopanga chisankho chanzeruchokayezetsa magazi kuti udziwe ngati uli ndi kachilombo ka HIV.Izi zikuonetsa kuti ndiwe wolimba mtima ndipo umapangazisankho zoyenera m’moyo mwako. Ndibwino kudziwa ngati ulindi kachirombo ka HIV kusiyana ndikumakhala ndi nkhawa.

Ukapita kukayezetsa ku HTC (HIV Testing and Counselling),phungu wophunzitsidwa bwino akakulandira bwino, akakupatsauphungu asanakuyeze komanso akakamaliza kukuyeza,akakuyankha mafunso ako onse mwansangala ndipoakakuthandiza kupanga chisankho choyenera malingana ndizotsatira za kuyezetsa magazi, kaya uli ndi kachilombo ka HIVkapena ayi. Chilichonse chimene ukakambirane naye ndichachinsisi ndipo sangauze munthu wina aliyense kotero kutisukusoweka kumuuza dzina lako.

Oyeza magazi akatenga magazi pachala chako ndi kuwayezanthawi yomweyo ndipo akakawuza zotsatira pakangotha mphindizochepa. Koma ngati unagonana ndi mwamuna mosadzitetezamiyezi itatu yapitayo, ndi bwino kuti udzayezetsenso kachiwiripakapita miyezi yochepa chifukwa kachirombo ka HIV kamatengapafupifupi miyezi itatu kuti kaonekere mmagazi a munthu.

Chonde mulimbikitse bwenzi lako kuti nayenso akayezetse kutiadziwe ngati ali ndi kachilombo ka HIV ndipo ngati sapita ndipoakulimbikira kuti sangavale kondomu, ndiye uli ndi udindo odziwachochita pawekha. Ngati angakupeze kuti ulibe kachirombo,uonesetse kuti ukukhala moyo wa bwino ndipo usadandaulensozankhaniyi.

Zabwino zonse kwa iwe ndi bwenzi lako.

Auntie Stella

©TARSC

14

AF14

Page 152: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB14

• Kodi Florence akapita kukayezetsa magazi ndikupezeka kuti alibekachirombo ka HIV, mungamulangize zotani kuti asatengekachiromboka? Kodi angafune chithandizo chotani?

• Lembani mndandanda wazifukwa zimene anthu samafunakudziwa ngati ali ndi kachirombo ka HIV kapena ayi? Ndipomulembenso mndandanda wina wa zifukwa zimene anthuayenera kuyezetsa magazi kuti adziwe ngati ali ndi kachirombokapena ayi?

• Kodi ndi mndandanda uti umene uli ndi zifukwa zambiri? Kodimunthu amene akuganiza zokayezetsa magazi, mungamulangizezotani?

• Fufuzani kuti kodi malo amene muyenera kuyezetsa magazi alipafupi bwanji ndi kumene mukukhala ? Kodi amalipilitsa? Kodiamapereka malire a zaka za anthu oyenera kukayezetsa kapenaaliyense atha kupita?

• Kodi munagonanapo osagwilitsa ntchito kondomu? Ngatimunagonanako, bwanji mupite mukayezetse magazi anu kutimudziwe ngati muli ndi kachilombo ka HIV kapena ayi? Kodimumafuna chilimbikitso chotani kuti mukayezetse magazi?Limbikitsanani pakati panu!

• SEWERO: Wina akhale Florence ndipo wina akhale bwenzilake la Florence. Florence amuuze bwenzi lake kuti ali ndinkhawa kuti mwina ali ndi kachirombo ka HIV ndipoakumulimbikitsa bwenzi lakeyo kuti akayezetse magazi.

• Ngati bwenzi la Florence likukana, kodi Florenceangamunyengelere bwanji bwenzi lake kuti mpaka aloleakayezetse?

• Werengani Khadi 26 kuti mumve zambiri zokhalamchiyembekezo ndi moyo wathanzi pamene uli ndi kachilomboka HIV.

Page 153: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndikuwopa khansa yam’chiberekero!

Okondedwa Lusibiro

Wachita bwino kufunsa, Lusibiro! Nthenda ya khansa yam’chiberekero imagwira khomo lachiberekero. Amai ambiri alindi nthenda imeneyi m’Malawi muno. Ngakhale izi ziri chonchi,ndi amai ochepa okha amene amadziwa za nthendayi. Munthuakadziwa msanga kuti ali ndi nthendayi nalandira chithandizo chamankhwala msanga, munthu amatha kuchiriratu ku nthendayi.

Khansa yamchiberekero itha kuyamba pa zifukwa izi:

– Ngati ayamba mchitidwe ogonana akadali wamng’ono(zaka zoyambilira atangotha kumene msikhu)

– Ngati wagonana ndi anthu ambiri

– Ngati amene akugonana naye wagonana ndi anthu enaambiri

– Ngati ali ndi mauka

– Ngati ali ndi HIV kapena Edzi

Azimai ena ngakhale ali ndi zaka zochepera 20 akupezeka ndikhansa yamchiberekero. Kodi ndi koyenera kugonana mudakaliachichepere? Ngati mwayamba mchitidwe ogonana ndi bwinochaka chilichonse kuyezetsa ngati muli ndi khansayamchiberekero. Ngati simungakwanitse chaka chimodzi ndibwino kuyezetsa zaka zitatu zili zonse. Zipatala zowerengekazimayeza ndipo ngati muyezetsa mwachangu palibe chifukwachakuti mzimai amwalire chifukwa cha khansa yamchiberekero.Kafunseni kwa alangizi a za umoyo a m’dera lanu za nkhaniyi

Auntie Stella

©TARSC

15

AF15

Page 154: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB15

• Mwaphunzira zotani zokhudza khansa yamchiberekero?Kambiranani ndi anzanu kapena abale anu a akazi. Auzenizakufunika kwa kuyezetsa ngati munthu ali ndi khansa kapena ayi.

• Werenganinso kalata imene alemba Auntie Stella kuseri kwaKhadi ili. Kodi mukuganiza kuti muli pa chiopsezo chakutimukhoza kukhala ndi khansa ya m’chiberekero? Fufuzani zambirizokhudza khansa ya m’chiberekero ndikufunika koyezetsapafupipafupi.

• Mukhoza kuitana namwino kuti adzakufotokozereni zambirizokhudza khansa ya m’chiberekero.

• Mukhonzanso kuwerenga mabuku kapena kupita kuchipatala kutimudziwe zambiri. Lembani zimene mwapeza ndipomuwauzekonso anzanu ndi abale anu.

Njira yodutsira dzira la akazi

Malo opangira dzira la akazi

Chiberekero

Khomo la chiberekero

Maliseche a mkazi

Page 155: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndinagwiriridwapo

Okondedwa Regina

Nkhani yako ndiyomvetsa chisoni kwambiri! Zimene anachitaamalume ako ndi zolakwika. Anaphwanya lamulo ndipo akuyenerakulangidwa ndi kukaponyedwa kundende.

Usachite mantha ndipo usabise. Uwadziwitse makolo ako kapenawachibale aliyense yemwe ukumukhulupilira kapenanso ukhozakukanena ku polisi. Pamenepa pakufunika munthu wakutiakuthandize ndikukulangiza kuti mpaka nkhani ikafike kupolisi.

Mtsikana ngati iwe ukagwiliridwa ndi bwino kukanena ku polisinthawi yomweyo usanasambe mthupi ndiponso usanasinthezovala ndi cholinga chakuti ukapereke umboni woyenera kupolisi. Ndi bwinonso kupita kuchipatalakuti akakuteteze kutiusatenge mimba pogwiritsa ntchito mankhwala amene munthuamamwa ngati wa gwiriridwa ndi cholinga chakuti asatengemimba ndi HIV

Kugwiliridwa sivuto la munthu wogwiliridwa ayi! Koma mongamunthu wamkazi ndi bwino kupewa mchitidwewu popewakuyenda wekha malo amene sukuwadziwa bwino, kumwa mowakwambiri kapena kusuta chamba. Ngati uli pachibwenzi ndimnyamata muuze malire achibwenzi chanu musanayambezogwiranagwirana kapena kugonana. Munthu aliyense akafunakukugwilira udzikuwa, kumuluma, kumumenya ndi bondo kapenamkono pakati pamiyendo yake, ndikuthawa.

Ndikukhulupilira kuti ndakuthandiza Regina.

Auntie Stella

©TARSC

16

AF16

Page 156: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB16

• Kodi ndi chifukwa chiyani kugwiriridwa komanso nkhanzazimachitika kwambiri kwa amayi ndi atsikana? Kambirananipagulu lanu. Payankho lililonse limene mupereke mudzifunse kutindi chifukwa chiyani? Mukhonza kufunsa chifukwa chiyani kwamayankho onse amene mungapeze.

• Fufuzani zambiri zokhudza mankhwala amene munthu angamwengati wagonana mosayembekezera kapena wagwiliridwa (morningafter pill) ndi mankhwala oteteza kuti munthu asatenge HIV ngatiwakhudzana ndi magazi a munthu osamudziwa ngati ali ndikachirombo kapenanso ngati wagwiliridwa (post-exposureprophylaxis – PEP)

Kodi m’dera lanu muli m’chitidwe wogwililirandi wankhanza ngati uwu? Werengani ziganizo zotsatirazi ndipo muone ngati zikufotokozadizochitika m’dera lanu. Lembani ZOONA kapena ZABODZA pambuyopa chiganizo chilichonse molingana ndi mmene mukuonera inu.

1 M’dera lathu atsikana ndi amai atha kuyenda paliponse, nthawiiliyonse popanda kuopa kuchitidwa nkhanza.

2 Mdera lathu anthu sabisa nkhani zakugwililira ndi nkhanza.Aliyense akangoulula kuti wagwililidwa, akuluakulu amachitapokanthu kuti zisadzachitikenso. Palibe amene angamunenewogwililidwa kuti ndi vuto lake ayi.

3 Ngati wa chinyamata aliyense wagwililidwa, achipatalaamathandiza moyenera ndipo apolisi amachita zotheka kutiamugwire munthu wogwililirayo ndi kumuimba mlandu.

4 Anyamata amalemekeza atsikana ndipo mtsikana akati sakufunazogonana, mnyamata amadziwa kuti mtsikanayo akukanadindipo samamukakamiza chifukwa anyamata a m’dera mwathuamatha kudziletsa.

Zotsatira: Ngati anthu ochepa okha mwainu mwayankha kutiZOONA paziganizo zili m’mwambazi, kodi titani kuti madera amenetikukhala akhale opanda nkhanza ndipo opanda kugwililira?

Page 157: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi ndiyambe kuchita uhulekuti ndipeze ndalama?

Okondedwa Janet

Vuto lakoli ndilovuta kwambiri ndipo uyenera udziwe kuti kuchita uhulekuti upeze ndalama zingokupezetsa mavuto ena ambiri. Amuna ambiriamene amapereka ndalama kuti agonane ndi mkazi amakana kugwiritsantchito kondomu kotero kuti ukhoza kutenga mimba, kachirombo kaHIV kapena zonse zimene. Akhonzanso kukugona osakupatsa ndalamandikukumenyanso.

Uhule, kapena kuti mchitidwe osinthitsa kugonana ndi ndalamandiwoletsedwa pa malumolo a dziko lino. Chilichonse chitachitika ndipoapolisi atadziwa kuti umapanga uhule, akhoza kukumangandikukutsekera mndende. Usayerekeze kupanga zimenezi chifukwazingokubweretsera mavuto ambiri.’

Chimene ungachite ndikuganinzanso njira zina zoyenera zopezerandalama kapena upeze munthu kaya bungwe limene lingakuthandizekokukulipilira sukulu ndi mayeso. Ufufuze bwino bwino kaya kwa anzako,kuchipembezo chako, kudera kumene ukuchokera ndikwina kulikonsekumene angathandize. Dziwanso kuti Unduna wa Amai ndi anaumapereka chithandizo kudzera ku nthambi yoyang’anira za umoyo waanthu limene pachingerezi amati Social Welfare. Ungopita kumaofesiaboma a m’boma la kwanu ndipo akakuthandiza.

Ngati zonse zalephereka dziwa kuti simathero a zonse ayi. Ukhozakuphunzira luso lililonse kuti uzizipezera wekha ndalama kapenakupanga ganyu kumene umakhala. Anthutu amatha kuphunzira ngakhaleatakula bola chidwi ndi kulimbikira kuwerenga.

Ukadzafuna kugonana, udzagonana mwakufuna kwako koma osatichifukwa ukufuna ndalama ayi. Ndipo uonetsetse kuti ukudziwa njirazonse zopewera mimba ndi kupewa kutenga kachilombo ka HIV mongakugwiritsa ntchito makondomu abambo ndi amai amene, mankhwalaolerera ndi njira zina.

Zabwino zonse!

Auntie Stella

©TARSC

17

AF17

Page 158: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB17

• SEWERO: Khalani awiriawiri ndipo pangani kasewerokakang’ono. Janet akupempha malangizo kuchokera kwa munthuwamkulu kuti amuthandize mmene angapezere ndalama zasukulu. Kenako sinthanani wina akhale Janet ndipo wina akhalemunthu wamkulu.

• Mukatero, muwauze anzanu ena kuti munamva bwanji kukhalaJanet. Kodi chimene chinali chovuta kapena chosavuta ndi chiyanipopempha chithandizo. Kodi mungapereke malangizo otani kwamunthu ngati Janet?

• Pangani mtsutso pa mutu uwu:

‘ Atsikana ambiri samayamba uhule chifukwa chakutiakusangalala koma chifukwa chosowa ndalama zakuti athekudyetsa ndi kuveka mabanja awo ndi azibale awo’

• Nthawi zambiri anthu amanyoza ndi kudzudzula amene amachitauhule koma samadzudzula amuna amene amapereka ndalamakwa atsikanawa ndikumagonana nawo. Kodi mukuganiza kuti ndichifukwa chiyani izi zimachitika chonchi? Kodi ndi bwino? Ngatisibwino, kodi anthu angachite chiyani kuti athetse mchitidweumenewu?

• Pangani kafukufuku wa malamulo okhudzana ndi akazi ameneamachita mchitidwe wogonana kuti apeze ndalama? Nangamalamulowo amanena chiyani za anthu amene akulipirandalamazo kuti agonane ndi akaziwo? Kodi akazi amenewa ali ndiufulu wawo wa chibadwidwe? Kodi inu mukuganiza kutichiyenera kuchitika ndi chiyani

Page 159: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndimatulutsa umuna ndikagonausiku

Okondedwa Edison

Pepa kuti wavutika chifukwa chaumuna umene ukumatulukaukagona. Osadandaula popeza kuti palibe chilichonse chovutandipo thupi lako lili bwinobwino, choncho palibe chifukwachochitira manyazi.

Kutulutsa umuna usiku ukagona ndi chizindikiro chakuti tsopanothupi lako likuchoka kuumwana ndipo likukhwima. Nthawiimeneyi, thupi limasintha ndipo mnyamata amayamba kutulutsaumuna. Panthawi imeneyi thupi lako ndilokonzeka kutulutsaumuna ndipo njira imodzi ndiyotuluka usiku utagona ngakhalekuti sunalote ukugonana. Zimathekanso kuti mnyamataamapezeka wadzuka atamema (kutota) ndipo sizitanthauza kutiamalota akugonana ayi.

Izi zimachitika kwambiri kwa achinyamata apakati pa zaka 13 ndi19 ngakhale kuti izi zitha kumachitika ngakhale utakula. Chonchoosada nkhawa kuti izi zidzaononga ubwenzi wako ndi mkaziwako ukadzakwatira, ndi mmene matupi athu amasinthira, palibechodandaulitsa pamenepa. Utha kufunsa munthu aliyensewamkulu yemwe umamukhulupilira kuti akutsimikizire.

Auntie Stella

©TARSC

18

AF18

Page 160: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB18

• Pitilizani ziganizo zotsatira:

a) Ndimasangalala thupi langa likamasintha ndikamakulachifukwa chakuti…

b) Koma zinthu zina zimene zikusintha nthupi mwangasindisangalala nazo chifukwa chakuti…

Auzeni anzanu agulu lina zimene mwakambirana

• Kodi mwaphunzira chiyani kuchokera pazochita zimenezi? Kodipali zina zimene mukufuna mutadziwa kwambiri? Pezani njira yabwino yochitira zimenezi.

• Kodi mulinso ndi nkhawa pa zinthu zimene zingakuchitikirenimthupi lanu makakamaka pamene mukukula? Mukhozakukambirana ndi anzanu kapena munthu aliyense wamkhuluyemwe mukumukhulupilira.

Page 161: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi ma ARV ndi chiyani?

Okondedwa Thandi

Inde ndi zoona kuti ma ARV amathandiza anthu amene akudwalamatenda a Edzi. Ma ARV samachiza Edzi ayi, amangochepetsakuchulukana kwa tizirombo ta HIV. Amathandizansokubwezeretsa chitetezo cholimbana ndi matenda mthupi. Ma ARVamathandiza kuti chitetezo chimenechi chikhalebe cha mphamvupopeza kuti tizirombo ta HIV sitimachulukananso kwambiri.Mankhwalawa amadula koma kuno ku Malawi amapezekamzipatala za boma mwaulere kwa wina aliyense amene adokotalaamuona kuti ayenera kuyamba kumwa mankhwalawa.

Ma ARV ndi a mphavu ndipo anthu amayamba kumwa akapezadikuti chitetezo chamthupi mwao chatsika kwambiri. Chonde,osamwa ma ARV popanda kuuzidwa ndi achipatala. Munthuameyenera kumwa mankhwalawa moyo wake wonse. Sibwinokuyamba kumwa ma ARV kenako ndi kusiya chifukwa zimachititsakuti ukadzayambanso kumwa mankhwalawa asazagwire ntchitomoyenera.

Kumwa ma ARV sinjira yokhayo yokhalira ndi moyo wanthanziayi. Ukhonza kumadya zakudya zopatsa nthanzi, kumamwamavitamini komanso kukhala m’chiyembekezo. Uzionesetsa kutiukumamwa mankhwala ukayamba kudwala matenda ena aliwonseamene angabwere chifukwa chakuchepa kwa chitetezo chamthupi monga chifuwa chachikulu. Kuchita izitu sizikutanthauzaHIV ichoka mthupi lako ayi, pamenepa utha kupatsira anthu enakapena kuonjezera tizirombo tina nthupi mwako ngati ugonanandi anthu ena. Ndi bwino kumadziteteza ndi kondomu nthawizonse ukamagonana. Izi zitha kukupatsa moyo wautari wakutiumuyang’anire bwino mwana wako.

Zabwino zonse!

Auntie Stella

©TARSC

19

AF19

Page 162: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB19

• Ukhoza kupita kuchipatala kumene amathandiza anthu amene alindi kachilombo ka HIV ndi matenda a Edzi kuti ukamve zambirizokhudza mankhwala ama ARV ndi njira zina zokhalira moyo wanthanzi.

• Ukhonzanso kuitanitsa munthu yemwe akudziwa bwinozamankhwalawa kuti adzakufotokozere kunyumba.

• Ufufuze kwambiri zokhudza ma ARV. Amapezeka kwa aliyense?,Ndi aulele? Komanso ufufuze ubwino ndi zovuta zimenezimabwera munthu akamamwa ma ARV.

• Kodi anthu amene akumwa ma ARV amafuna chithandizochotani? Kodi ayenera kuwathandiza ndi ndani? Kodi achibale ndianzathu atha kupereka chithandizochi? Nanga kuchipatala ndimagulu osamalira anthu amene amapezeka kumudzi kwanu?

• Ngati ma ARV amathandiza munthu kukhala moyo nthawi yayitalindi chifukwa chiyani anthu ena amavutika kuti awapeze? Kodiamapezeka mosavuta m’dera mwanumo? Kodi inu ndi anthu ena,komanso magulu oyang’anira odwala m’mudzi mwanu mukuchitachiyani kuti mulikakamize boma kuti anthu asamayende mtundawautali kuti akalandile ma ARV? Inu monga achinyamata,mukuchitapo chiyani?

• Onani khadi 26 kuti mudziwe zambiri za mmene mungakhalirendi moyo wathanzi ngati muli ndi kachilombo ka HIV kapenamatenda a Edzi.

Page 163: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Akufuna kuti ndizigonana nawo

Okondedwa Patrick

Ngati amai a nyumba yomwe ukakhalamoyo akufuna kumagonananawe, imeneyi ndi nkhanza yokhudza kugonana. Nkhanza imeneyiimatchedwa “indecent assault” pachingerezi ndipo ndikuphwanyamalamulo adziko. Ukuyenera upeze chithandizo ndipo utulukem’nyumbayo mwa msanga zinthu zisanafike poyipa kwambiri.

Ndikugwirizana nawe kuti kuwauza amuna awo zankhaniyizikhoza kukubweretsera iwe mavuto. Choncho ndikukupemphakuti uwauze makolo ako za nkhaniyi, komanso mnyumbamoutulukemo mwa msanga ndikupeza kwina kokakhala. Ndikudziwamakolo ako angafunitsitse kuti iwe ukhale ku malo komwe kulibechiopsezo, ndipo adzayesetsa kulipila ndalama za nyumbayo mwamsanga. Ngati atakuyesanso kuti uchite nawo zoyipazousanasamuke, iwe uvale zilimbe ndipo, udzawauze molimba mtimakuti asiyiretu. Ngati angayesere kulimbana nawe, iwensousadzagonje.

Ndikovuta kupereka umboni wakuti mwamuna wachitiridwankhanza zokhudza zogonana ndi munthu wamayi, makamakapamene palibe chizindikiro chilichonse cha nkhanzayo. Koma ndichachidziwikile kuti mayiwo akukukakamiza iwe kugona nawopamene iwe usakufuna, kumeneku ndi kukuphwanyira iwe ufuluwako.

Chonde uyesetse kuchoka mu vuto limeneli mwa mnsanga .

Auntie Stella

©TARSC

20

AF20

Page 164: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB20

• Mukuganiza bwanji za mndandawu? Pali zimene mungaonjezerekapena kuchotsera?

• Kodi mfundozi zimagwira ntchito mofanana kwa achinyamata ndiatsikana?

• Kodi anthu a m’dera lanu amateteza bwanji ufulu waachinyamata? A chongereni pa teni (10) pa momwe akutetezeraufulu wa achinyamata.

• Aliyense adzichongere pa teni pa momwe amalemekezera ufuluwa achinyamata ena.

Lonjezani kulemekeza ufulu wa anthu ena komanso kukapezachithandizo ngati ufulu wanu ukuphwanyidwa.

Ufuluwa achinyamata achisodzera wokhudzanandi kugonana ndi ma ubwenziWerengani ma ufulu ali mmusiwa okhudza kugonana ndi maubwenzi pakatipa achinyamata achisodzera (achichepele)

1 Wina aliyense asakugwire kapena kukupangitsa kuti ugonane nayepamene iwe sukufuna.

2 Kuyenera kukhala kwa pafupi kwa inu kupeza chithandizo cha kulerera(maleledwe) ndi uthenga wokhudza umoyo wa bwino wogonana ndimoyo wa achinyamata.

3 Anthu onse ogwira ntchito kuchipatala komanso ku Polisi ayenerakukhala ndi uthenga okwanira / ozindikira bwino, othandiza, komansoakumva chisoni pa chinthu.

4 Pakuyenera pakhale mayezedwe abwino, kupereka uphungu, ndimankhwala a HIV/AIDS komanso mankhwala ake azipezeka mosavutandi pamtengo wotsika.

5 Atsikana omwe ali ndi pathupi, ali ndi ufulu wophunzira.6 Ngati muli ndi kachilombo ka HIV kapena matenda a AIDS, musasalidwe

kapena kuchitilidwa nkhanza.7 Aliyense wa mkazi, wa mwamuna, mwana, wakuda ,woyera, woonda, wa

mtali, olumala, akuyenera kupatsidwa ulemu.8 Achinyamata ali ndi ufulu wodzipangira ndondomeko yopezera

chithandizo ndi chisamaliro chabwino cha moyo wawo.

Page 165: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Papita nthawi yaitalindisanapange msambo

Okondedwa Irene

Osadandaula – palibe chifukwa choganizira kuti sudzabereka.Sichinthu chachilendo kuona kuti kusamba kwako ndi kojowajowa, makamaka munthu ukangoyamba kusamba kumene ngatiwachitira iwemu. Atsikana ena amakhala akusamba bwino bwino,kenaka ndikuyamba kudumphitsa dumphitsa ngati mmeneukuchitira iwemu, kapenanso kusiya kumene kwa kanthawikapena kwa chaka chonse chathunthu osasamba. Koma pakapitanthawi izi zimatha ndipo amayamba kusamba bwino bwino.

Pali zinthu zinanso zimene zimatha kusokoneza kasambidwekanu, monga kukhala ndi nkhawa , kapena pamene ukunenepakapena kuwonda kwambiri, kapenanso pamene wadwala kwanthawi yaitali. Koma kwa mkazi yemwe wagonana ndi mwamuna,kusasamba ndi chizindikiro choyamba kuti mwina watengamimba.

Koma funsani a chipatala kapena a namwino, makamaka pamenekusamba kwanu sikukuyamba patatha chaka chathunthu.Muyesenso kudya zakudya za thanzi zachilengedwe, zipatsozambiri, ndi za masamba, komanso zimene zili ndi ayiloni wambiri- monga masamba obiliwira, nyemba, nandolo, mazira, nsombankhuku, ndi nyama zina komanso ziwala ndi ngumbi.

Iwe ndi anzako muyenera kudziwa bwino za momwe matupi anuakusinthira. Kapezeni chithandizo chimene mungachifune kwa achipatala chothandiza achinyamata kapena ogwira ntchito ya zaumoyo kuti mudziwe zambiri

Auntie Stella

©TARSC

21

AF21

Page 166: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB21

• Irene akuopa kuti mwina iye ndiosabereka. Inu muli ndi manthaotani okhudza thupi lanu, kugonana kapena kukhala ndi ana.Kambiranani ndi anzanu za mantha anuwo ndipo muone ngatiangakuthandizeni. Ngati pagulu lanu mukufuna za chinsinsi,lembani mafunso anu pa pepala lopanda dzina ndipo musakanizem’thumba. Kenaka awerengedwe kugulu kuti mukambirane.

Ngati gulu lanu silinakuthandizeni, kodi mungapite kwa ndanikukapeza chithandizo?

• Anthu amadziwa zambiri zokhudza matupi awo, monga kugonanandi zibwenzi kuchokera kumalo osiyanasiyana ndi kwa anthunso.Kodi inu mumapeza kuti chithandizo ngati chimenechi? Lembanim’ndandanda wonse. Kodi mungazindikire bwanji kutimwathandizidwa zoona zeni zeni kapena mwauzidwa za bodza.

• Jambulani chithunzi cha chipatala chimene mukuganiza kutichimathandiza bwino achinyamata. Muonetse bwino lomwechifukwa chimene mukuganiza kuti chimathandiza bwinoachinyamata. Yerekezani chithunzi chanucho ndi chipatalachomwe inu mudapitako. Kodi mukuganiza kuti chipatala chanuchimathandiza achinyamata moyenera ndi mwaulemu? Ngati sichoncho, Kodi inu ndi anzanu m’dera lanu mungachite chiyanipamodzi kuti izi zisinthe?

Page 167: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi ndi koyenera kuti ndigonane naye

Okondedwa Emily

Chofunikira kwambiri ndichakuti, kukhala ndi kachilombo ka HIV,sikupangitsa munthu Kukhala wosiyana ndi momwe analilipoyamba, ndipo palibe munthu amene amakonza malamuloapadera azimene zimaloledwa kapena ayi. Aliyense amene ali ndikachilombo ka HIV zosoweka zake ndi zofanana ndi ena, mongachikondi, ubwenzi, kugonana, ukwati komanso kukhala ndi ana.Ambiri mwa anthu amene ali ndi kachilombo ka HIV, ali ndiabwenzi awo, amenenso ena mwa iwo ali ndi kachilombo ka HIV.

Kuti umuuze Gobede sichinthu chapafupi ayi koma udzayenerakumuuzabe nthawi ina yake. Poyambirira umuwuze za m’meneiwe uliri musanapitirize za chibwenzi chanu chanu.Chachidziwikire muyenera kuyamba mwakambirana kaye nkhaniyogwiritsa ntchito kondomu musanayambe kugonana. Ngatiangakane kugwiritsa ntchito makondomu, kapena kukulola iwekugwiritsa ntchito makondomu achikazi, kapena sangakwanitsekuti musamalowetsane pogonana, pamenepa simuyeneransokugonana , ngakhale angaoneke ngati ndi wabwino pamaso.

Ukuganiza bwino powopa zopatsirana kachilombo ka HIV.Ndikanakonda anthu onse akanakhala ozindikira udindo waopankhani ngati izi monga iwe. Koma kumbukiranso kutingakhaletu bwenzi lakolo angapezekenso kuti ali ndi kachilomboka HIV, muyenerabe kugwiritsa ntchito makondomu pogonana. Izizidzakuthandizani kupewa kupatsirana tizilombo tina nthawiyomwe inu mukugonana.

Ine ndikukufunirani zabwino zonse za tsogolo lanu labwino,pamaganizo alionse amene ungapange.

Auntie Stella

©TARSC

22

AF22

Page 168: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB22

• Kodi mukugwirizana nawo maganizo a Auntie Stella kapena ayi.Fotokozani zifukwa zake.

• SEWERO: Pasoweka anthu awiri, Emily amufotokozeraGobede kuti ali ndi kachilombo ka HIV.

• Sewero likatha, anthu opanga sewerowo awuze anzao enamomwe anamvera akukambirana za nkhaniyi. Kenako aliyenseakhoza kukambirana nawo mafunso awa.

a) Kodi chinachitika ku mapeto ndi chiyani? Kodi zinalizovuta kwa awiri opanga sewero aja? Kodi kutha kwakekunali kwa bwino? Ngati silinathe bwino, kodimukanafuna likanatha bwanji?

b) Kodi mathero awa angakhale choncho pakati paachinyamata amene inu mukuwadziwa?

c) Kodi mathero amenewa akanasiyana akanakhala kutiGobede ndiye anali ndi kachilombo ka HIV ndipoamamuuza Emily? Ngati ndi choncho, kodi kusiyanakwake kungakhale kotani? ( Mupangeso sewero lija, komamusinthitse ma udindo, pakati pa mkazi ndi mwamuna,ndipo onetsetsani kuti chichitike ndi chiyani).

d) Kodi ndi mabungwe ati, kapena anthu ameneangathandizepo pa zinthu ngati izi?

Tiyenera kukambirana tsopanoNdikufuna ndikuuze

zina zake…….

Page 169: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi chamba chingandichotsemanyazi?

Okondedwa Jack

Anzakowa akukupatsa malangizo oipa. Ngakhale anthu enaamanena kuti chamba chimawachititsa kuti akhale omasuka,uyenera kudziwa kuti anthu ena chimawazunguza mutundikuwapatsa mantha.

Ndikudziwa kuti ndiwe osasangalala pakuti ulibe chibwezi, komachofunika ndikumacheza ndi atsikana ngati anzako basi.Ukamacheza nao choncho, ubwenzi umayambira mukuchezakomweko.

Ukhonza kuyamba kucheza ndi atsikana pa kuwapatsa moni,kuwamweturira ndikucheza nao za sukulu, zanyengo ndizinazotero. Njira ina ndi yakuti udziwe bwino anthu amene ukufunakupalana nawo ubwenzi-monga kudziwa zimene amakondakomanso mavuto awo. Atsikana ambiri amakonda munthu wotereosati odzitukumula.

Komanso zindikira kuti palibe amene akufuna atakuona utapangachinthu chopusa ayi. Palibe munthu amafuna kuti achite zinthuzopusa kapena zoipa.

Zindikira kuti sungathetse mavuto pakumwa mankhwalaozunguza bongo, kusuta kapena kumwa mowa. Anthu ambiriamachita zinthu zosayenera akamwa mowa zimene zimayambitsamavuto m’mabanja awo, kuntchito komanso ndi anzawo ochezanao. Kusuta chamba ndikoletsedwa ndi malamulo a dziko linondipo kukhoza kukupezetsa mavuto.

Kuti ukondedwe ndi anthu sikufuna kumwa mankhwala ozunguzabongo ayi. Pali njira zambiri zabwino zothetsera manyazi.Zabwino zonse.

Auntie Stella

©TARSC

23

AF23

Page 170: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB23

• Lembani mndandanda wa mankhwala ozunguza bongo amenemumawadziwa ndi zimene amachita mthupi la munthu amenewawagwiritsa ntchito mankhwalawa. Nanga ndi mankhwala atiomwe umati ukayamba kuwagwiritsa ntchito ndipovuta kusiya.

• Yang’anani mndandanda wa zifukwa zimene zimapangitsa kutiachinyamata azigwiritsa ntchito mankhwala ozunguza ubongo.Kambiranani zifukwa zimene zikukukhudzani. Zilembenimundondomeko iyi: 1-5 kuyamba ndi chifukwa chodziwikakwambiri.

Achinyamata amagwiritsa mankhwala ozunguza bongo chifukwa:

– Chakutengera anzawo– Kuti aiwale mavuto omwe akukumana nao– Kudzizimbaitsa – Kuchotsa mantha– Kusowa chochita

• Mutatha kukambirana izi, fufuzani ngati gulu lanu lili ndi vutologwiritsa nchtito mankhwala ozunguza bongo. Kenakokambiranani zimene inu eni ake mungachite kuti muthetse vutoli.Nanga ndani wina angakuthandizeni?

• Sewero: Pakhale msungwana ndi mnyamata. Mnyamata wamanyazi ayambe kukambirana ndimtsikanayu. Pakapita mphindizochepa awiriwa asinthane, mtsikana ayambe kulankhulitsamnyamata uja. Pamapeto pake kambiranani izi:

i) Munthu amamva bwanji kuti ayambe kucheza ndimnzake?

ii) Mwaphunzira chiyani za kuthetsa manyazi kapenakupanga ubwenzi ndi munthu?

Page 171: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Makolo anga ndi ovuta

Wokondedwa Davie

Sindiwe wekha. Achinyamata ambiri satha kulankhula ndi makoloawo, makamaka pa nkhani zokhudza kugonana ndi zibwezi.Makolo amatenga nthawi kuti adziwe kweni kweni za umunthuwako ukamakula kuti ayambe kukumvetsetsa ndi kukukhulupirirapamene ukukhwima msinkhu.

Uyenera kumvetsetsa kuti makolo ako amakukonda kwambirindipo amafuna kuti ukule bwino ndikukhala munthu wa tsogololabwino. Makolo amadziwa bwino za mavuto amene ungakumanenawo mmoyo wako pamene ukukhwima msinkhu chifukwanawonso adakhalapo ana. Iwo akudziwa bwino lomwe kuti moyowa masiku ano ndi oopsa makamaka chifukwa cha matenda aEdzi. Ndi chifukwa chake akukulangiza pafupipafupi zimeneuyenera kuchita. Zindikira kuti makolo ndi gwero lako lamalangizo abwino.

Ukhoza kulimbikitsa mgwirizano wako ndimakolo ako mosavuta.Poyamba yesetsa kuti uzikukhulupirika pomvera malamulo awo.Ngati ukuona kuti akukulakwira uwafotokozere za ichi ndipoumvere malangizo awo. Chachiwiri uziwafusa pa zimeneumalakwitsa ndipo uwauze zimene umafuna mmoyo wako kutiadziwe. Pomaliza ndikulangize kuti uzilankhula nawo modekha ndimwaulemu, osawakwiira kapena kuwachitira mwano. Ngatimkwiyo wakufikira ndi bwino kukhala phee ndipo ulankhulepatapita kanthawi.

Yesetsa kutsatira izi-udzasangalala. Ngati izi zingalepherekeukafunse aphunzitsi ako kapena wachibale kuti akuthandizemaganizo.

Auntie Stella

©TARSC

24

AF24

Page 172: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB24

• Lembani mndandanda wa zimene mumakonda-mongakumweturira, luso lomwe muli nalo kapena kusatengekatengeka.Munaphunzira kuti izi? Kapena munaphunzira kuchokera ku banjalanu?

Kodi phunziroli lakuthandizani bwanji pa zimene banja lanulinakuchitirani kuti mukhale m’mene mulilimu.

• Sewero: Khalani awiri awiri, sankhani kukambirana china chirichonse chimene simumagwirizana kapena kukangana pakati pamakolo ndi achinyamata. Sinthanani kuti wina atenge gawo lamakolo pa mkanganowo ndipo muwafotokozere anzanu mmenemukudzimvera.

• Pagulu lanu, fanizirani dziko lomwe makolo ndi akuluakulusanapereke malangizo kwa ana. Nanga dzikoli lingakhale lotani?Kambiranani ndi anzanu zimene gulu lanu lapeza poyimba nyimbo,sewero kapena ndakatulo.

• Konzani tsiku lomwe mukufuna mukalankhule ndi kholo kapenamakolo anu onse pa zimene zikukukhumudwitsani. Yeseranim’mene mukanenere osaiwaila paja ndakuuzani kuti muzilankhulamodekha, momvetsetsa ndi mwa ulemu.

Page 173: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi ndimuuze kuti ndili ndi matenda opatsirana pogonana?

Wokondedwa Alex

Kuchita chisankho chogonane ndi munthu ndiye kutimukudziwana ndi munthuyo. Sibwino kumupatsa matendamnzako. Uyenera kumuteteza ku matendawa. Ngati bwezi lakoliri ndi matenda opatsirana pogonana ndipo silikupita kuchipatalalitha kukupatsiranso matendawa.

Matenda opatsirana pogonana alipo ambiri ndipo zizindikiro zakendi zovuta kudzisiyanitsa. Pamene mzimayi watenga matendawapamatenga nthawi kuti zizindikiro zitulukire kunja.

Nonse awiri mupite kuchipatala kuti mukalandire mankhwala.Afunse a namwino akupatse kalata yokamudziwitsa bwezi lako(komanso mzimayi yemwe unagona naye kubala uja). Popitakuchipatala adzaonetsetse kuti atenga kalata imeneyi kutiakalandire chithandizo cha mankhwala oyenera ndiponsosakawafunsanso mafunso ayi. Mankhwalawa sagawana ayi. Aliyenseamayenera kulandira mankhwala ake ndipo amayenera kumalizakumwa mankhwalawo ngakhale zizindikiro za matendewo zitatha

Uyenera kukhala ndi mkazi mmodzi ndipo chifukwa chakutiunagonanapo ndi mkazi mosadziteteza, ndi bwino upiteukayezetse kuti udziwe ngati uli ndi kachilombo ka HIV kapenaayi.

Auntie Stella

©TARSC

25

AF25

Page 174: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB25

• Sewero: Pakhale mnyamata ndi mtsikana. Alex waganizazomuuza bwezi lake za matenda opatsirana pogonana omwe alinao. Chichitike ndi chiyani? Kutengera pa zomwe mwadziwatsopano, mukanakhala Alex mukanatha kumuuza bwezi lanu kutimunali ndi matenda opatsirana pogonana?

• Ntchito: Jambulani mapu osonyeza malo omwe achinyamataangapezeko makondomu. Pamalo alionse muike mayankho amafunso awa:

1) Kodi makondomu ndi aulere kapena ogulitsa?2) Uyenera kukhala wa zaka zingati kuti upeze

makondomuwa?3) Kodi amapereka makondomu kwa atsikana?4) Kodi amagawa makondomu a amayi?5) Kodi amalemekeza achinyamata?

Perekani malikisi 10 kwa malo ena alionse molingana ndimayankho omwe mwapeza. Ngati mayankho anu akusonyeza kutiachinyamata sangapeze makondomu mwaulere ndi mosavuta,mungachite chiyani kuti makondomu azipezeka mosavuta? Ndianthu ati kapena mabungwe ati amene angakuthandizeni?

• Yang’anani khadi nambala 7 ndi 13 kuti mudziwe zambiri.

Page 175: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndili ndi kachirombo ka HIV.Kodi ndimwalira?

Okondedwa Charity

Kupezeka ndi HIV simathero a moyo wako ayi. Pali njira zambirizimene ungatsate kuti usadwale matenda a Edzi monga kudyazakudya zoyenera ngati za chilengedwe monga bonongwe, ziwalandi zina zotere osati zakudya zopangidwa ku fakitolekokhakokha. Udzigonanso kokwanira ndithu ndi kumachitamasewero olimbitsa thupi. Usamamwe zakumwa zoledzeretsa,zozuna (za shuga kwambiri). Nthawi zonse ukadwalauzithamangira kuchipatala kuti ukapeze chithandizo chamankhwala. Nthawi zonse pogonana, uzigwiritsa ntchitokondomu. Njira ina yothandiza kwambiri ndi kusakhala ndinkhawa ina iri yonse komanso kukhala wa chiyembekezo.

Ukhozanso kulowa nawo mm sapoti gulupu a anthu amene alindi HIV komwe amakumana ndi kumachotsana nkhawa.Maguluwa akhozanso kukambirana ndi azakhali ako za nkhaniyingati iweyo utafuna kuti atero.

Anthu ambiri amaopa matenda a Edzi chifukwa chakuopakumwalira, kusalidwa ndi kuchitiridwa nkhanza. Ku sapoti gulupuakakuthandiza kuchotsa nkhawa ngati zimenezi. Anthu enaanapezeka ndi HIV zaka zambiri zapitazo ndipo lero lino alibwino bwino ndipo amakhala mosangalala, amagwira zintchitozawobwino bwino ndipo ena amabereka ana. Iwensoutalangizidwa bwino ukhoza kuchita zimenezi. Anthu ena akhozakukulimbitsa mtima ndikukupatsa chiyembekezo. Iwenso ukhozakuthandiza ena.

Auntie Stella

©TARSC

26

AF26

Page 176: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB26

• Uzilankhula ndi anthu omwe ndi omasuka kulankhula zokhala ndikachilombo koyambitsa Edzi kapena kukhala ndi Edzi imene.Uwafunse zimene amachita kuti azikhala athanzi, opanda nkhawandikukhala ndi chikhulupiriro cha moyo wabwino. Ndi anthuambiri amene ayenera kudziwa izi-ugwire ntchito ndi mabungwendi malo a achinyamata kuti uwadziwitse achinyamata ambiri.

• Upange kafukufuku wa maganizo a anthu pankhani ya Edzi: Kwamulungu umodzi ukhale tcheru ndikumvera zomwe anthuamanena za Edzi. Uwafotokozere zambiri zomwe iwe ukudziwapokambirana nawo mwaulemu maka pamene akunena zotsutsanandi zoona zokhudza Edzi.

• Takumbukira nthawi imene unali osasangalala ndi osungulumwandi zimene unachita kuti uthetse izi. Chinakuthandiza ndi chiyani?Tawauza anzako ndipo ndi mfundo ziti zomwe zingathandizeanthu omwe ali ndi matenda a Edzi.

• Tayang’ana pa khadi nambala 19, 22 ndi 40 kuti uone mafunsoena omwe anthu odwala matenda a Edzi amafunsa.

Page 177: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Kodi ndiri ndi mimba?

Okondedwa Doreen

Dziwa kuti ukhoza kutenga mimba ngakhale munagonanakamodzi kokha. Chimene ungachite ndi kupita kuchipatala kutiakakuyeze ngati ulidi ndi mimba.

Ngati uli ndi mimba ukambirane ndi bwenzi lako komansomnzako yemwe umagwirizana naye. Chonde usachotse mimbayi.Ndi kwa bwino kufunsa nzeru kwa anthu amene angakuthandizemaganizo a mmene ungalelere mwana wako Ichi sichapafupi ayi,koma abale ako ndi ena akhoza kukuthandiza bwino.

Mapilisi oteteza kutenga mimba ngati wagonana ndi mwamunaamapezeka mzipatala komanso msitolo zogulitsa mankhwala.Koma mapilisi amenewa amagwira ntchito pokhapokha ngatiamwedwa pa nthawi yosapyolera maola 72 kuyambira pomwemunthu wagonana ndi mwamuna.

Ngati ulibe mimba uli ndi mwayi. Anyamata amakakamiza munthukuti agonane naye koma monga wadziwa tsopano, kugonanasikusangalatsa ngati munthu sukufuna.Ndi bwino kupewa kumwamowa ndi mankhwala ozunguza bongo, chifukwa zimenezizimasokoneza zolinga za munthu.

Ndi bwino kudziletsa mpaka utakula ndi kukhwima msinkhu,usanachite zogonana. Ngati ungafune kuchita zogonana,udzigwiritsa ntchito kondomu- kaya ya chimuna kapena yachikazi.

Auntie Stella

©TARSC

27

AF27

Page 178: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB27

• SEWERO: Khalani awiri awiri ( mnyamata ndi m’tsikana)

Mnyamata afunsire mtsikana, yemwe ayankhe kuti ali ndimakondomu ndipo akhoza kuthandiza mnyamatayu kuti avaleimodzi. Chachitika ndi chiyani?

– Panganinso sewelori, ndipo mnyamata ayerekeze ngatindiye mtsikana ndipo mtsikana ayerekeze kuti ndiyemnyamata. Kodi zichitika ngati poyamba paja?

– Kenaka kambiranani zifukwa zomwe atsikana ndianyamata osadziletsa ayenera kuyenda ndi ma kondomunthawi zonse.

• Lembani nyimbo kapena mawu (slogan) olimbikitsa achinyamatakuti asamagonane m’paka atakula, komanso kuti azikhala ndichibwenzi chimodzi ngati atafuna kukhala ndi chibwenzi.Muyimbe nyimboyo, kapena onetsani mau ena ndi enaachilimbikitso. Kenaka sankhani ndi kugwirizana kuti walembamau / nyimbo ya chilimbikitso yoposa ena onse ndi ndani.

• Onani khadi 32 pofuna kudziwa zambiri zoyenera kuchitamunthu akakhala oyembekezera, mosayembekezera.

MAFUNSO : Kondomu ya chikazi.Kodi muziganizo zili m’musizi, zili zoona komanso zili zonama ndi ziti.Pezani mayankho olondola pambuyo pake omwe alipansi penipeni patsambali.

1 Ma kondomu achikazi, amateteza amuna ndi akazi kutenga mimba,matenda opatsirana pogonana, komanso ku kachilombo ka HIV.

2 Makondomu achikazi, ndi okwelerako mtengo kuposa makondomuachimuna.

3 Kondomu yachikazi imatha kupanga phokoso pogwiritsa ntchito.Kupewa izi mayi ayenera kuivala maola ochepa musanayambekugonana.

Mayankho:Ziganizo zonse ndi zoona.

Page 179: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Bwenzi langa akukwatiwa

Okondedwa Joshua

Pepa chifukwa cha vuto lomwe lamugwera bwenzi lako, komabendili okondwa chifukwa ndiwe okonzeka kumuthandiza.

Kulowola kumakhala bwino ngati kuchitika mu dongosolo lakeosati pamene anthu angotengeka ndi ndalama. Izi ndi zotsutsanandi ufulu wa chibadwidwe wa munthu wa mkazi,wosakakamizidwa kukwatiwa pamene iye sakufuna.

Kambilana naye Suzeniyo kuti udziwe kuti iye akufunaumuthandize bwanji. Ndipo awirinu mupeze njira yothetsera vutolimeneri.

Mwinanso iwe ndi Suzeni mukhoza kukambirana ndi anthu ena am’banja mwa Suzeniyo za zinthu zimene mukuona kuti zikhozakumuthandiza ndipo ngati akumumvera chisoni akhozakuthandizapo pokalankhulana ndi makolo ake

Ngati sizinathandizebe, Suzeni akhoza kukadandaula ku bungweloona za amayi. Koma njira iyi ikhoza kubweretsa udani pakati paiye ndi abale ake. Ichi ndi chisankho chachikulu chakuti Suzeniachite, choncho muthandizeni kuti asaonjezere mavuto ena paamene ali nawo kale.

Nkhaniyi ndi yovuta, koma ndili ndi chikhulupiliro kuti mupezachithandizo kuchokera kwa wina wa m’banja lakwa Suzenikapena anthu ena a m’dela lanu.

Auntie Stella

©TARSC

28

AF28

Page 180: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB28

• Mulungu wa mawa mufunse anthu 10 ena achikulire enansoachichepere. Mumve maganizo awo ngati kuli koyenera kapenaayi kuti makolo azipezera ana awo a akazi kapena a amunamunthu omanga naye banja. Mukamaliza, nonse khalaninso pansindipo kambiranani zimene aliyense wapeza pakafukufukuyo.

• Taganizirani zinthu zina zimene akuluakulu ndi achinyamataamatha kusemphana maganizo m’mene zinthu ziyenerakuyendera. Kodi mungachite chiyani kuti mukambirane nawoachikulirewa kuti kusemphana maganizoko kuthe, ndipo nonsemupeze njira imodzi yothandiza pa zinthu ngati zimenezi.

• Konzani nthawi yakuti mugwiritse ntchito makhadi a Auntie Stellapakati pa achinyamata a chisodzera ndi anthu akulu akulu.Apempheni achikulirewo kuti akambirane gawo la ZoyeneraKuchita ndi ntchito. Mukatero nanunso achinyamata kambirananimaganizo anu. Kodi maganizo anu akusiyana ndi maganizo a anthuachikulirewo? Kodi izi zimathandiza kuchepetsa kusiyanamaganizo pakati pa achikulire ndi achinyamata?

Page 181: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Aphunzitsi anapeleka mimbakwa mnzanga

Okondedwa Cynthia

Wandisangalatsa kwambiri ndipo ndikukunyadira iwe ndi anzakoa m’kalasi mwako. Pamafunika kulimba mtima ngati unachitiraiwemu kuti munthu aime pagulu ndi kudzudzula khalidwe loipa.Chodandaulitsa kwa ine ndi chakuti nkhani ngati izi zikuchulukirachulukirabe masiku ano

Dziwani kuti ngakhale cholinga chanu ndikumuthandiza Loveness,zimene mukuchitazi zikhozanso kusintha mmene sukuluimazengera mlandu aphunzitsi amene amaphwanya ufulu wa anaawo a sukulu. Ntchitoyi siyamasewera ayi. Ndiyovuta kwambiri.

Kuti ntchitoyi itheke, yesetsani kupeza anthu ambiri ameneangakuthandizeni kumenya nkhondo imeneyi. Ena mwa anthuamene angakuthandizeni ndi makolo, aphunzitsi, ana a sukuluanzanu, achinyamata, mabungwe, ndi anthu ena a m’dera lanu.Anthu amenewa akhale makamaka amene amapatsidwa ulemu,amene amalemekezedwa chifukwa cha nzeru zawo, otchukakomanso a chikoka, (monga atsogoleri a ndale, a mipingo, ndiochita ntchito za malonda).Mulemberenso makalata ku mawailesindi kumanyuzipepala za mdziko muno kuti nkhani yanu imvekepatali. Ngati anthu ambiri ayidziwa nkhaniyi ndipo ali kumbaliyanu, kudzakhala kosavuta kuti akulu akulu asukulu yanu achitepokanthu pa nkhani ya mphunzitsi wochititsa manyaziyu.

Ngati mutaona kuti simukupambana pa nkhondo imeneyi, inumusadandaule. Kawirikawiri kusintha kwa zinthu sikumachitikanthawi yomweyo, kumachitika pang’onopang’ono. Chonchomusaganize kuti mwagonja mukaona kuti palibe chachitikapanopo. China chili chonse chimene chingachitike pa nkhaniyi,ngakhale chitachepa bwanji, koma ngati chiri chofuna kukonzachoipa ndi kupambana basi.

Auntie Stella

©TARSC

29

AF29

Page 182: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB29

• Kodi kuyankha kwa Auntie Stella mukukuona bwanji? Kodimukugwirizana nako?

• Kodi pali zinthu zina zake zoipa pasukulu panu, m’bungwe lanu,kapena m’mudzi mwanu zimene mukufuna kuti zisinthe.Gwirizanani nonse pamodzi kupanga dongosolo lomwemungatsate pogwira ntchito yosintha zinthu zimenezi. Panganiziganizo kuti ndi chiyani chomwe mukufuna chisinthe, nanga ndindani yemwe angakuthandizeni. Konzani msonkhano ndipomukonze dongosolo ngati lili m’musimu.

Vuto

Kodi vutondi chani?

Zimenetikufuna

Koditikufunakusinthakotani?

Njirazimenetigwiritsentchito

Tikuyenerakuchitachiyani kutikusinthakukutheke.Mwachitsanzo,kuchitamisonkhano,kukambirana ndi anthuameneangakuthandizeni, Kulembakalata yachidandaulo.

Zidazimenetizifune

Zosowekandi chiyani?(Mongandalama,anthu, ndizinazofunikirakugwiritsantchito.

Ndaniameneagwirentchitoimeneyi

Ndi ndanimugulu lanuyemweadzachitentchitoyanji? Mwachitsanzo;Joyceadzakonzamisonkhano,Georgeadzakonzama poster,Lindaadzakakhoma ma poster.

Nthawi

Tsikulomwetagwirizanakudzagwirantchito,komansonthawiimeneTikufunakuti zinthuzikhalezitatheka.

Page 183: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Mwamuna wanga ndi wachimasomaso

Okondedwa Josephine

Kulowa m’banja uli wamng’ono nthawi zambiri kumabweretsamavuto m’banja chifukwa chakuti achinyamata amakhala akukulakumene ndipo asanazindikire bwino bwino zimene akufuna pamoyo wawo. Komabe udziwe kuti pali azimayinso ambiri angatiiwe amene masiku ano amakana kugonana ndi amuna awopopanda kugwiritsa ntchito kondomu. Amayi ambiri masiku anoakuonesetsa kuti amuna awo akhale okhulupirika, ndipo akukanakuti atenge kachilombo ka HIV chifukwa cha kusakhulupirika kwaamuna awo.

Ndiwe wolimba mtima posamusekelera Charles pofunakudziteteza wekha kukachilombo ka HIV polingaliranso kuti ulindi mwana wamng’ono yemwe asoweka chisamaliro chanu pamoyo wake. Njira imodzi imene ungatsate ndi kugwiritsa ntchitokondomu ya amayi.. Choncho nonse muyenera kukayezetsamagazi. Uyenera kukambirana nayenso Charles za nkhani yakulandira uphungu ndi kuyezetsa magazi. Umumvetsetse zimeneakuopa. Ngati pali wina amene angamulimbikitse kuti apitekoyezetsa magazi, umupeze munthu ameneyu kuti akuthandize.

Ngati Charles apitiliza kukana, uyenera kuti uganize bwino zachinthu chimene chili chofunika kwa iwe ndi mwana komansochimene ungachite kuti chikuthandize. Umuuze mwamuna wakopa zimene ukuganiza ndipo umve maganizo ake ngati akufunakuteteza banja lanu. Ngati mungakhalebe pa ukwati wanu, uwundi mwayi wakuti mukambirane za chiyembekezero cha munthuwina aliyense pakati pa anthu awirinu m’banja mwanu. Abale anukapena alangizi akhoza kukuthandizani.

Ine ndikukufunirani za bwino zonse.

Auntie Stella

©TARSC

30

AF30

Page 184: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB30

• SEWERO: Khalani anthu awiri awiri wina akhale ngati mkaziwina mwamuna Mukhonzanso kukhala m’magulu amuna kapenaakazi okhaokha. Kambiranani pamene mkazi akufuna kutimwamuna avale kondomu, kapena pamene mkazi akufuna kutimwamuna akayezetse magazi.

Kenaka uzani gulu lanu momwe zinthu zinakhalira. Kodi amunakomanso akazi awo anamva bwanji? Kodi inu mwaphunzirapochiyani pa Zoyenera Kuchitazi?

• Kodi ndichapafupi kuti mkazi awuze bwenzi lake kugwiritsantchito kondomu? Kapena mkazi wa m’baja kuuza mwamunawake? Kodi kapena ndi chimodzimodzi? Ngati ndi zosiyana ndichifukwa chiyani?

• M’magulu mwanumo jambulani mwamuna ndi mkazi womweakusangalala limodzi. Pachithunzicho jambulani kapena lembanizinthu zonse zimene zimachitika m’banja labwino. Kodi maganizoanu anali ofanana.

Page 185: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndimakhala ndi nkhawapopanda chifukwa

Okondedwa Lucy

Kukhala ndi nkhawa ndi mbali imodzi ya munthu wina aliyense.Achinyamata ambiri amakhala ndi moyo wovutika chifukwa chaumphawi ndi nkhaza zimene zimawaonekera.

Thupi la mtsikana aliyense wa msinkhu wako, limakhalalikukhwima nthawi ndi nthawi. Izi zimachititsa kuti nthawi zinamunthu uziti nthawi pang’ono wakhumudwa komanso pakapitaka nthawi kochepa wayambanso kosangalala. Sikuti ndiwe wekhaayi. Aliponso anzako amene zikuwachitikira izi. Chofunika kuchitandi chakuti uwauze anzako za zimene zikukuchitikira ndipo iwoadzakhala omasuka kukuwuza zimene nawonso zikuwachitikira.

Atsikana ndi azimayi ena amakhala okhumudwa pa nthawi imeneayandikira kupanga msambo. Choncho ndi bwino kufunsa azimaikapena atsikana anzako kuti akuuze zimene uyenera kumachitaukakhala ndi vuto ngati limeneri

Ukhozanso kuchita masewero olimbitsa thupi kapena kumadyazakudya zopatsa thanzi, komanso kugona nthawi yokwanirakuimba nyimbo kapena kuwerenga mabuku. Ngati ukufuna kulira,ukhoza kutero chifukwa nthawi zina kulira kumatithandizakuchepetsa kukhumudwa kwathu. Ngati sizikukuthandiza, ndibwino kuti ukalandire chithandizo cha mankhwala ndikukalandira uphungu oyenera kuchipatala. Za bwino zonse.

Auntie Stella

©TARSC

31

AF31

Page 186: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB31

• Jambulani chithunzi chachikulu cha munthu yemwe aliokhumudwa pakati pa tsamba lalikulu la pepala . Mozunguliramunthu ameneyu, lembani zinthu zosiyana siyana zimenezingachitike kuti kukhumudwa kumeneku kuthe, kapena kuchepe.Mulembe zinthu zimene zingathandize kwambiri pafupi ndimunthuyu, ndipo zimene sizingamuthandize, kutali ndi munthuyu.

• Kambiranani ndi anzanu za nthawi zimene munakhalapookhumudwa ndi osasangalala. Afotokozereni anzanuwo ngatipanali chifukwa china chiri chonse chimene chinakuchititsani kutimukhale choncho. Nanga zimenezi zinatha bwanji.

• Gwirizanani pa gulu lanu kuti mukhale ndi nthawi imenemuzikumana pa sabata kamodzi kuti muzikambirana za mmenesabata lanu lathera komanso za mmene mukumvera mthupindipo muzigwirizana za mmene mungathandizire amene angafunechithandizo komanso za kumene mungapite kutimukathandizidweko. Ngati munayamba kale kukumana , yambanimsonkhano wanu ndi ntchito imeneyi.

• Ngati mumapanga masewero olimbitsa thupi mochepera katatupa mulungu, pangani dongosolo ndi anzanu kuti muzitha kuchitazina limodzi zimene inu mumakonda. Mwachitsanzo kuyenda,kapena kuthamanga.

• Kuthandiza anthu ena ndi njira imodzi yothandiza munthu kumvabwino. Gwirizanani zinthu ziwiri zimene mungakonde kuchitamonga kugwira ntchito modzipereka ku mpingo kwanu, kapenakuthandiza ana kulemba ntchito yao ya kusukulu. Panganindondomeko ya mmene muzichitira zimenezi. Pomalizakambiranani momwe mukumvera mutapanga ntchito zimenezi.

Page 187: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Sindikumfuna mwana ameneyu

Okondedwa Patuma

Pepa kuti izi zinakuchitikira. Komatu suli wekha ayi, chonchousachite china chiri chonse chimene chingaononge moyo wakokomanso wa mwanayo. Uyenera kuti ukambirane ndi munthuamene umamukhulupilira pa banja lanu kapena kumenemumakhala. Munthu ameneyu akhoza kukuthandiza kuwauzamakolo ako. Makolowa adzakhumudwa kwambiri akadzamva,koma pakadzapita nthawi adzayamba kumakuthandiza.

Zina zimene ungathe kuchita ndi izi;

– Samala mwanayu ndi chisamaliro chochokera ku banja lanu,komanso mwina kuchokera kwa bwenzi lakoyo.Usadandaule chifukwa ukhoza kudzapitiliza maphunziroako mwana akadzakula. Komanso mwina wina m’banjamwanu akhoza kukulelera mwanayo pamene iweukupitiliza maphunziro ako..

– Ukhozanso kukamupereka kwa anthu osowa ana kutiakamutenge kukhala wawo. Alipo mabungwe ameneangakuthandize kuti izi zitheke

Chonde Patuma usachotse mimbayi. Kuchotsa mimba pogwiritsantchito mankhwala a zitsamba ndi koopsa kwambiri chifukwakukhoza kuchititsa kuti usadzaberekenso ndiponso ukhozakumwalira kumene. Ndiponso usamaganize zodzamutaya mwanawakoyo chifukwa izi ndizosaloledwa mmalamulo adziko lathulino.

Ganizira mozama ndi mofatsa usanachite chili chonse.Ndikukhulupilira kuti upeza chithandizo chomwe ukusowa.Zabwino zonse.

Auntie Stella

©TARSC

32

AF32

Page 188: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB32

• M’ Malawi, kuchotsa mimba kumaloledwa pokha pokha ngatimunthu wachita kugwiriridwa ndipo kuti mayi kapena mwanayoali pa chiopsyezo cha imfa. Njira yopezera chilolezo chochotseramimba ndi yaitala komanso yovuta. M’mayiko ena anthu amathakukhala ndi chilolezo chochotsera mimba ngati pasanathemasabata khumi ndi awiri. Inu maganizo anu ndi otani pankhaniyi?

Pangani mtsutso pa mutu wa nkhani imeneyi.

• SEWERO: Anthu atatu pa gulu apange sewero lomwem’modzi mwa omuthandiza Patuma, msewelori awuze makoloake a Patuma za kuti mwana wao ali ndi mimba. Aliyense mwaowonera ali ndi ufulu kuimitsa sewelori nthawi ina ili yonse iyendi kulowamo ndi kusewera mosiyana ndi amene watulukamoyo.Kenaka kambiranani za zinthu zimeme mukuona kuti zinalizomuthandiza Patuma.

• Kodi mumadziwapo mabungwe amene amathandiza atsikanaotenga mimba ngati Patuma amene ali ku dera lanu? Fufuzani zambiri zokhuza mabungwe amenewa kuti muwadziwe.

• Kodi pali ena mwa ma bungwe amenewa amene akuyesetsakumenya nkhondo yakuti pakhale lamulo lololeza kuchotsamimba? Afunseni ena mwa iwo abwere ndipo adzalankhule nanu.

Page 189: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Chipembedzo changa chimaletsamakondomu

Okondedwa Juma

Wachita bwino pokhala ndi maganizo ofuna kudziteteza, komansokuteteza bwenzi lako ku matenda opatsirana pogonana, kutengamimba, komanso ku kachilombo ka HIV.

Zipembedzo zambiri zimalimbikitsa anthu awo kudziletsa osachitazogonana mpaka munthu atalowa m’banja ndipo sizimalora kutianthu ake azigwiritsa ntchito kondomu pogonana. Ngakhale izi zirichoncho, masiku ano anthu ambiri amene amatsatira zipembezoziamadziwa kuti ndi bwino kugwiritsa ntchito kondomu podzitetezaku kachilombo ka HIV. Ena amati kugonana musanalowe m’banjandi tchimo. Koma kugonana opanda kugwiritsa ntchito kondomundi kuika moyo wanu pa chiswe.

Iwe ndi bwenzi lako mukafuna kugonana, muyenera kukambirana zaubwino ndi kuyipa kogwiritsa kapena kusagwiritsa ntchitokondomu. Ubwino ogwiritsa ntchito kondomu pa moyo wako wathupi ndi odziwikiratu, komanso ganizirani kwambiri za ubwinookhuza moyo wanu wa uzimu.

Pafunso lako losavuta lija, makondomu, samakhala ndi ma bowo ayi,ndipo kachilombo ka HIV sikangalowe pa kondomu. Nthawi zinakondomu imatha kuvuka kapena kung’ambika mukugwiritsa ntchito,ichi ndi chifukwa amati kondomu singateteze munthu kotheratu.Koma pokha-pokha mukamagwiritsa ntchito bwino, komansonthawi zonse, makondomu amateteza kumatenda opatsiranapogonana komanso ku kachilombo ka HIV. Njira zodalirikakwambiri kupewa kutenga kachilombo ka HIV ndi kudziletsakotheratu ndi kukhulupilika kwa okondedwa wako moyo wakoonse. Koma kwa amene sangakwanitse zimenezi kugwiritsa ntchitomakondomu ndi kothandiza kwambiri. Ngati munagonanapo opandakugwiritsa ntchito kondomu, ganizirani zokayezetsa magazi anumusanayambe kugonana ndi bwenzi lanu.

Auntie Stella

©TARSC

33

AF33

Page 190: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB33

• Mchaka cha 2004, Bishopu wa mpinga wa a katolika wa ku SouthAfrica-Kelvin Dwling anati:

• Kambiranani pa mutu uwu:

‘Munthu ukhoza Kukhala opemphera koma ndi kukhala ndimaganizo akoako pa zinthu zimene zimakhudza moyo wako ndima ubwenzi’

• Kambiranani ndi anthu kapena mabungwe amene amagwirantchito ndi anthu kapena mabanja amene alindi kachilombo kaHIV ndi matenda a Edzi - kodi maganizo awo ndi otani pa nkhaniya makondomu.

• Kodi ku dera lanu kuli bungwe limene achinyamata a zipembedzozosiyanasiyana amakambirana za mavuto amene amakumananawo mmoyo mwawo? Ngati sichoncho, mungatani kutimukhazikitse bungwe limeneri. Nanga mungagwire bwanji ntchitolimodzi kuti muthandize anthu a m’dera lanu?

Kudziletsa musanalowe m’banja, komanso kukhulupilikapa banja lokhazikika- ndi njira zokhazo zothandizakukhala ndi moyo wa bwino ndi kupewa matendaopatsirana pogonana. Komabe mpingo umayendetsantchito zake mkati mwa zipsyinjo zosiyana siyana zadziko lapansi kotero kuti uyeneranso kulora anthukugwiritsa ntchito njira zosiyana siyana kuti akhale ndimoyo wa bwino. Imodzi mwa iyo ndi kugwiritsa ntchitokondomu, osati polera, koma kupewa imfa zodzera kukachilombo ka HIV ndi matenda a Edzi.

Page 191: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndimafuna kukhala mchikondindi akazi okha okha – kodialipo angandikonde

Okondedwa Alice

Palibe cholakwika munthu kukhala mchikondi ndi mkazi mnzakokapena mamuna mnzako (gay). Anthu amene amati izi ndizolakwika, amachita izi chifukwa cha chikhalidwe ndichimbembedzo chowo. Komatu maganizo otere ndi olakwika.Kumakhala kusamvetsa chabe.

Iwe ungovomereza za mmene iwe uliri basi. Upeze munthu winaamene angakuthandize. Anthu ngati iwe alipo ambiri. Mwinansonawonso amaopa kusekedwa ndi chifukwa chake sanena poyera.Chomwe ungachite ndi kuwafufuza anthu amenewa pofunsaanthu ena, kuwerenga manyuzipepala komanso magazini.

Nthawi zambiri abale a munthu amene amagwa mchikondi ndimkazi kapena mamuna mnzake amakhala omvetsetsa ndiposachita za nkhanza kwa mbale wawoyo. Anthu ambiriamamvesetsa ukakambirana nawo pa okha. Ukafuna kumuuzamunthu uzionetsetsa kuti munthuyo palibe chomusokonezamaganizo. Ndipo udziyamba wayesezera kulankhula za kukhosizakozo usanamuze. Kuchita izi kudzakupatsa mphamvu ndichirimbikitso chachikulu. Alipotu abusa ena omvesetsa kwambirikuposa abusa ako. Abusa amenewa amadziwa kuti ngati Chautaanalenga anthu amene amagwa mchikondi ndi akazi kapenaamuna anzawo ndiye kuti mpingo nawonso uyenerakuwavomereza anthu ngati amenewa. Chifukwa cha ichiusamakhumudwe.

Zabwino zonse pamene ukufunafuna wachikondi wako.

Auntie Stella

©TARSC

34

AF34

Page 192: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB34

• MAYANKHO A MTSUTSO

1 ndi 4 ndi nkhambakamwa chabe, 2 ndi 3 ndi zoona (mfundo)

• Kodi mukugwirizana ndi mmene Auntie Stella ayankhira? Kodi,ndi zinthu ziti zimene mukudziwa chifukwa chakukumana ndianthu amene amagwa mchikondi ndi akazi kapena amuna amunaokha okha? Nanga ndi ziti zimene mukudziwa zimenemunangomva kuchokera kwa anthu ena?

Page 193: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndimamva ululu kwambirindikakhala kuti ndiri kumwezi(ndikusamba)

Okondedwa Agness

Kumva ululu panthawi imene ukusamba si chinthu chachilendoayi. Ndi chilengedwe. Pali zinthu zingapo zimene ungathe kuchitakuti uchepetse vutol monga kusisita mimba yako pansi pamchombo, ndi kufinya pamimba ndi chikhato chako komansokuviika nsalu yolemerela bwino m’madzi otentha, kapenakugwiritsa ntchito botolo la madzi otentha ndi kuliyika pa malopamene pakupwetekapo. Ukhozansokumwa madzi a masamba atiyi wa mbiri, kuchita masewero olimbitsa thupi, kumwa panado,kupemphera kwa Mulungu kuti akuchize ndi kumanga nsalukapena mpango pansi pa mchombo mothinitsa.

Ngati zonsezi sizithandiza, upite kuchipatala kuti akakuthandizemankhwala olerera amene amachepetsa ululu ndi kuchititsa kutiusamataye magazi ambiri panthawi imene ukusamba. Mankhwalaamenewa ndi abwino ndithu ngakhale kwa atsikana achisodzera.

Dziwani kuti atsikana nonse muli ndi ufulu wanu kuti mulandiremaphunziro, kotero kuti ngati mavuto ngati amenewa amachititsakuti pa nthawi ina pa mwezi muzijomba ku sukulu chifukwakulibe zinthu zothandizira panthawi imene mukusamba ndibwinokuti inuyo ndi aphunzitsi mukhale pansi kuti mupeze njirazothetsera vutoli .

Auntie Stella

©TARSC

35

AF35

Page 194: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB35

• ATSIKANA: Yesanipo imodzi mwa njira zimene Auntie Stellaakuwuzani ngati mukumva ululu pamene mukusamba mwezi ndimwezi.

ANYAMATA: Kambiranani ndi alongo anu kapena atsikanaomwe muli nawo m’kalasi mwanu. Mvetsetsani zambiri zokhudzakusamba, ndipo awuzeni nkhawa iliyonse imene mungakhale nayopankhaniyi.

• Ku madera ena ndi kwapafupi kusintha zinthu zimenesizitisangalatsa pamene kumadera ena kumakhala kovuta kutero.Tawerengani zimene zalembedwa m’mipira imene ili pansiyondipo muigawe m’magawo atatu awa;

– Zosavuta kuzisintha.– Zotheka kuzisintha.– Zovuta kwambiri kuzisintha.

Tsopano sankhani malo, atatu kapena zinthu zitatu Kuchokera pam’ndandanda wanu wa; “Zosavuta kuzisintha, Zotheka kuzisintha,Zovuta kwambiri kuzisintha” Kodi ndi chiyani chimenemungakufune kuti chisinthe mu zinthu zimenezi? Kodimungathandizane nawo bwanji anzanu kuti kusintha kumenekukutheke? Yanga’anani dongosolo la ntchito kumapeto kwa khadinamba 29, ndipo muyambe kukonza ndondomeko imeneyi.

Kusukulu

Pagulu lazisudzo Ku

Chipatala

KuBanki

Kutchalitchi

anzako Chibwenzi

Chachikazi/chachimuna

Ndondomekoyoyendetsera

maphuziro ndi zantchito

Page 195: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Achidyamakanda angaamandizunza

Okondedwa Veronika

Pepa kuti bwenzi lako sakukondanso ngati kale. Ndizachisoni kutiizi zimachitika kawirikawiri ndi amuna achikulire komansoolemera. Achidyamakanda amakonda atsikana ang’ono ang’onochifukwa amawamva kukoma akamagonana nawo ndiponsoatsikanawo samadandaula. Nthawi zina achidyamakandawaamaganiza kuti atsikana ang’ono ang’ono amakhala alibekachilombo ka HIV.

Nthawi zambiri zibwenzi za mtundu umenewu zimakhalazopanda tsogolo.ndipo pamene chidya makanda chatopa nayemtsikanayo chimayamba kuphwanya malonjezano akendikuyamba kumuzunza mtsikana uja. Ichi ndi chimenechikukuchitikira iweyo.

Kugonana mosagwiritsa ntchito kondomu ndi koopsya ndipomankhwala a zitsamba sangathe kuchiritsa kachilombo ka HIV.Akanakhala kuti asing’anga amachiza kachilombo ka HIV bwenzipano ali olemera kwambiri. Kumwa mankhwala azitsamba pofunakuchotsa mimba ndi koopsya ndipo nthawi zinanso sizimatheka.

Ndibwino kuti uganize zochisiya chidyamakandacho . Chibwenzichanuchi chiribe tsogolo. Kuli bwino upeze mnyamata wamsinkhu wako amene ungamathe kukambirana naye momasukaza kukhosi kwako ndi zatsogolo lanu.

Ganizira tsogolo lako ndi m’mene ungakwanilitsire maloto ako.Uphunzire luso lina lili-lonse limene lingakuthandize kumapezabendalama zokuthandiza kuti uchite za umodelo ukufunazo.

Auntie Stella

©TARSC

36

AF36

Page 196: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB36

• Onaninso zija munakambirana, zimene munanena kutizimachititsa atsikana kumakonda kupanga zibwenzi ndiachidyamakanda. Pamfundo ina iliyonse pezani njira imenemtsikana angachite kuti asapeze vuto. Mwachitsanzo, ndalama ndizovala za bwino zima…(pitirizani)

• SEWERO: Awiri awiri, kambiranani, yerekezani Veronikaakumuuza chidyamakanda kuti sakufuna kumuonanso koma kodichidyamakanda achite chiyani? Kenaka awuzeni anzanu zimenezimachitika ndiponso awuzeni kuti munamva bwanji pamenemumapanga sewero lija. Kodi mwaphunzirapo chiyani paseweroli.

• Anthu ena amati, achidyamakanda amazunza atsikana ndipoayenera kulandira chilango. Ena amati vuto ndi atsikanawo omwechifukwa cha kususuka kwawo amafuna achidyamakandawo kutiapeze zofuna zawo. Inu mukuganiza bwanji?

• Mukhale awiriawiri kapena pa gulu lanu ndipo muimbe nyimbokusonyeza maganizo anu pa nkhani ya achidyamakanda. Konzaninthawi yakuti nyimbo imeneyi mukaimbe ku gulu lonse.

Page 197: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Chikondi ChimandilepheretsaKuwerenga

Okondedwa Mussa

Chikondi cha munthu wa zaka 17 chimakhala chachikuluchimodzimodzi kwa munthu wa zaka 27. Komatu uyenerakuonetsetsa kuti zochitika zonse m’moyo wako zipitilire bwinobwino, ngakhalenso kwinaku ukumva za chikondi mumtimamwako. Udziwe kuti anthu ambiri anapezaka kuti akagwamchikondi kumene, amasokonezeka pa zochita zawo komanthawi ikamadutsa, amayamba kuganiza ndi kumachita zinthumodekha ndiponso chikondicho chimakhala chozama. Chonchoiwe usadandaule ayi chifukwa zimenezi zitha ndipo uyambansokuwerenga bwino bwino mabuku ako a sukulu.

Komabe kuzindikira kuti pali vuto ndi chiyambi chothana ndivutolo. Ukambirane ndi wokondeka wako ndipo nonse mupezenjira imene ingakuthandizeni kuti mukhale mchikondi mbali inayimukupitiliza maphunziro anu bwinobwino.

Mwinanso mukhoza kupanga nthawi yapadera yoti muthakucheza. Kapena kugwirizana kuti muzionana pokhapokhamukamaliza kuwerenga phunziro lina lake. Njira ina ndiyakutingati nayenso akulemba mayeso, mwina mutha kumawerengerapamodzi, bola maso anu asamakhale pa wina ndi mnzake komapa mabuku basi ndi kuwonesetsa kuti simukugwiranagwirana.Ngati chikondi chanu chili bwino, ngakhaletu kugwira ntchito zinamonga kulima pamodzi zimasangalatsa.

Chilichonse chimene mungasankhe muonesetse kuti mwaikapatsogolo maphunziro anu. Mukadzamaliza ndi ku pambana pamaphunziro anu, mudzatha kukwaniritsa maloto anu ndi zofunazanu mosavuta

Auntie Stella

©TARSC

37

AF37

Page 198: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB37

• Lembani nyimbo kapena ndakatulo ya ubwino kapena kuipakumene chikondi chingabweretse pa moyo wanu. Kodi ambiri ainu munapeza kuti zoipa zinali zambiri kuposa za bwino kapenazinali chimodzimodzi?

• ‘Chikondi chimazunguza dziko lonse lapansi, komasichimabweretsa chakudya pa tebulo. ‘

Pangani miyambi yanu-yanu yokhudzana ndi Chikondi. Kodi ndi itimwa miyambiyi imene mwaikonda kwambiri?

• Khalani awiri awiri ndipo mukonze dongosolo la nthawi yanusabata iliyonse. Onetsani nthawi yogwirira ntchito zanu zonsemonga, Kuwerenga, kuchita masewero, kugwira nthito zapakhomo, ndi nthawi yopuma. Ndipo pamene mwaika nthawiyopuma ndi pamene mungacheze ndi bwenzi lanu. Muonesetsekuti nthawi yanu mwaigawa bwino bwino

• Nthawi zina zimene zimachitika pa moyo wathu (kayazosangalatsa, kaya zoipa) sitimatha kudzimvetsa kuti zikuthekabwanji ndipo zimatizunguza mutu kwambiri. Kodi inuzimakuchitikirani zimenezi? Nanga mumathana nazo bwanji? (zinazimene mungachite pa nthawi ngati zimenezi ndi kupemphera,kupanga masewera, kuthandiza anzanu, kulankhula ndi anzakoomwe umakondana nawo ndi kuwakhulupilira). Auzeni anzanuzimene inu mumachita ndipo nonse lonjezani kuthandizanapamene wina asoweka chithandizo.

Page 199: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Mai anga ali ndi kachilombo kaHIV ndipo samabisa

Okondedwa Paulo

Sindingakupatse yankho la amene angakuuze kuti uli ndikachilombo ka HIV kapena matenda a Edzi. Ndi chinthu chachikulundipo chovuta kuchichita. Munthu aliyense, ayenera kuchitachisankho chake. Anthu ena sauza wina aliyense, ndipo ena amauzaachibale ndi anzawo komanso ena amawuza anthu ambiri pa nthawizosiyanasiyana. Koma chisankho china chilichonse ndi chabwino.

Anthu ambiri amakhala wosangalala akauza anzawo nkhawa zawomonga amayi ako ndi wolimba mtima kunena pagulu. Munthu winaaliyense amene ali ndi kachilombo ka HIV kapena matenda a Edzindi wofunikira kukhala ndi womulangiza kapena gulu lolimbikitsananalo.

Komabe mpaka anthu adzakhale omasuka pa nkhani yokhudzakachilombo ka HIV kuwauza anthu zoti uli ndi kachilombokoyambitsa Edzi, kukhoza kukhala ndi zotsatira zovuta, mongakutha kwa ntchito, kutha kwa ubwenzi ndi anzako ngakhalekuchotsedwa pamalo omwe ukukhala. Anthu amayika pa mlingozinthu zimene sizingakhale za bwino kapena zomwe zingakhalezabwino ku mbali yawo asanawuze wina aliyense zoti ali ndikachilombo koyambitsa matenda a Edzi.

Ngati uli pa ntchito mpofunika udziwe za ufulu wako ngati munthuamene ukugwira ntchito pamene uli ndi kachilombo ka HIV.

Ndikugwirizana nazo kwa thunthu kuti mwana amakhalawosangalala kuti adziwe chilungamo ngakhale chikhale choswetsamtima.

Choncho ndikukuthokoza powathandiza achinyamata pokhalaomasuka. Iwe ndi nkhani ya amayi ako yapatsa chikhulupiriro anthuambiri.

Auntie Stella

©TARSC

38

AF38

Page 200: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB38

• Mukuganiza bwanji za yankho lochokera kwa Auntie Stella?

• Lembani mndandanda zinthu zimene inu ndi anzanu mungachitekuti muthetse m’chitidwe wosala anthu amene ali ndi kachilomboka HIV ndi matenda a Edzi (mwachitsanzo kuchita mtsutso,kuyankhula poyera kwa anthu amene ali ndi kachilombokoyambitsa Edzi, Zovala zolembapo kuti ndili ndi matenda a Edzikapena mzanga amene ali ndi matenda a Edzi ndi mnzangabe.Sankhani zitatu zofunikira kwambiri pa gulu lanu ndipo wonetsanimmene maganizo anu mungawagwiritsire nchito.

• SEWERO:

Muchite sewero pa gulu lanu lowonetsa kuti anthu akumunenamunthu amene ali ndi matenda a Edzi. Anthu ambiriakunyansidwa naye munthu ameneyu koma mmodzi yekhaadzitsutsa mwamphamvu kuti anthu enawo asinthe maganizoawo. Kodi chimene chichitike kumapeto ndi chiani?.

• Itanani anthu ena monga Paulo ndi amayi ake kudzayankhula zamavuto amene anakumana nawo chifukwa cha maganizo a anthuena pa za kachilombo ka HIV ndi matenda a Edzi. Afunsenizimene zinawathandiza kuti athetse kusalidwa kotere.

Page 201: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndingathane nazo bwanjiZiphuphu zanga?

Okondedwa Joana

Zikuwoneka ngati uli ndi ziphuphu zimene zimatuluka kunkhopekwa achinyamata akatha msinkhu kapena akamakhwima.Ziphuphu ndi chimodzi mwa zizindikiro za kuti munthu akukulandipo nthawi zambiri zimatha zokha. Pali zinthu zingapo zimeneungachite kuti vuto lako lithe ndipo zina mwaizo ndi izi:

– Choyamba, zimene umadya ndi zofunika kwambiri. Uzidyazipatso ndi masamba kwambiri komanso ufa wa mgaiwa.Osakonda tizakudya totsekemera ngati maswiti ndimabisiketi, zakudya zamafuta ndiponso zakumwazotsekemera. Zipatso kapena chimanga chophika kapenachootcha ndi zakudya zabwino kusiyana ndi mabanzi.

– Chachiwiri, kumamwa madzi ambiri. Madzi amachapam’thupi.

– Chachitatu ndiponso chofunikira, musamadzole mafutaambiri ku nkhope yanu ndiponso musamazifinyeziphuphuzi. Nthawi zonse mudzigwiritsa ntchito madziofunda ndi sopo posamba kunkhope kwanu.

Achinyamata ena akhoza kukafuna chithandizo cha mankwala kukuchipatala

Usamangoganiza za ziphuphu zakozo ayi koma kumbukiransozinthu zabwino zimene zili pa thupi lako ndiponso usasiyekukacheza ndi anzako. Sikuti anthu amangokhala kuganiza zaziphuphu zathu ayi. Timangowaganizira. Ndikufunira zabwinozonze.

Auntie Stella

©TARSC

39

AF39

Page 202: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB39

• Tchulani zakudya zimene mumadya kawirikawiri. Zigawenimagulu awiri; zakudya zabwino ndi zakudya zosathandiza thupilanu. Taganizirani za nthawi imene mumadya zakudyazosathandizazi ndi chifukwa chimene mumachitira izi.

• Jambulani chithunzi chanu. Onetsani zinthu zabwino pa thupilanulo ndi ntchito zake. Chitsanzo; miyendo yamphamvuyomenyera mpira, maso akuluakulu owonera, makutu abwinoomvera mavuto a wanthu, mano oyera bwino, manjawothandizira banja langa. Onetsani zinthu pafupifupi zisanu.

Pomaliza jambulani nkhope yanu ikusangalala kwambiri.

Page 203: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndine woyembekezera komansondili ndi kachilombo ka HIV

Okondedwa Namoyo

Zikomo Zikomo kwambiri chifukwa cholimba mtima kuyezetsamagazi kuti udziwe ngati uli ndi kachilombo ka HIV kapena ayi.Panopo utha kuchita zinthu zambiri pofuna kudzisamalira,komanso kusamalira mwana ukuyembekezerayo. Ana ambiri ameneamabadwa kwa amayi omwe ali ndi kachilombo ka HIV, amabadwaopanda kachilomboka. Atatu mwa ana khumi aliwonse ndiwoamene amatha kubadwa ndi kachilomboka. Anawa amatengakachilomboka pamene ali m’mimba, kapena pamene akubadwa,ngakhalenso poyamwa. Masiku ano pali njira zambiri zimenezimathandiza kuti mwana asatenge kachilombo ka HIV kuchokerakwa mai.

Zipatala zambiri mdziko muno zimapereka mankhwala aNeverapini mwa ulere kwa amayi oyembekezera omwe ali ndikachilombo ka HIV. Mankhwalawa amateteza kuti mwana asatengekachilombo ka HIV pamene akubadwa, komanso kwa masiku atatuoyambilira atangobadwa. Kafunseni zambiri kuchipatala za njirazotetezera mwana kuti asatenge kachilombo ka HIV kuchokerakwa amake. Komanso mukhoza kudzayamwitsa mwana wanumkaka wa m’botolo. Mukhozanso kukafunsa ku chipatala zammene mungayamwitsire mwana wanu ndi mkaka wa m’mawereokha okha popanda kum’patsa chakudya china chilichonsengakhale madzi akumwa , kwa miyezi 6 kuti asatenge ka chilomboka HIV. Pakatha miyezi 6, mwana ayenera kusiya kuyamwa ndikuyamba kudya ndi kumwa zinthu zina zosiyana siyana.

Komanso muyenera kuteteza mwana wanu pakudzisamalira bwinothupi lanu, ndipo mutha kumva zambiri kuchokera ku chipatala.Achipatala adzakufotokozerani nthawi imene mwana wanuadzayenere kuyezedwa ngati watenga kachilomboka komansomomwe mungamusamalire.

Auntie Stella

©TARSC

40

AF40

Page 204: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB40

• SEWERO: Mzimayi yemwe ali ndi kachilombo ka HIVwaganiza zakuti ayamwitse mwana wake mkaka wa m’mawereokha kwa miyezi 6 , ndipo akuyenera kuwauza apongozi ake kutiasamamupatse mwanayo chakudya kapena chakumwa chinachilichonse. Kodi mukuganiza kuti kunena zimenezi ndikovuta?Nanga chingachitike ndi chiyani kuti vutoli lithe?

• Lembani ubwino ndi kuyipa koyamwitsa pamene mayi ali ndikachilombo ka HIV. Lembaninso chimodzimodzi mokhudzana ndikumpatsa mwana m’kaka wa m’botolo. Kodi mukanatani zimenezizikanakuchitikirani ?

• Kodi mukuganiza bwanji za moyo wa munthu yemwe ali ndi HIVkomanso mwana wake ndi wodwalika? Fufuzani za ntchito zam’dera lanu zimene zimathandiza amayi omwe ali ndi mavutongati amenewa. Kodi ma bungwe amenewa akusowekachithandizo chotani? Nanga inu mungachitepo chiyani?

• Werengani nkhani ya pa khadi nambala 26 kuti mudziwe zambiriza m’mene mungakhalire moyo wabwino ngakhale muli ndikachilombo ka HIV.

Page 205: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Mchimwene wanga anachitamdulidwe

Okondedwa Sunganani

Mchimwene wako akunena zoona ndipo wachita bwinokuchititsa mdulidwe kuchipatala. Kafukufuku amasonyeza kutimdulidwe umthandiza munthu kuti asamatenge matenda opatsirapogonana kuphhatikizapo HIV. Ngati sunadulidwe ndipo wa chitazogonana mosadziteteza, tizilombo ta HIV timakakamila ku songaya chokodzera chako choncho ndi kwapafupi kutenda HIV.

Maiko ambiri muno mu Africa anayamba ntchito yolimbikitsaanthu kuti adzichita mdulidwe ana awo amuna akanali ang’ono.

Iweyonso ngati ungfune, upite kuchipatala kumene anthuophunzitsidwa bwino pa ntchitoyi amapezeka komanso malo ndizochitika zonse zimakhala za ukhondo. Amakupatsansomankhwala ochepetsa ululu.

Ukakachititsa mdulidwe, uyenera kukhala masabata asanu ndilimodzi usanagonane ndi munthu kuti bala lipole msanga.Uyeneranso kukhulupirika kwa chibwenzi chako ndipo pogonanamudzigwiritsa ncthito kondomu. Mdulidwe umathandizakuchepetsa mpata wakuti munthu angatenge HIV komasumakutetezeratu ku HIV. Yankhula nayenso mchimwe wakoyondipo umumvere malangizo amene angakupatse.

Auntie Stella

©TARSC

41

AF41

Page 206: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB41

• Kodi mukuganiza kuti ndi bwino kuti anyamata adzichitamdulidwe? Auzeni anzanu za zimene mukuganiza pa nkhaniyi?

• Chitani mtsutso pa mutu eakuti achinyamata onse adzichitamdulidwe kuti apewe kutenga HIV

• Kodi tsopano mukufuna kuchitapo chiani pa nkhani yolimbikitsaanzanu ndi anthu a mdera lanu kuti adzichita mdulidwe. Dziwaniamai nawonso akhoza kuchitapo kanthu pa nkhaniyi. Lembanizonse zimene mukufuna kuchita ndimene mudzichitire.

• Pitani kuchipatala chimene muli nacho pafupi kuti mukamvemmene amachitira mdulidwe. Musanapite yambani mwalembamafunso anu pa pepala kuti musakaiwale. Mukhozanso kuitanitsawina amene amadziwa bwino za mdulidwe kuti adzakulankhuleniku sukulu kapena kumalo kumene mumakumanirana.

Page 207: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

Ndiri ndi zibwenzi zambiri zoganana nazo

Okondedwa Grace

Nkhani yako ndi yondandaulitsadi. Mchitidwe ogonana ndi amunaambiri ukhoza kukuchititsa kutenga HIV. Komanso mamunaamene ali okullirapo msinkhu ngati Amon akhoza kuti anatengakale kachilombo ka HIV. Ndizotheka kuti Amon ali ndi zibwenzizina za mseri zimene zikhoza kukhalanso ndi HIV.

Kukhala ndi zibwenzi zambiri zogonana nazo ndi koopsakwambiri chifukwa ndi kwapafupi kutenga HIV. Choyenerakudziwa ndi chakuti munthu amene wangokatenga kumenekachilombo ka HIV ndi chapafupi kuti apatsire munthu ameneakugonana naye ngati sakugwiritsa ntchito kondomu. Munthuotereyu amakhala ndi tizilombo tamabiri zedi mthupi mwakemakamaka miyezi itatu yoyambirira chitengereni kachilomboka.

Ngati mwakhala mukugonana osadziteteza ndi bwino kutiukayezetse magazi ako kuti ukadziwe ngati uli ndi HIV. Udziuzezibwenzi zakozo kuti nazonso zikayezetsenso.

Uwetu ukadali wang’ono ndipo utadzisunga bwino ukhozakudzakhala ndi tsogolo la bwino. Kodi unonge tsogolo lako ndi laMichal chifukwa cha zinthu zakutha zimene Amon amakupatsa?

Ndiri ndi chikhulupiriro kuti upanga chisankho chabwino.Zabwino zonse.

Auntie Stella

©TARSC

42

AF42

Page 208: Auntie Stella - TARSC in Chichewa vvlfs... · Auntie Stella Bwalo la achinyamata DONGOSOLO LA OTSOGOLERA ZOKAMBIRANA Training and Research Support Centre,Zimbabwe

ZOYENERA KUCHITA

©TARSCAB42

• Kodi mukuganiza bwanji za yankho la Auntie Stella? Kodimwaphunzirapo kanthu kena katsopano pa zakuopsa kugonanandi anthu ambiri?

Kambiri za nkhani ili mmunsiyi

• Maxwell anali ndi zibwenzi zitatu nthawi imodzi. Brightonamakhala ndi chibwenzi chimodzi pa nthawi koma zibwenzi zakezonse zinakwana zitatu. Chibwenzi chake choyamba chinathamiyezi 8, chachiwiri chinatha miyezi itatu ndipo panopa akanalibendi chibwenzi chachitatu. Kodi pakati pa Maxwell ndi Brightonamene ali pachopsezo chotenga HIV ndi ndani? Perekanichifukwa chake.

• Chitani sewero. Nkhani yake ikhale yakuti mnzake wa Maxwelladzimulangiza za kuopsa kokhala ndi zibwenzi zambiri nthawiimodzi. Maxwell akhuzidwe kwambiri ndipo anene kuti akufunakusiya mchitidwewu. Mnzakeyo amuthandize mmene angasiirekhalidwe loopsali.

• Gulu la achinyamata mdera lanu likufuna kuyamba ntchitoyoteteza achinyamata ku HIV ndi Edzi. Gululi likudziwa kutiachinyamata amachita chisankho chabwino ngati ali ndi uthengaokwanira komanso owona ndipo likufuna anthu kuti awathandizemaganizo pa ntchitoyi.

Khalani mmagulu ndipo mugwirizane ma uthenga a mitundupatatu amene angakhale pa poster. Pa uthenga ulionse jambulaniposter imodzi. Mukatero gwirizanani kuti musankhe maposterabwino kwambiri ndipo muwakhome mmalo osiyanasiyana mdelalanu